Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Yankho la m’Baibulo

 Inde, Mulungu amathandiza anthu amene amapempha kuchokera pansi pa mtima zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Mwina inu simunapempherepo koma mukhoza kulimbikitsidwa kuona zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anapemphera kwa Mulungu kuti, “Ndithandizeni” kapena kuti, “Inu ndinu mthandizi wanga.” Mwachitsanzo:

  •   “Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu.”—Salimo 109:26, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

  •   “Ine ndine wozunzika ndi waumphawi . . . Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga.”—Salimo 40:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

 N’zoona kuti amene analemba mawu amenewa ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Koma Mulungu amamvetseranso munthu aliyense amene akupemphera ndi cholinga chabwino. Mwachitsanzo amamvetsera anthu “a mtima wosweka” kapena “odzimvera chisoni mumtima mwawo.”—Salimo 34:18.

 YMusamaganize kuti Mulungu ali kutali kwambiri ndi inuyo moti mavuto anu alibe nawo ntchito. Baibulo limanena kuti: “Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa, koma wodzikuza samuyandikira.” (Salimo 138:6) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.” (Mateyu 10:30) Mulungu amakudziwani bwino kwambiri kuposa mmene inuyo mumadzidziwira. Choncho n’zosakayikitsa kuti akhoza kuyankha mapemphero anu pamene muli pa mavuto enaake.—1 Petulo 5:7.