Pitani ku nkhani yake

MARCH 6, 2015
MOZAMBIQUE

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique

A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique

MAPUTO, Mozambique—Mvula yamphamvu yomwe inagwa m’dera la Zambezia kuyambira mwezi wa December mpaka pakati pa mwezi wa January, inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri ndipo anthu 158 anafa. Ofesi ya Mboni za Yehova ku Mozambique inanena kuti palibe wa Mboni amene anavulala kapena kufa. Koma madzi osefukirawo anawononga Nyumba za Ufumu ziwiri za a Mboni za Yehova, ndiponso nyumba 225 za a Mboni.

A Mboni ongodzipereka anathandiza pa ntchito yopereka chakudya kwa anthu okhudzidwa ndi madzi osefukira m’dera la Chire lomwe lili m’boma la Zambezia.

A Mboni anakhazikitsa makomiti othandiza anthu okhudzidwawa. Pa nthawiyi anthu ena amene anakhudzidwa ankakhala kaye m’Nyumba za Ufumu zina ndipo nyumbazi ankazigwiritsa ntchito monga malo ogawira chakudya. Madzi osefukira anakokololanso mlatho wa m’dera lotchedwa Chire, lomwe lili pamtunda wa makilomita 1,500 kuchokera ku Maputo. Zimenezi zinachititsa kuti anthu azilephera kufika ku derali komwe kuli a Mboni 1,300. Unduna woona za maulendo a pandege unapereka chilolezo choti a Mboni agwiritse ntchito ndege pokapereka katundu wothandizira anthuwo ndipo katunduyu anali wokwana matani 17.

Anthu a ku Morrumbala, akupakira matumba a chimanga ndiponso mbewu ya chimanga kuti akagawire anthu

Bambo Alberto Libombo, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Mozambique, anati: “N’zosangalatsa kuti a Mboni anzathu anawolowa manja pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi. Ofesi ya Mboni za Yehova ku Mozambique ikupitiriza kupereka chakudya kwa anthu okhudzidwa ndiponso ikufuna kumanga ndi kukonza nyumba zowonongeka. Tipitirizanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo polimbikitsa anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi.”

Nyumba ya Ufumu ya ku Chiromo inagwiritsidwa ntchito monga malo ogawira chakudya

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Mozambique: Alberto Libombo, tel. +258 21 450 500