Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa

Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa

Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa

YESU KRISTU anawakomera mtima kambiri anthu amene anali ovutika. Mwachitsanzo, anadyetsa anthu anjala ndipo anachiritsa odwala. (Mateyu 14:14-21) Komabe ndi ntchito iti imene iye anaiika pamwamba pa zonse? Zimene zinachitika nthaŵi imene Yesu ankayamba utumiki wake zitipatsa yankho? Zinalembedwa m’chaputala choyamba cha Uthenga Wabwino wa Marko.

Yesu ali ku Kapernao, pafupi ndi Nyanja ya Galileya, anatengedwa kupita kunyumba ya Simoni, kapena Petro. Kumeneko “mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo” ndipo Yesu anam’chiritsa. (Marko 1:29-31) Kenaka anthu ambiri kuphatikizapo ‘odwala nthenda za mitundumitundu’ anayamba kusonkhana pakhomo lanyumba ya Petro ndipo Yesu anawachiritsanso. (Marko 1:32-34) Kenaka kunada ndipo aliyense anakagona.

M’maŵa mwake “usikusiku,” Yesu anadzuka mwakachetechete n’kuchoka panyumbapo “namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.” Mosakhalitsa, nawonso ophunzira anadzuka n’kuona panja panyumbayo pali namtindi wa anthu akudikirira pakhomo. Koma kodi akanatani? Yesu anali asakudziŵika kumene ali! Mwamsangamsanga Petro ndi anzake anayamba kufunafuna Yesuyo ndipo atam’peza anamuuza kuti: ‘Akukufunani inu anthu onse.’ (Marko 1:35-37; Luka 4:42) Zikukhala ngati kuti iwo ankamuuza Yesu kuti: ‘Kodi mukudzatani kuno? Dzulo usiku zinayenda bwino kwambiri pamene munachiritsa odwala. Lero mukhalanso ndi mpata wina waukulu wochiritsa anthu!’

Koma taonani mmene Yesu anawayankhira: ‘Tiyeni kwina, ku midzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso.’ Yankho limeneli lili ndi mfundo yofunika. Yesu sanabwererenso kunyumba ya Petro kukachiritsa anthu ena. Iye anasonyeza chifukwa chake ponena kuti: ‘Pakuti ndadzera ntchito imeneyi [yolalikira].’ (Marko 1:38, 39; Luka 4:43) Kodi ponena mawu ameneŵa Yesu anali kuwauza chiyani ophunzira ake? Kukomera anthu mtima kunali kofunika kwa iye, koma chinthu choyambirira chimene Yesu anafunikira kuchita chinali kulalikira ndi kuphunzitsa Mawu a Mulungu.—Marko 1:14.

Popeza kuti Baibulo limalimbikitsa Akristu ‘kulondola mapazi a [Yesu],’ndiye kuti Akristu oona masiku ano ali ndi chitsanzo akamafuna kusankha ntchito yongodzipereka yoyenera kuichita poyamba. (1 Petro 2:21) Mofanana ndi Yesu, iwo amathandiza anthu amene akuvutika, monga mmene nkhani imene tangomaliza kuŵerenga ikunenera. Komanso monga Yesu, ntchito imene amaiika pamwamba pa zonse ndi yophunzitsa nkhani ya m’Baibulo yokhudza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. * (Mateyu 5:14-16; 24:14; 28:19, 20) Koma n’chifukwa chiyani kudzipereka kuphunzitsa anthu za uthenga wa m’Baibulo kuyenera kukhala pamwamba pa mitundu ina yonse yofunika yantchito yongodzipereka?

Chifukwa Chake Kuphunzira Baibulo Kumathandiza Ndiponso Mmene Kumathandizira

Mwambi wina wa amwenye umanena bwino za nkhaniyi. Mwambiwo umati: “Ngati mukuganizira za chaka chimodzi m’tsogolo, dzalani mbewu. Ngati mukuganizira za zaka khumi, dzalani mitengo. Ngati mukuganizira za zaka 100, phunzitsani anthu.” Zoonadi, pankhani ya zinthu zothandiza kwa nthaŵi yaitali, maphunziro ndiwo ali patsogolo pa zonse chifukwa amam’thandiza munthu kuganizira bwino zinthu zomwe zingam’thandize m’moyo mwake. Ndiye n’chifukwa chake panopo anthu ongodzipereka oposa 6 miliyoni ogwira ntchito kwa nthaŵi yochepa ndiponso ena nthaŵi zonse akugwiritsa ntchito nthaŵi yawo, mphamvu zawo ndi zinthu zimene ali nazo pophunzitsa anthu Baibulo. Ntchito yongodzipereka imeneyi yomwe yakhala ikuchitidwa ndi Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali, ikuthandiza kwambiri anthu padziko lonse. Ikuthandiza motani?

