Aheberi 13:1-25
13 Mupitirize kukonda abale.+
2 Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+
3 Kumbukirani amene ali m’ndende+ ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.+ Kumbukiraninso amene akuzunzidwa,+ popeza inunso mudakali m’thupi lanyama.
4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+
5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+
6 Moti tikhale olimba mtima ndithu+ ndipo tinene kuti: “Yehova* ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+
7 Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.+ Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani+ chikhulupiriro chawo.+
8 Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo ndi lero, ndiponso mpaka muyaya.+
9 Musatengeke ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo.+ Ndi bwino kuti mtima ukhale wolimba chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu,+ osati chifukwa cha zakudya.+ Pakuti amene amatanganidwa ndi zakudyazo sakupindula nazo.
10 Ife tili ndi guwa lansembe limene ochita utumiki wopatulika kuchihema, alibe ulamuliro wodya za paguwapo.+
11 Pakuti nyama zimene magazi ake, mkulu wa ansembe amalowa nawo m’malo oyera chifukwa cha machimo, amakazitentha kunja kwa msasa.+
12 Zinalinso chimodzimodzi ndi Yesu. Kuti ayeretse+ anthu ndi magazi ake,+ anakavutikira kunja kwa chipata.+
13 Chotero, tiyeni timutsatire kunja kwa msasako, titasenza chitonzo chimene iye anasenza.+
14 Pakuti pamene tili pano, tilibe mzinda wokhazikika,+ koma ndi mtima wonse tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.+
15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+
16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+
17 Muzimvera amene akutsogolera pakati panu+ ndipo muziwagonjera.+ Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu.+ Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.+
18 Pitirizani kutipempherera,+ pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.+
19 Koma makamaka ndikukulimbikitsani kuchita zimenezi, kuti ndibwerere kwa inu mwamsanga.+
20 Tsopano, Mulungu wamtendere,+ amene anaukitsa kwa akufa+ m’busa wamkulu+ wa nkhosa+ wokhala ndi magazi a pangano losatha,+ Ambuye wathu Yesu,
21 akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, achite mwa ife zimene zili zokondweretsa pamaso pake.+ Kwa iye kukhale ulemerero kwamuyaya.+ Ame.
22 Tsopano, ndikukudandaulirani abale, chonde khalani oleza mtima pamene mukuwerenga mawu olimbikitsawa, chifukwa ndakulemberani kalatayi m’mawu ochepa.+
23 Dziwani kuti m’bale wathu Timoteyo+ wamasulidwa, ndipo ngati angabwere posachedwapa, ndibwera naye limodzi kudzakuonani.
24 Mundiperekere moni kwa onse amene akutsogolera pakati panu,+ ndiponso kwa oyera ena onse. A ku Italiya+ akukupatsani moni.
25 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu+ kukhale nanu nonsenu.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 2.

