Aheberi 3:1-19

3  Chotero, abale athu oyera, amene muli nawo m’gulu la oitanidwa kumwamba,+ ganizirani za Yesu, mtumwi+ ndi mkulu wa ansembe amene tikumuvomereza.+  Iye anali wokhulupirika+ kwa Mulungu amene anamuika kukhala mtumwi ndi mkulu wa ansembe, monga mmenenso Mose+ analili wokhulupirika m’nyumba yonse ya Mulungu.+  Pakuti Yesu waonedwa kukhala woyenera ulemerero waukulu+ kuposa Mose, monganso mmene womanga+ nyumba amakhalira wolemekezeka kuposa nyumbayo.+  N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.+  Ndipo Mose monga wantchito+ anali wokhulupirika m’nyumba yonse ya Mulungu. Utumiki wakewo unali umboni wa zinthu zimene zidzalankhulidwe m’tsogolo.+  Koma Khristu monga Mwana+ wa mwiniwake wa nyumbayo, anali kuyang’anira nyumba ya Mulungu mokhulupirika. Ife ndife nyumba ya Mulunguyo,+ ngati tagwira mwamphamvu ufulu wathu wa kulankhula ndi kupitirizabe kunyadira chiyembekezocho mpaka mapeto.+  Pa chifukwa chimenechi, mzimu woyera+ ukunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+  musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima,+ ngati mmene zinalili pa tsiku la mayeso+ m’chipululu.+  M’chipululumo, makolo anu anandiyesa ndi mayesero, ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga+ kwa zaka 40.+ 10  Pa chifukwa chimenechi ndinanyansidwa ndi m’badwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,+ ndipo sadziwa njira zanga.’+ 11  Choncho ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga.’”+ 12  Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13  M’malomwake, pitirizani kudandaulirana+ tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuopera kuti chinyengo+ champhamvu cha uchimo chingaumitse mtima wa wina wa inu. 14  Pakuti kwenikweni timachita nawo zimene Khristu akuchita,+ ngati zinthu zimene tinali kudalira pa chiyambi, tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.+ 15  Tichite zimenezi pamene Malemba akunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima.”+ 16  Kodi paja ndi ndani amene anamva koma n’kupsetsa mtima Mulungu?+ Kodi si anthu onse amene anatuluka m’dziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+ 17  Komanso, kodi Mulungu ananyansidwa ndi ndani kwa zaka 40?+ Kodi sananyansidwe ndi anthu amene anachimwa aja, amene anafera m’chipululu?+ 18  Nanga kodi analumbirira+ ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Kodi si omwe aja amene anachita zosamvera?+ 19  Choncho, tikuona kuti sakanatha kulowa mu mpumulowo chifukwa anali opanda chikhulupiriro.+

Mawu a M'munsi