Anthu akamathandizidwa kumvetsa ndi kutsatira uphungu wothandiza wa m’Baibulo, amakhala okonzeka kuthana ndi mavuto awo. Amakhala ofunitsitsa kusonyeza khalidwe labwino pothetsa makhalidwe oipa. Mnyamata wina wa ku Brazil dzina lake Nelson, akufotokoza phindu lina la kuphunzira Baibulo ponena kuti: “Chiyambireni kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndapeza chimwemwe chifukwa tsopano ndili ndi cholinga m’moyo.” (Mlaliki 12:13) Achikulire ndi achinyamata ambiri amene ayamba posachedwapa kuphunzira Mawu a Mulungu nawonso amasangalala ngati Nelson. Kuwonjezera pa kuthandiza ophunzira kuti apeze cholinga chokhutiritsa m’moyo, uthenga wa Ufumu wa Mulungu umapereka chiyembekezo cholimbikitsa cha m’tsogolo. Chiyembekezochi chimachititsa moyo kukhala wokoma, ngakhale poyesedwa kwambiri. (1 Timoteo 4:8)—Onani m’kabokosi kakuti “Mmene Ufumu wa Mulungu Udzasinthire Zinthu.”

Pophunzitsa anthu Baibulo, Mboni za Yehova zimachita ntchito yongodzipereka yokhala ndi mapindu okhalitsa. Kodi n’njokhalitsa mpaka liti? Mawu a Mulungu amati: ‘Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.’ (Yohane 17:3) Tangoganizirani mutamachita nawo ntchito yokhala ndi mapindu osatha. Komatu ntchito imeneyo ndi ntchito yongodzipereka yothandizadi ena! Kodi imeneyi si ndiyo ntchito imene mungakonde kuiphunzira? Ngati zili choncho, dziŵitsani Mboni za Yehova m’dera lanulo. Simudzanong’oneza bondo ayi mukatsatira zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mboni za Yehova zimaona ntchito yawo yolalikira monga mmene mtumwi Paulo ankaionera, monga chinthu chofunikira kwa Akristu oona. Paulo anati: “Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho [“pakuti ndimafunikira kutero,” NW].” (1 Akorinto 9:16) Komabe ntchito yawo yolalikira ndi yongodzipereka chifukwa anasankha okha kukhala ophunzira a Kristu, ndipo amakhala akudziŵa bwinobwino ntchito imene ayenera kuchita akapeza mwayi umenewu.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

“Ngati mukuganizira za chaka chimodzi m’tsogolo, dzalani mbewu. Ngati mukuganizira za zaka khumi, dzalani mitengo. Ngati mukuganizira za zaka 100, phunzitsani anthu”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 20]

Amathandiza Ndiponso Amapereka Chiyembekezo

Namwino wina wa zaka 43 wa ku France dzina lake Nadine yemwe amadziŵa kuchiza matenda ambiri a mu Africa, ali m’gulu la anthu ongodzipereka amene anagwirako ntchito m’chigawo chapakati cha Africa. “Anthu amandifunsa kuti ndimachitiranji zimenezi,” iye anatero atam’funsa posachedwapa. “Ndimakhulupirira Mulungu, ndimakonda anthu ndipo ndimafuna kudzipereka kuti ndithandize anthu. Ndipo pokhala m’gulu la Mboni za Yehova ndimalimbikitsidwa kuthandiza ndi kupereka chiyembekezo kwa anthu amene akuvutika.” Pa ntchito yake yongodziperekayi mu Africa, Nadine amagaŵa nthaŵi yake pogwira ntchito yopereka chithandizo kwa anthu amene akuvutika ndiponso pochita nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene Mboni za kumeneko zikuchita.

[Zithunzi]

Nadine ali kuno ku Africa

[Bokosi patsamba 22]

Mmene Ufumu wa Mulungu Udzasinthire Zinthu

Taŵerengani malemba aŵa m’Baibulo lanu muone mmene Mulungu akulonjezera kukwaniritsa zofuna za anthu pankhani zotsatirazi:

Thanzi “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”Chivumbulutso 21:4; Yesaya 33:24; 35:5, 6.

Maphunziro “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”Yesaya 11:9; Habakuku 2:14.

Ntchito “Adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; . . . Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”Yesaya 65:21-23.

Chakudya “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”Salmo 67:6; 72:16; Yesaya 25:6.

Kakhalidwe ka Anthu “Yehova wathyola mkunkhu wa woipa . . . Dziko lonse lapuma, lili du.”Yesaya 14:5, 7.

Chilungamo “Tawonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.”Yesaya 11:3-5; 32:1,2.