Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Makolo Ena Ananena

Zimene Makolo Ena Ananena

 Zimene Makolo Ena Ananena

Pamene ana anu akukula, kodi mungawathandize bwanji kuti akhale omvera? Kodi mungawaphunzitse bwanji ntchito zosiyanasiyana? Tamvani zimene makolo ena padziko lonse anena.

KUWAPHUNZITSA ULEMU KOMANSO KUGWIRA NTCHITO

“Tikamadya chakudya pamodzi komanso tikamakambirana zimene takumana nazo tsikulo, mwana aliyense amaphunzira luso lomvetsera. Akamaona bambo ndi mayi awo akumvetsera mwatcheru, iwonso amatengera zomwezo ndipo amalemekezana komanso amadziona kuti ndi ofunika.”—Anatero Richard, wa ku Britain.

“Timasangalala kwambiri kuona kuti ana athu amalemekezana, amathetsa kusamvana paokha komanso amalankhulana momasuka ndi anthu achikulire.”—Anatero John, wa ku South Africa.

“Monga munthu, nthawi zina ndimalakwitsa zinthu n’kukhumudwitsa ana anga. Zimenezi zikachitika, ndimaona kuti ndi bwino kuwapepesa.”—Anatero Janelle, wa ku Australia.

“Timaphunzitsa ana athu ntchito zosiyanasiyana zapakhomo. Kuwaphunzitsa kuchitira ena zinthu zabwino kumathandiza ana athu kuti azisangalala ndi zimene achita komanso kuti banja lathu liziyenda bwino.”—Anatero Clive, wa ku Australia.

“N’zofunika kwambiri kuphunzitsa ana kuti azimvetsetsana, azilemekezana, komanso azikhululukirana, ngakhale kuti kuchita zimenezi si kophweka.”—Anatero Yuko, wa ku Japan.

KUWAPHUNZITSA UKHONDO KOMANSO MMENE ANGAKHALIRE ATHANZI

“Ana athu ali aang’ono, tinkawaphunzitsa kuti azisamba okha. Kuti azikonda kusamba, tinkawapatsa sopo n’kuwauza kuti apange zinthu zosiyanasiyana ndi thovu la sopoyo, komanso tinkawapatsa mafuta omwe pa botolo pake pankajambulidwa zidole. Ngakhale siponji yosambira imene tinkawapatsa inkakhala yooneka ngati kanyama kenakake.”—Anatero Edgar, wa ku Mexico.

“Pa nthawi imene tinkakhala panyumba yopanda mpopi, ndinkaonetsetsa kuti ndaika beseni la madzi ndi sopo malo enaake kuti tizisamba m’manja tisanalowe m’nyumba.”—Anatero Endurance, wa ku Nigeria.

“Tsiku lililonse timapatsa ana athu chakudya cha magulu onse, ndipo timawafotokozera ubwino wodya chakudya chotere. Ana athu amakhala ndi chidwi chofuna kudziwa zinthu zosiyanasiyana zimene timaika m’zakudya zathu ndipo amandithandiza kuphika. Pa nthawi imene tikuphika chakudyacho, ndi pamenenso timakambirana zinthu zambiri momasuka.”—Anatero Sandra, wa ku Britain.

“Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kofunika kwambiri ndipo timayesetsa kuti tizipereka chitsanzo chabwino kwa ana athu pa nkhani imeneyi. Ana athu amasangalala kwambiri tikamathamanga nawo limodzi, tikamachita nawo masewera osiyanasiyana monga kusambira, kusewera mpira, kapena kukwera njinga. Amadziwa kuti masewera olimbitsa thupi ndi ofunika komanso ndi osangalatsa.”—Anatero Keren, wa ku Australia.

“Ana amasangalala kwambiri akamacheza ndi makolo awo. Zimenezi n’zofunika kwambiri kuposa kuwapatsa ndalama, mphatso inayake kapena kuwalola kupita kwinakwake. Ineyo ndimagwira ntchito m’mawa wokha basi pamene ana anga ali kusukulu n’cholinga choti akaweruka masana, ndizicheza nawo.”—Anatero Romina, wa ku Italy.

KUPEREKA CHILANGO

“Tapeza kuti palibe njira imodzi yoperekera chilango, zimangodalira mmene zinthu zilili. Nthawi zina mwana amangofunika kukambirana naye koma nthawi zina amafunika kumuletsa kuchita zinthu zinazake.”—Anatero Ogbiti, wa ku Nigeria.

“Timauza ana athu kuti abwereze kunena malangizo amene tawapatsa n’cholinga choti tione ngati awamvetsa. Ndiyeno timaonetsetsa kuti malangizowo akutsatiridwa. Timaona kuti tiyenera kupereka chilango kwa ana athu akalephera kutimvera n’cholinga choti asamanyalanyaze malangizo amene timawapatsa.”—Anatero Clive, wa ku Australia.

“Ndikamalangiza ana anga ndimaona kuti ndi bwino kugwada kapena kukhala pansi kuti tizionana maso ndi maso. Zimenezi zimathandiza kuti azimvetsa zimene ndikuwauza komanso zimawathandiza kudziwa mmene ndikumvera.”—Anatero Jennifer, wa ku Australia.

“Timayesetsa kuti tisauze ana athu kuti, ‘Ndiwe wosamva,’ ngakhale atasonyezadi unkhutukumve. Komanso sitikalipira ana athu pamaso pa anzawo. Tikafuna kuwadzudzula, timawatengera pambali kapena timalankhulana nawo motsitsa.”—Anatero Rudi, wa ku Mozambique.

