Aheberi 6:1-20

6  Pa chifukwa chimenechi, pamene tasiya chiphunzitso choyambirira+ cha Khristu+ tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.+ Tisayambe kuyalanso maziko,+ amene ndi kulapa ntchito zakufa,+ chikhulupiriro mwa Mulungu,+  chiphunzitso chokhudza ubatizo,+ kuika manja,+ kuuka kwa akufa+ ndi chiweruzo chamuyaya.+  Mulungu akalola, tiyesetsadi mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.+  Pali anthu amene Mulungu anawaunikira,+ amene analawa mphatso yaulere yakumwamba,+ amene analandira mzimu woyera,+  amene analawa+ mawu abwino a Mulungu ndi zotsatira za mphamvu zimene Mulungu adzaonetse m’nthawi* imene ikubwerayo,+  koma tsopano anagwa.+ Anthu amenewa n’zosatheka kuwadzutsanso kuti alape.+ N’zosatheka chifukwa chakuti anthu amenewa akupachika kachiwiri Mwana wa Mulungu ndi kumunyoza poyera.+  Mwachitsanzo, nthaka imamwa madzi a mvula imene imagwera panthakapo kawirikawiri. Kenako imatulutsa zomera zimene zimapindulitsa amene ailima.+ Nthaka imeneyi imalandiranso dalitso kuchokera kwa Mulungu.  Koma ikatulutsa minga ndi mitula, imakanidwa ndipo imatsala pang’ono kutembereredwa.+ Mapeto ake imatenthedwa.+  Komabe ngakhale kuti tikulankhula motere, ndife otsimikiza kuti kwa inu okondedwa, zinthu zili bwino kwambiri kuposa amene anagwa aja. Muli ndi zinthu zabwino kwambiri zobweretsa chipulumutso. 10  Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ mwa kutumikira oyera+ ndipo mukupitiriza kuwatumikira. 11  Koma tikufuna kuti aliyense wa inu apitirize kuonetsa khama limene anali nalo poyamba, kuti chiyembekezo+ chanu chikhale chotsimikizika+ mpaka mapeto.+ 12  Pitirizani kuchita zimenezi kuti musakhale aulesi,+ koma mukhale otsanzira+ anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.+ 13  Pamene Mulungu analonjeza Abulahamu,+ analumbira pa dzina lake+ chifukwa panalibe wina wamkulu kwa iye amene akanamulumbirira. 14  Iye anati: “Kudalitsa, ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakuchulukitsadi.”+ 15  Choncho Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli.+ 16  Pakuti anthu polumbira amatchula winawake wamkulu kwa iwo,+ ndipo lumbiro lawo limathetsa mkangano uliwonse, chifukwa kwa iwo lumbiro ndi chotsimikizira chalamulo.+ 17  Mofanana ndi zimenezi, Mulungu pofuna kuwatsimikizira kwambiri anthu olandira lonjezolo monga cholowa chawo,+ kuti chifuniro chake n’chosasinthika,+ anachita kulumbira pa zimene analonjezazo. 18  Anachita zimenezo kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, zimene chifukwa cha zinthu zimenezo n’zosatheka kuti Mulungu aname,+ ife amene tathawira kumalo otetezeka tilimbikitsidwe kwambiri, kuti tigwire mwamphamvu chiyembekezo+ chimene chaikidwa patsogolo pathu. 19  Chiyembekezo+ chimene tili nachochi chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika. Chiyembekezo chimenechi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa nsalu yotchinga,+ 20  kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Nangula” ndi chinthu chimene amachimangirira kusitima ndipo amachiponya pansi pa nyanja kuti sitima ikaima isatengeke ndi mphepo.