Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndimadziwa Mfundo Zimene Ndimayendera?

Kodi Ndimadziwa Mfundo Zimene Ndimayendera?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndimadziwa Mfundo Zimene Ndimayendera?

Michael akuona Brad akubwera poteropo, ndipo akuopa kukumana naye. Atakumana, Brad akunena kuti: “Aise Mikey, tayesako aka.” Michael akuona kuti Brad akumupatsa ndudu ya chamba. Iye sakufuna kusuta, komabe sakufunanso kuti aoneke ngati wotsalira. Michael akumuuza mnzakeyo mokayikira kuti: “Leroli ayi, mwina tsiku lina.”

Jessica akuona Brad akubwera poteropo, ndipo sakuopa kukumana naye. Atakumana, Brad akunena kuti: “Jess, tayesako aka.” Jessica akuona kuti Brad akumupatsa ndudu ya chamba. Iye akuyankha molimba mtima kuti: “Ayi. Sindikufuna kuwononga thanzi langa. Ndili ndi zochita zambiri pa moyo wanga. Ndiponso iwe Brad, . . . zoona munthu wabwinobwino ngati iwe ungamasute?”

PA ANTHU awiriwa, n’chifukwa chiyani Jessica wakwanitsa kukana molimba mtima? Chifukwa chakuti mosiyana ndi Michael, Jessica amadziwa mfundo zimene amayendera. Munthu amene amadziwa mfundo zimene amayendera satengeka ndi zimene anthu ena akuchita. Iye salola kuti anthu ena amukakamize kuchita zinthu zimene zingamuike m’mavuto. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni inuyo kuti muzichita zinthu molimba mtima? Choyamba, mungachite bwino kudzifunsa mafunso otsatirawa:

1 KODI NDIMACHITA BWINO PA ZINTHU ZITI?

Kufunika kodziwa zimenezi: Kudziwa zinthu zimene mumachita bwino komanso zimene mungakwanitse kuchita, kungakuthandizeni kuti mupewe kumachita zinthu mokayikira.

Ganizirani izi: Munthu aliyense ali ndi zinthu zimene amachita bwino. Anthu ena ali ndi luso loimba, ena lochita masewera osiyanasiyana, ndipo ena ali ndi luso lokonza zinthu. Mwachitsanzo, Raquel yemwe ali ndi luso lokonza magalimoto anati: “Nditakwanitsa zaka 15, ndinadziwiratu kuti ndidzakhala wokonza magalimoto.”  *

Chitsanzo cha m’Baibulo: Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndilibe luso la kulankhula, si kuti ndine wosadziwanso zinthu.” (2 Akorinto 11:6) Paulo ankadziwa bwino Malemba, choncho anthu akamamunena ankadziwa chowayankha ndipo sankalola kuti zonena zawozo zimufooketse.—2 Akorinto 10:10; 11:5.

Dzifufuzeni bwino. Lembani pansipa luso lililonse limene muli nalo, kapena chinthu chilichonse chimene mumachita bwino.

․․․․․

Tsopano lembani khalidwe labwino limene muli nalo (Mwachitsanzo, kodi mumaganizira anthu ena, ndinu wopatsa, wodalirika, kapena wodziwa kusunga nthawi?)

․․․․․

“Ndimayesetsa kuchita zinthu zoganizira anthu ena. Mwachitsanzo, ngati munthu akufuna kulankhula nane koma ineyo ndatanganidwa, ndimasiya zimene ndikuchita n’kuyamba kumvetsera.”—Anatero Brianne.

Ngati mukulephera kupeza khalidwe labwino limene muli nalo, yesani kuganizira chinthu chimene munkachita muli mwana koma panopa munasiya. Lembani chinthu chimenecho pansipa.—Onani zitsanzo pa bokosi lakuti  “Zimene Achinyamata Anzanu Amanena.”

