Aheberi 5:1-14
5 Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa mwa anthu amaikidwa kuti achite utumiki wa Mulungu m’malo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+
2 Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu ndi olakwa, chifukwa iyenso ndi wofooka.+
3 Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, monga mmene amaperekera nsembe za machimo a anthu onse.+
4 Komanso, munthu amalandira ulemu umenewu, osati mwa kufuna kwake,+ koma mwa kuchita kuitanidwa ndi Mulungu,+ monga mmene anaitanira Aroni.+
5 Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ mwa kudziika yekha kukhala mkulu wa ansembe.+ Koma amene anamupatsa+ ulemerero umenewo ndi amene analankhula zokhudza iyeyu kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala atate wako.”+
6 Monga mmene akuneneranso penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+
7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+
8 Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.+
9 Ndipo atakhala wangwiro,+ anakhala ndi udindo wopereka chipulumutso chamuyaya+ kwa onse omumvera,+
10 chifukwa watchulidwa mwachindunji ndi Mulungu kuti ndi mkulu wa ansembe monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+
11 Tili ndi zambiri zoti tinene zokhudza iyeyu koma zovuta kuzifotokoza chifukwa chakuti inu mumachedwa kumvetsa zinthu.+
12 N’zoona kuti munayenera kukhala aphunzitsi+ pofika nthawi ino. Koma sizili choncho, ndipo mukufunikanso wina woti akuphunzitseni mfundo zoyambirira+ za m’mawu opatulika a Mulungu,+ kuyambira pa chiyambi. Inu mwakhala ngati munthu wofunika mkaka, osati chakudya chotafuna.+
13 Pakuti aliyense woyamwa mkaka sadziwa mawu a chilungamo, chifukwa adakali kamwana.+
14 Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu, amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira,+ aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.+