Yankho la m’Baibulo

Inde angayankhe. Baibulo limasonyeza zimenezi komanso anthu ena aona okha kuti Mulungu amayankha mapemphero. Baibulo limati: “Anthu amene amamuopa [Mulungu] adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Salimo 145:19) Kuti Mulungu ayankhe mapemphero anu zimadalira kwambiri pa zimene inuyo mumachita.

Zimene Mulungu amafuna

  • Muzipemphera kwa Mulungu osati kwa Yesu, Mariya, anthu oyera mtima, angelo kapena mafano. Yehova Mulungu yekha ndi amene ‘amamva pemphero.’​—Salimo 65:2.

  • Muzipemphera mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna zomwe zalembedwa m’Baibulo.​—1 Yohane 5:14.

  • Muzipemphera m’dzina la Yesu chifukwa zimenezi zimasonyeza kuti mukuzindikira udindo wa Yesu. Paja iye anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”​—Yohane 14:6.

  • Musamakayikire zimene mukupempha ndipo nthawi zina mungapemphenso kuti akuwonjezereni chikhulupiriro.​—Mateyu 21:22; Luka 17:5.

  • Muzipemphera kuchokera pansi pa mtima ndiponso modzichepetsa. Baibulo limati: “Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa.”​—Salimo 138:6.

  • Muzipemphera mwakhama. Paja Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”​—Luka 11:9.

Zimene Mulungu saganizira poyankha

  • Mtundu kapena dziko lanu. “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:​34, 35.

  • Mmene mwakhalira. Zilibe kanthu kuti mwakhala, mwagwada, mwawerama kapena mwaima.​—1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25.

  • Ngati mukupemphera motulutsa mawu kapena chamumtima. Mulungu amayankha mapemphero ngakhale amumtima.​—Nehemiya 2:​1-6.

  • Ngati nkhaniyo ndi yaing’ono kapena yaikulu. Mulungu akukulimbikitsani ‘kumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.