“Ana sachedwa kukopeka, ndipo amakonda kutengera zochita za ena. Choncho, makolo amafunika kuthandiza ana awo kuti asamatengeke ndi zochita za anzawo a kusukulu, zimene amaonera pa TV, kapena zinthu zina zimene anthu ambiri amachita. Timawathandiza kutsatira mfundo zabwino n’cholinga choti akhale ndi khalidwe labwino. Zimenezi zimawathandiza kuti azipewa kuchita zinthu zimene zingawabweretsere mavuto.”—Anatero Grégoire, wa ku DRC.

“Makolo ayenera kupereka chilango choyenera chogwirizana ndi zimene mwanayo walakwa. Ana ayenera kudziwa kuti akalakwitsa, apatsidwa chilango ndipo sipakhalanso zokambirana.”—Anatero Owen, wa ku England.

 [Mawu Otsindika patsamba 14]

“Musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.

 [Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

ZIMENE MABANJA AMAKUMANA NAZO

Kulera Wekha Ana

Zimene Lucinda Forster anatifotokozera

Kodi vuto lalikulu limene mumakumana nalo ndi lotani?

Kukhala kholo ndi udindo waukulu paokha, ndipo kulera wekha ana kumawonjezera udindo umenewu. Vuto lalikulu limene ineyo ndimakumana nalo ndi kugawa nthawi. Ndimafunika kukhala ndi nthawi yokwanira yophunzitsa ana anga makhalidwe abwino komanso kukhala ndi nthawi yopuma ndi yocheza nawo. Nthawi zambiri ntchito zapakhomo zimandichulukira moti sindikhala ndi nthawi yopuma.

Kodi mumatani kuti muzilankhulana momasuka ndi ana anu?

Kunena zoona, banja likatha ana amakhumudwa komanso amadera nkhawa za tsogolo lawo. Ndimaona kuti pakakhala vuto linalake, ndi bwino kulankhula nawo pamasom’pamaso modekha. Tikakhumudwitsana, ndimadikira kuti aliyense mtima wake ukhale pansi, kenako timakambirana bwinobwino ndipo timapewa kukulitsa nkhaniyo. Ndimawapempha kuti afotokoze maganizo awo, ndipo ndimatchera khutu pamene iwo akulankhula, komanso ndimalemekeza maganizo awo. Ndimasonyeza chidwi ndi zimene akuphunzira kusukulu, ndipo ndimawayamikira pa zimene akuchita bwino. Timakonda kudyera limodzi chakudya. Komanso nthawi ndi nthawi ndimawauza kuti ndimawakonda kwambiri.

Kodi mumatani mukafuna kupereka chilango?

Ana amafunika kupatsidwa malamulo omveka bwino ndipo malamulowo sayenera kusinthasintha. Ndimayesetsa kukhala wokoma mtima koma akalakwitsa sindimawanyengerera. Ndimakambirana ndi ana anga zimene alakwitsa n’kuwafotokozera kuipa kwake. Ndisanawapatse chilango, ndimawafunsa mafunso kuti ndidziwe zimene zinawachititsa kuti aphwanye malamulo. Koma ngati ndalakwitsa ndine, mwachitsanzo ngati sindinamvetsetse zimene zinachitika, ndimawapepesa.

Kodi mumawaphunzitsa bwanji ana anu kuti azilemekeza ena?

Ndimawakumbutsa mfundo imene Yesu anaphunzitsa yakuti tizichitira ena zimene tingafune kuti iwo atichitire. (Luka 6:31) Ndimalimbikitsa ana anga kuti azikambirana akalakwirana komanso ndimawaphunzitsa ubwino wochita zinthu modekha komanso moleza mtima makamaka akakhumudwa.

Mumachita chiyani mukafuna kusangalala?

Popeza kuti nthawi zina sitingakwanitse kutenga tchuti n’kupita kwinakwake kutali kokasangalala, timafufuza zinthu zimene tingachite kuti tisangalale popanda kuwononga ndalama. Timatha kutenga chakudya chathu n’kukadyera kumalo enaake aphee kapena kupita kumene amabzala maluwa osiyanasiyana. Komanso tili ndi dimba limene timabzalapo mbewu zosiyanasiyana zokometsera ndiwo ndipo timatha kuthyola mbewuzi n’kukathira mu ndiwo. Timaona kuti kuchita zosangalatsa n’kofunika kwambiri, ngakhale ngati titangopita kukacheza penapake pafupi.

Kodi mwapeza madalitso otani polera ana anu?

Kulera wekha ana n’kovuta. Komabe ine ndi ana anga timayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndipo timayamikira Mulungu chifukwa cha zimene wakhala akutichitira. Ndimasangalala kuona mmene mwana aliyense akukulira. Popeza kuti ana anga adakali aang’ono, amafuna kuti azicheza nane ndipo ndimasangalala kukhala nawo pamodzi. Iwo amatha kudziwa ngati ndadzuka bwino kapena ayi, ndipo nthawi zina akaona kuti sindinadzuke bwino, amandikumbatira n’cholinga chondilimbikitsa. Ndimasangalala kwambiri kudziwa kuti amandikonda. Chofunika kwambiri n’chakuti Mlengi wathu amatikonda kwambiri ndipo wakhala akutithandiza pa mavuto athu. Baibulo landithandiza kuti ndiziyesetsa kukhala kholo labwino kwambiri.—Yesaya 41:13.

[Chithunzi]

Lucinda ndi ana ake awiri, Brie ndi Shae