Aheberi 12:1-29

12  Choncho, chifukwa chakuti tili ndi mtambo wa mboni+ waukulu chonchi wotizungulira, tiyeninso tivule cholemera chilichonse+ ndi tchimo limene limatikola mosavuta lija.+ Ndipo tithamange mopirira+ mpikisano+ umene atiikirawu.+  Tichite zimenezi pamene tikuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu+ ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu,+ Yesu. Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake,+ anapirira mtengo wozunzikirapo.* Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.+  Ndithudi, ganizirani mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza+ ngati amenewo a anthu ochimwa, amene mwa kulankhula koteroko anali kungodzivulaza okha. Ganizirani za munthu ameneyu kuti musatope ndiponso kuti musalefuke.+  Popitiriza mpikisano wanu wolimbana ndi tchimo limenelo, simunafikebe polimbana nalo mpaka kutaya magazi anu.+  Ndipo mwaiwaliratu langizo lokudandaulirani limene limakutchani ana,+ lakuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova, kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula.+  Pakuti Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamulandira monga mwana wake.”+  Kupirira kumene mukupiriraku,+ mukupirira kuti chikhale chilango chanu. Mulungu akuchita nanu zinthu ngati ana ake.+ Ndi mwana wanji amene bambo ake samulanga?+  Koma ngati simunalandire chilango chimene ena onse alandira, ndiye kuti ndinu ana apathengo,+ osati ana ake enieni.  Ndiponso, bambo athu otibereka, amene anali ndi thupi lanyama ngati lathuli anali kutilanga,+ ndipo tinali kuwalemekeza. Kuli bwanji ndi Atate wa moyo wathu wauzimu. Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+ 10  Pakuti bambo athu otiberekawo, kwa masiku ochepa anali kutilanga malinga ndi zimene anaziona kuti n’zoyenera,+ koma Mulungu amatilanga kuti tipindule ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+ 11  Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+ 12  Choncho limbitsani manja amene ali lende+ ndi mawondo olobodoka,+ 13  ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo,+ kuti chiwalo chimene chavulala chisaguluke polumikizira, koma chichiritsidwe.+ 14  Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse,+ komanso yesetsani kukhala oyera+ chifukwa ngati munthu si woyera, sadzaona Ambuye.+ 15  Pochita zimenezo, muonetsetse kuti wina asalandidwe kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ komanso kuti pakati panu pasatuluke muzu wapoizoni+ woyambitsa mavuto, ndi kuti ambiri asaipitsidwe nawo.+ 16  Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika, ngati Esau,+ amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.+ 17  Mukudziwa kuti pambuyo pake, atafunanso kulandira dalitso monga cholowa chake,+ anamukanira.+ Pakuti ngakhale kuti anayesetsa ndi mtima wonse, kwinaku akugwetsa misozi,+ kuti bambo ake asinthe maganizo, sizinatheke.+ 18  Pakuti simunafike paphiri limene mungathe kulikhudza,+ loyaka moto,+ lokhala ndi mtambo wakuda, mdima wandiweyani komanso lowombedwa ndi mphepo yamkuntho.+ 19  Simunafike paphiri limene panamveka kulira kwa lipenga+ ndi mawu a winawake akulankhula,+ amene anthu atawamva, anachonderera kuti asawauzenso mawu ena.+ 20  Pakuti lamulo lija linawakulira, lakuti: “Nyama iliyonse imene ingakhudze phirilo, iponyedwe miyala.”+ 21  Komanso, zimene anaona kumeneko zinali zoopsa kwambiri moti Mose anati: “Ndikuchita mantha ndipo ndikunjenjemera.”+ 22  Koma m’malomwake, inu mwafika kuphiri la Ziyoni+ ndi mzinda+ wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba,+ kumene kuli angelo miyandamiyanda,*+ 23  pamsonkhano wawo waukulu.+ Kumenenso kuli mpingo wa woyamba kubadwayo,+ mpingo wa iwo amene analembedwa+ kumwamba. Kumeneko kulinso Mulungu, Woweruza wa onse,+ ndiponso kuli moyo wauzimu wa olungama+ amene akhala angwiro.+ 24  Kulinso Yesu, mkhalapakati+ wa pangano latsopano,+ ndiponso magazi owaza,+ amene amalankhula m’njira yabwino kwambiri kuposa magazi a Abele.+ 25  Samalani kuti musasiye kumvetsera wolankhulayo.+ Pakuti ngati amene analephera kumvera wopereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke,+ kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikachoka kwa iye amene amalankhula ali kumwamba.+ 26  Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.”+ 27  Tsopano, mawu akuti “Ndidzagwedezanso,” akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzachotsedwa. Zimenezi ndi zinthu zimene zinapangidwa ndi winawake,+ ndipo adzazichotsa kuti zimene sizikugwedezeka zitsale.+ 28  Ndiye chifukwa chake, poona kuti tidzalandira ufumu umene sungagwedezeke,+ tiyeni tipitirize kulandira kukoma mtima kwakukulu, kuti kudzera m’kukoma mtima kwakukulu kumeneko, tichitire Mulungu utumiki wopatulika m’njira yovomerezeka, ndipo tiuchite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.+ 29  Pakuti Mulungu wathu alinso moto wowononga.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 9.
Onani Mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Kapena kuti, “masauzande makumimakumi.”