Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Makolo Ena Ananena

Zimene Makolo Ena Ananena

 Zimene Makolo Ena Ananena

Ngati muli ndi mwana wamng’ono, muyenera kuti mukudziwa mmene mwana amavutira. Ndiye kodi mumafunika kuchita chiyani akayamba kuvuta? Kodi mungamuphunzitse bwanji kusiyanitsa chabwino ndi choipa? Kodi muyenera kutani kuti muzimupatsa chilango choyenerera akalakwitsa? Tamvani zimene makolo ena ananena pa nkhani zimenezi.

AKAYAMBA KUVUTA

“Mwana akafika zaka ziwiri amavuta kwambiri. Iye amafuna kupatsidwa chilichonse chimene akufuna. Mwana wathu wamwamuna ankavuta kwambiri. Tikapanda kumupatsa zimene akufuna, ankaponyaponya zinthu. Popeza anali woyamba, sitinkadziwa kuti titani kuti asiye kuvuta. Anthu ena ankatiuza kuti tingozolowera zochita zake chifukwa n’zimene ana ambiri amachita, koma malangizo amenewa sankatithandiza kwenikweni.”—Anatero Susan, wa ku Kenya.

“Mwana wathu wamkazi atakwanitsa zaka ziwiri ankavuta kwambiri. Iye ankagubuduka pansi, kwinaku akulira mokuwa komanso akumenyetsa miyendo yake . . . Zochita zake zinkatikhumudwitsa kwambiri. Akayamba zimenezi, kulankhula naye sikunkathandiza. Choncho ine ndi mwamuna wanga tinkamutsekera kuchipinda kwake n’kumuuza modekha kuti mtima wake ukakhala pansi, tikambirana naye. Akatonthola, mmodzi wa ife ankapita kuchipinda kwakeko kukamuthandiza kuona kuti zimene anachitazo n’zosayenera. Zimenezi zinkathandiza kwambiri moti tsiku lina tinamumva akupemphera kwa Mulungu kuti amukhululukire chifukwa cha zimene wachita. Pang’ono ndi pang’ono anayamba kusiya kuvuta ndipo kenako anasiyiratu.”—Anatero Yolanda, wa ku Spain.

“Nthawi zina ana amavuta n’cholinga chofuna kukuyesani. Amafuna aone kuti mungawalekerere mpaka kufika pati. Choncho si bwino kuwaloleza zinthu zimene munawakaniza poyamba, chifukwa kuchita zimenezi kungawasokoneze. Tinaona kuti kuchita zinthu mosasinthasintha, kunathandiza kuti pang’ono ndi pang’ono ana athu ayambe kuzindikira kuti kulira si njira yabwino yopezera zimene akufuna.”—Anatero Neil, wa ku Britain.

KUPEREKA CHILANGO

“Mwana akakhala kuti sanakwanitse zaka zisanu, zimakhala zovuta kudziwa ngati akumva zimene makolo ake akumuuza. Koma chofunika kwambiri n’kumuuza zinthu mobwerezabwereza. Muyenera kubwereza zomwezomwezo kambirimbiri, ndipo muyenera kumuuza mwamphamvu komanso ndi manja omwe.”—Anatero Serge, wa ku France.

“Ngakhale kuti ana athu anayi tinawalera mofanana, aliyense anali wosiyana ndi mnzake. Mwana wathu wina ankati akalakwitsa chinachake, amangoyamba kulira, pomwe mwana wathu wina akalakwitsa, sizinkamukhudza ndipo ankapitirizabe kuvuta kuti awone kuti timulekerera mpaka pati. Nthawi zina mwana angafunikire kupatsidwa chilango pamene nthawi zina kungomuyang’ana kokha n’kokwanira kuti adziwe kuti walakwitsa chinachake.”—Anatero Nathan, wa ku Canada.

“Si bwino kumulola mwana kuti azingochita zimene akufuna chifukwa chotopa ndi zochita zake. Komabe, muyenera kupewa kukhwimitsa kwambiri zinthu kapena kukakamira mfundo zosathandiza kwenikweni. Ifeyo tikaona kuti mwana wathu wazindikira kulakwa kwake, timamuchepetsera chilango.”—Anatero Matthieu, wa ku France.

