Aheberi 4:1-16

4  Chotero, popeza lonjezo lolowa mu mpumulo wake lidakalipo,+ samalani kuopera kuti pa nthawi ina, wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+  Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ monga mmenenso unalengezedwera kwa makolo athu.+ Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo,+ chifukwa sanakhale ndi chikhulupiriro+ ngati cha amene anamvera mawuwo.+  Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira+ mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti ntchito zake zinali zitatha+ kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.*+  Pakuti penapake, ponena za tsiku la 7, anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+  Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+  Choncho, popeza kuti ena ayenerabe kulowa mu mpumulo umenewo, ndipo amene anali oyamba kuwalalikira uthenga wabwino+ sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+  iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+  Pakuti ngati Yoswa+ anawalowetsa m’malo ampumulo,+ Mulungu sakananenanso pambuyo pake+ za tsiku lina.  Chotero mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10  Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu,+ ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake,+ monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake. 11  Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+ 12  Pakuti mawu+ a Mulungu ndi amoyo+ ndi amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo+ ndi mzimu,+ komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.+ 13  Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ 14  Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+ 15  Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni+ pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16  Choncho, tiyeni tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu+ ndi ufulu wa kulankhula,+ kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.