․․․․․

2 KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE SINDICHITA BWINO?

Kufunika kodziwa zimenezi: Moyo wanu uli ngati tcheni. Tcheni chimapangidwa ndi mawaya ambirimbiri amene amalumikizidwa pamodzi. Ngati waya mmodzi atakhala wosalimba, tchenicho chikhoza kuduka n’kulephera kugwira bwino ntchito yake. Choncho, ngati inunso mutalola kuti chinthu chinachake chimene simuchita bwino chikufooleni, moyo wanu ukhoza kusokonekera.

Ganizirani izi: Palibe munthu amene anganene kuti sachimwa. (Aroma 3:23) Aliyense amakhala ndi khalidwe linalake limene amafuna atasintha. Mtsikana wina, dzina lake Seija, anadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani ndimakhumudwa ndi zinthu zazing’ono zomwe? Ndimapezeka kuti zinthu zazing’ono zandikhumudwitsa kwambiri.”

Chitsanzo cha M’Baibulo: Paulo ankadziwa zinthu zimene sankachita bwino. Iye analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo.”—Aroma 7:22, 23.

Dzifufuzeni bwino. Kodi ndi zinthu ziti zimene simuchita bwino zimene mumafuna mutasintha?

․․․․․

“Ndaona kuti nthawi zambiri ndikamaliza kuonera filimu yachikondi, ndimakhudzidwa kwambiri ndipo ndimafuna nditakhala ndi chibwenzi. Choncho masiku ano ndimasamala kwambiri ndi mafilimu amene ndimaonera.”—Anatero Bridget.

3 KODI NDIKUFUNA NDIDZACHITE CHIYANI PA MOYO WANGA?

Kufunika kodziwa zimenezi: Munthu akakhala ndi zolinga zinazake zimene akufuna kuzikwaniritsa, amadziwa zoyenera kuchita pa moyo wake. Munthu wotere amapewa anthu komanso zinthu zimene zingamulepheretse kukwaniritsa zolinga zakezo.

Ganizirani izi: Kodi mungachite hayala galimoto ndiyeno n’kumuuza woyendetsa kuti muzingozungulira malo amodzimodzi, mpaka galimotoyo itatha mafuta? Kuchita zimenezi kungakhale kupanda nzeru chifukwa kukhoza kungokudyerani nthawi komanso ndalama. N’zimenenso zimachitika munthu akakhala kuti alibe zolinga. Muyenera kukhala ndi zolinga kuti muzichita zinthu zaphindu zokhazokha. Munthu amene ali ndi zolinga amadziwa kumene akupita.

Chitsanzo cha M’Baibulo: Paulo analemba kuti: “Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikulowera.” (1 Akorinto 9:26) M’malo mochita zinthu mwachisawawa, Paulo anali ndi zolinga pa moyo wake zimene ankayesetsa kuzikwaniritsa.—Afilipi 3:12-14.

Dzifufuzeni bwino. Lembani zinthu zitatu zimene mukufuna kuzikwaniritsa chaka chamawa.

1 ․․․․․

2 ․․․․․

3 ․․․․․

Ndiyeno sankhani chinthu chimodzi chimene mukuchiona kuti n’chofunika kwambiri, ndipo lembani m’munsimu zimene mungayambe kuchita panopa kuti mudzathe kukwaniritsa cholingacho.

“Ndikakhala kuti ndilibe cholinga chilichonse chimene ndikufuna kuchikwaniritsa, ndimangochita zinthu mwachisawawa. Ndikuona kuti ndi bwino kukhala ndi zolinga n’kumayesetsa kuzikwaniritsa.”—Anatero José.

4 KODI NDIMAKHULUPIRIRA MFUNDO ZOTANI?

Kufunika kodziwa zimenezi: Ngati mulibe mfundo zilizonse zimene mumakhulupirira, mumangochita zinthu mwachisawawa. Mofanana ndi bilimankhwe, mumangosinthasintha kuti mugwirizane ndi zimene anzanu akuchita. Munthu amene amasinthasintha popanga zinthu amasonyeza kuti alibe mfundo zimene amayendera pa moyo wake.