“Ndimaonetsetsa kuti ndisapatse ana anga malamulo ambirimbiri, komabe sindilola kuti malamulo ochepa amene alipowo aphwanyidwe. Mwana wanga wazaka zitatu amadziwa kuti akapanda kumvera lamulo linalake alandira chilango, ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti asamachite zinthu motayirira. Nthawi zina ndikatopa, ndimaganiza zonyalanyaza zoipa zimene wachita. Komabe ndimadziumiriza kuti ndim’patse chilango, n’cholinga choti adziwe kuti malamulo amene timamupatsa sasintha. Kukhala ndi malamulo osasinthasintha n’kofunika kwambiri.”—Anatero Natalie, wa ku Canada.

MUSAMASINTHESINTHE

“Ana amakumbukira kwambiri zinthu, ndipo makolo akamasinthasintha malamulo, iwo amaona.”—Anatero Milton, wa ku Bolivia.

“Nthawi zina mwana wathu ankatifunsa zinthu zomwezomwezo koma m’njira zosiyanasiyana, n’cholinga choti aone ngati timupatse yankho lofanana. Nthawi zinanso ankafuna kuona ngati zimene ndamuuza n’zofanana ndi zimene mayi ake anamuuza. Zikasiyana, ankaona kuti adutsire kwa ndani, n’cholinga choti zolinga zake zitheke basi.”—Anatero Ángel, wa ku Spain.

“Nthawi zina ndikakhala kuti ndadzuka bwino ndinkanyalanyaza zimene mwana wanga walakwitsa, koma ndikakhala kuti sindinadzuke bwino ndinkamupatsa chilango chokhwima. Kenako ndinaona kuti zimenezi zinkangomuchititsa kuti apitirize kuvuta.”—Anatero Gyeong-ok, wa ku Korea.

“Ana ayenera kudziwa kuti zimene makolo awo akuwauza kuti n’zoipa zidzakhalabe zoipa mpaka kalekale.”—Anatero Antonio, wa ku Brazil.

“Makolo akamasinthasintha malamulo, mwana wawo amaona kuti bambo ndi mayi ake ndi osadalirika ndiponso kuti malamulo awo amasintha mogwirizana ndi mmene akumvera pa nthawiyo. Koma makolo akamapanda kusinthasintha mfundo zawo, mwana amadziwa kuti zimene makolo ake akumuuza kuti n’zolakwika, sizidzasintha n’kukhala zabwino. Choncho, mwana amadziwa kuti makolo ake amamupatsa malamulo chifukwa chakuti amamukonda.”—Anatero Gilmar, wa ku Brazil.

“Ana ndi ochenjera. Amatha kupempha makolo awo zinthu zinazake pa nthawi imene makolowo sangathe kukana, monga pamene ali ndi alendo. Ineyo ndikamukaniza mwana wanga zinazake, ndimamuuziratu kuti ngakhale atandichonderera bwanji sindingasinthe maganizo anga.”—Anatero Chang-seok, wa ku Korea.

“Makolo onse awiri ayenera kugwirizana chimodzi. Ine ndi mkazi wanga tikalephera kumanga mfundo imodzi, timakambirana kaye pa awiri. Ngati makolo sakugwirizana chimodzi, ana amaona zimenezo ndipo amapezerapo mwayi wochita zofuna zawo.”—Anatero Jesús, wa ku Spain.

“Mwana akaona kuti makolo ake akugwirizana chimodzi ndiponso kuti sangasinthe mfundo zawo, iye amawadalira. Amadziwa kuti akamawamvera, zinthu zimuyendera bwino ndipo akapanda kuwamvera alandira chilango.”—Anatero Damaris, wa ku Germany.

“Ine ndi mkazi wanga timaonetsetsa kuti zinthu zabwino zimene tinamulonjeza mwana wathu tazikwaniritsa. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti azitidalira.”—Anatero Hendrick, wa ku Germany.

“Ngati bwana wanga atamangokhalira kundisinthira malamulo ogwirira ntchito, sindingasangalale. Ananso n’chimodzimodzi. Ayenera kudziwa kuti pali malamulo oti azitsatira omwe sasinthasintha. Afunikanso kudziwa chilango chimene angalandire ngati atalakwitsa zinazake komanso kuti chilangocho sichingasinthe.”—Anatero Glenn, wa ku Canada.

