Chichewa
Malo a Nkhani
https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/d71826a198/images/syn_placeholder_sqr.png

Malo a Nkhani

 

2016-02-18

ANGOLA

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Angola

Madzi atangosefukira m’chigawo cha Benguela ku Angola, a Mboni anakhazikitsa komiti yoti ithandize anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.

2015-09-28

GUATEMALA

Sukulu za ku Guatemala Zinapempha Mabuku kwa a Mboni za Yehova Pofuna Kuthandiza Achinyamata Kuti Asiye Kuchita Zachiwawa

Sukulu za ku Guatemala zinapempha mabuku athu ambiri omwe ndi a zinenero za Chispanish komanso Quiché. Mabukuwa amawagwiritsa ntchito pophunzitsa m’kalasi n’cholinga chofuna kuthandiza ana a sukulu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

2015-06-03

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Alengeza za Misonkhano Yachigawo ya 2015

Misonkhano yachigawo ya 2015 ya Mboni za Yehova ya mutu wakuti “Tsanzirani Yesu” idzathandiza anthu kudziwa mmene angapindulire ndi chitsanzo cha Yesu. Misonkhanoyi idzachitika m’madera osiyanasiyana padziko lonse kuyambira mu May 2015 mpaka January 2016.

2016-02-18

MEXICO

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero cha Chitsotsilu Linatulutsidwa ku Mexico

A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu (Chipangano Chatsopano) la Chinenero cha Chitsotsilu. Chinenerochi chimayankhulidwa ndi anthu a mtundu wa Maya omwe amakhala m’madera okwera a chigawo chapakati ku Chiapas.

2016-02-18

RUSSIA

Wa Mboni Wina wa ku Russia Anatola Ndalama Zokwana Mayuro 6,000 Ndipo Anazibweza kwa Mwini Wake

Mayi Svetlana Nemchinova, omwe ndi a Mboni za Yehova, anafufuza mwini wa ndalama zomwe zinatayidwa mwangozi pamalo ena.

2018-11-15

VANUATU

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho

A Mboni za Yehova akuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene katundu wawo kapena nyumba zawo zinawonongeka ndi mphepo yoopsa.

2015-12-07

AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Likupitirizabe Kuphwanya Ufulu Wachipembedzo

Akuluakulu a boma akusokoneza misonkhano ya Mboni za Yehova yomwe amaichita mwamtendere ndipo akuwalipiritsa ndalama zambiri komanso a Mboni ena akumangidwa. Kodi akuluakulu a boma la Azerbaijan athandiza kuti zinthu ziyambe kuyenda mwachilungamo?

2015-05-10

MOZAMBIQUE

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique

A Mboni za Yehova akupitiriza kupereka zinthu zofunika kwa anthu okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi m’chigawo chakumpoto ndi chapakati m’dziko la Mozambique. Kuwonjezera pamenepa, akuwalimbikitsanso pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

2015-08-04

KYRGYZSTAN

Akuluakulu a Boma ku Kyrgyzstan Sakumanga Mfundo Imodzi pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo

Pa December 24, 2014, khoti lalikulu linalimbikitsa kuti nzika zonse kuphatikizapo a Mboni za Yehova zili ndi ufulu wouza ena zimene amakhulupirira. Kodi nthawi yakwana yoti a Mboni za Yehova m’madera a kumwera kwa Kyrgyzstan ayambe kuchita zinthu mwaufulu?

2016-02-18

UNITED STATES

A Mboni Analandira Mphoto Chifukwa Chosamalira Zachilengedwe pa Ntchito Yawo Yomanga

Nyumba ziwiri zomwe zinamangidwa ndi a Mboni za Yehova ku Wallkill mumzinda wa New York, zinalandira mphoto chifukwa chomangidwa mosawononga chilengedwe.

2015-12-07

SOUTH KOREA

Dziko la South Korea Lapezeka ndi Mlandu Womanga Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Chaka chilichonse, dziko la South Korea limamanga anyamata a Mboni chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Komiti Yoona za Ufulu Wachibadwidwe ya Bungwe la United Nations lanenetsa kuti dziko la South Korea lilibe zifukwa zomveka zomangira a Mboniwa. Aka ndi ka nambala 5 kuti komitiyi ikane zifukwazi.

2015-12-07

ARMENIA

Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Okana Kulowa Usilikali

Werengani zimene a Mboni za Yehova, anthu amene akugwira nawo ntchito ndiponso amene akuwayang’anira ananena zokhudza dongosololi.

2015-07-20

KAZAKHSTAN

A Mboni za Yehova Anagawa Baibulo la Chinenero cha Chikazaki Pamsonkhano Komanso Pamwambo Umene Anaitanira Anthu Ambiri

A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Chikazaki pamsonkhano womwe unachitikira munzinda wa Almaty ku Kazakhstan.

2015-05-10

PHILIPPINES

Anthu Amene Anakhudziwa ndi Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Typhoon Haiyan Tsopano Amangiridwa Nyumba

Mphepo yamkuntho yotchedwa Typhoon Haiyan itawononga zinthu, a Mboni za Yehova anagwira ntchito yaikulu yomanga nyumba pafupifupi 750.

2015-06-03

POLAND

Mwambo Wokumbukira Kuti Patha Zaka 70 Kuchokera Pamene Anthu Anatulutsidwa Kundende ya Auschwitz Ndipo Ena Mwa Anthuwa Anali a Mboni

Pa January 27, 2015, anthu ambirimbiri adzapezeka pa mwambo wokumbukira kuti patha zaka 70 kuchokera pamene anthu anatulutsidwa kundende ya Auschwitz yomwe ankazunzirako anthu nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku German.