Aheberi 1:1-14

1  Kalekale, Mulungu analankhula ndi makolo athu nthawi zambiri+ ndiponso m’njira zambiri kudzera mwa aneneri.+  Kumapeto kwa masiku ano,+ iye walankhulanso kwa ife kudzera mwa Mwana wake,+ amene anamuika kuti akhale wolandira zinthu zonse monga cholowa.+ Kudzera mwa iyeyu, Mulungu analenga+ nthawi* zosiyanasiyana.  Iye amasonyeza ndendende mmene ulemerero wa Mulungu ulili+ ndipo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo,+ ndipo amachirikiza zinthu zonse mwa mawu ake amphamvu.+ Atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala pansi kudzanja lamanja+ la Wolemekezeka m’malo okwezeka.+  Choncho iye wakhala woposa angelo,+ moti monga cholowa chake, walandira dzina+ lapamwamba kwambiri kuposa lawo.  Mwachitsanzo, kodi Mulungu anauzapo mngelo uti kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala atate wako”?+ Kapena kuti: “Ine ndidzakhala atate wake ndipo iye adzakhala mwana wanga”?+  Koma ponena za nthawi imene adzatumize kachiwiri Mwana wake Woyamba kubadwayo+ padziko lapansi kumene kuli anthu, iye akuti: “Angelo+ onse a Mulungu amugwadire.”+  Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amapanga angelo ake kukhala mizimu, ndipo amapanganso antchito ake otumikira ena kukhala lawi la moto.”+  Koma ponena za Mwana wake, iye akuti: “Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka muyaya,+ ndipo ndodo ya ufumu+ wako ndiyo ndodo yachilungamo.+  Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu kuposa cha mafumu ena.”+ 10  Iye akunenanso kuti: “Inu Ambuye, pachiyambipo munaika maziko a dziko lapansi, ndipo kumwamba ndiko ntchito ya manja anu.+ 11  Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapo mpaka muyaya. Ndipo zonsezi zidzatha ngati mmene malaya akunja amathera.+ 12  Mudzapindapinda zinthu zimenezi ngati mkanjo,+ ndipo zidzasinthidwa ngati malaya akunja. Koma inu simudzasintha, ndipo zaka za moyo wanu sizidzatha.”+ 13  Koma kodi ndi mngelo uti amene anamuuzapo kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako”?+ 14  Kodi angelo onse si mizimu+ yotumikira ena,+ yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo?+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.