 [Mawu Otsindika patsamba 8]

“Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Yakobo 5:12.

 [Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

ZIMENE MABANJA AMAKUMANA NAZO

Mimba Yosakonzekera—Mmene Zinatikhudzira

Yosimbidwa ndi Tom ndi Yoonhee Han

Tom: Titangotha miyezi 6 m’banja, mkazi wanga anazindikira kuti ndi wodwala. Pamaso ndinkaoneka ngati ndilibe nkhawa chifukwa ndinkafuna kuti ndizimulimbitsa mtima mkazi wanga, Yoonhee. Koma mumtima ndinali ndi nkhawa yaikulu.

Yoonhee: Ndinkada nkhawa kwambiri komanso ndinkachita mantha. Ndinkangokhalira kulira chifukwa ndinkaona kuti ndinali ndisanakonzekere kukhala ndi mwana.

Tom: Inenso ndinkaona kuti sindinali wokonzeka kukhala bambo. Koma titacheza ndi makolo ena, tinazindikira kuti kukhala ndi mimba yosakonzekera n’kofala m’mabanja ambiri. Komanso zimenezi zinatithandiza kudziwa chisangalalo chimene makolo ena amakhala nacho mwana akabadwa. Pang’ono ndi pang’ono ndinaleka kuda nkhawa ndipo ndinkayembekezera mwachidwi kubadwa kwa mwana wathu.

Yoonhee: Mwana wathu, Amanda, atabadwa tinayamba kukumana ndi mavuto atsopano. Iye ankangokhalira kulira ndipo kwa milungu ingapo sindinkagona. Sindinkafuna kudya, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti ndizingokhala wofooka nthawi zonse. Poyamba sindinkafuna ngakhale kucheza ndi anthu. Koma kenako ndinazindikira kuti kudzipatula sikungandithandize. Ndinayamba kucheza ndi amayi ambiri amene anali ndi ana aang’ono. Zimenezi zinandithandiza kudziwa mavuto amene anzangawo ankakumana nawo komanso kudziwa nkhawa zawo.

Tom: Ndinkayesetsa kuti tisasiye kuchita zinthu zofunika zimene timachita nthawi zonse. Mwachitsanzo, popeza kuti ndife a Mboni za Yehova, tinkaonetsetsa kuti tisamalephere kupita kolalikira komanso kumisonkhano ya mpingo. Ndiponso kukhala ndi mwana kumachititsa kuti muziwononga ndalama zambiri chifukwa cha zinthu zina zosayembekezereka, choncho tinkayesetsa kuti tisamakhale ndi ngongole, zimene zikanatiwonjezera nkhawa.

Yoonhee: Poyamba ndinkaganiza kuti sindingakwanitse kupita kolalikira chifukwa chakuti mwanayo azikandivutitsa. Koma ndinazindikira kuti anthu amakonda ana. Choncho sindinasiye kupita kolalikira komanso ndinkamunyadira mwana wangayo.

Tom: Baibulo limanena kuti ana ndi “cholowa chochokera kwa Yehova” komanso ndi “mphoto.” (Salimo 127:3) Mawu amenewa amandithandiza kuona kuti mwana ndi mphatso yamtengo wapatali. Munthu akapatsidwa cholowa, amafunika kuchisamala kuti chidzamuthandize m’tsogolo. Koma n’zothekanso kuchigwiritsa ntchito mosasamala. N’chimodzimodzinso ndi ana. Panopa ndazindikira kuti mwana akamakula amakumana ndi zinthu zosiyanasiyana. Choncho, ndimayesetsa kuchita chidwi ndi zimene zikumuchitikira pa nthawi iliyonse ya moyo wake chifukwa ndimadziwa kuti nthawi imeneyi ikadutsa, yadutsa basi.

Yoonhee: Moyo uli ndi zinthu zambiri zochititsa chidwi. Nthawi zina munthu umakumana ndi zinthu zosayembekezereka, monga kukhala ndi mimba yosakonzekera. Panopa, mwana wathu Amanda ali ndi zaka 6 ndipo ndimamukonda kwambiri.

[Chithunzi]

Tom ndi mkazi wake Yoonhee komanso mwana wawo Amanda