Ganizirani izi: Baibulo limalimbikitsa Akhristu ‘kuzindikira chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.’ (Aroma 12:2) Ngati nthawi zonse mumachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zimene mumayendera, simutengeka ndi zimene ena akuchita.

Chitsanzo cha M’Baibulo: Mneneri Danieli ali wachinyamata, “anatsimikiza mumtima mwake” kutsatira malamulo a Mulungu, ngakhale kuti iye anali kutali ndi makolo ake komanso atumiki anzake. (Danieli 1:8) Chifukwa chotsimikiza mumtima mwake kutsatira malamulo a Mulungu, Danieli sanayese ngakhale pang’ono kuchita zosiyana ndi mfundo zimene ankakhulupirira.

Dzifufuzeni bwino. Kodi inuyo muli ndi mfundo zimene mumakhulupirira? Mwachitsanzo:

● Kodi mumakhulupirira kuti kuli Mulungu? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani mumakhulupirira zimenezo? Kodi muli ndi umboni wotani umene umakutsimikizirani kuti Mulungu alipo?

● Kodi mumakhulupirira kuti kutsatira malamulo a Mulungu n’kopindulitsa? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani mumakhulupirira zimenezo? Mwachitsanzo, n’chiyani chimakutsimikizirani kuti kutsatira malamulo a Mulungu okhudza kugonana n’kwabwino kusiyana ndi kutsatira zimene achinyamata ambiri amachita?

Mafunso amenewa ndi ofunika kuwaganizira mwakuya. Yesani kupeza umboni wotsimikizira kuti zimene mumakhulupirira ndi zoona. Ngati mutachita zimenezi, mukhoza kukhala wokonzeka kufotokozera ena momveka bwino zimene mumakhulupirirazo.—Miyambo 14:15; 1 Petulo 3:15.

“Kusukulu kwathu, ana asukulu anzako akaona kuti ulibe mfundo zimene umatsatira, amakupezerera. Choncho ineyo ndinachita khama kupeza umboni womveka bwino wotsimikizira kuti zimene ndimakhulupirira ndi zoona. M’malo mouza anthu kuti, ‘Sindichita nawo zimenezi chifukwa kutchalitchi kwathu amaletsa,’ ndimawauza kuti ‘Ndikuona kuti zimenezi si zabwino.’ Ndimasonyeza kuti zimenezo n’zimene ineyo ndimakhulupirira.”—Anatero Danielle.

Kodi inuyo mungafune kukhala ngati tsamba limene likungouluka ndi mphepo, kapena mungafune kukhala ngati mtengo wolimba umene sungagwe ngakhale kutaomba chimphepo champhamvu? Ngati mukufuna kukhala ngati mtengo wolimba, muyenera kukhala ndi mfundo zimene mumakhulupirira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamangotengera zochita za anzanu.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

  Popeza kuti tsopano ndakula, ndimaunika mfundo zonse bwinobwino posankha zochita, kaya zikhale zazing’ono kapena zazikulu. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipewa kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse Mulungu.

Ndili wamng’ono, ndinkaona kuti aliyense amene ali ndi maganizo osiyana ndi anga ndi woganiza moperewera. Koma masiku ano ndimasangalala kumva maganizo a anthu osiyanasiyana chifukwa ndimadziwa kuti aliyense ndi wosiyana ndi mnzake.

[Zithunzi]

Jeremiah

Jennifer

[Bokosi patsamba 28]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi ndi zinthu ziti zimene mumaona kuti ndimachita bwino? Kodi mukuona kuti ndi makhalidwe ati amene ndingafunike kusintha? Kodi n’chiyani chinakuthandizani inuyo kuti muzikonda kwambiri malamulo a Mulungu?

[Chithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZIMENE NDIMACHITA BWINO

ZIMENE SINDICHITA BWINO

ZOLINGA ZANGA

ZIMENE NDIMAKHULUPIRIRA

[Chithunzi patsamba 28]

Munthu amene amadziwa mfundo zimene amayendera, amakhala ngati mtengo umene wazika mizu womwe sungagwe ngakhale kutaomba chimphepo