Nkhani za Padziko Lonse
Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 6 la 2026
Mulipotili, tifotokoza za kusintha kumene kwachitika pa zimene timakhulupirira zokhudza kugwiritsa ntchito zigawo zikuluzikulu za magazi. Vidiyoyi komanso nkhani ya mu “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” ndiponso tchati, zatulutsidwa kaye mu Chingelezi. Vidiyoyi komanso nkhani zina zofotokoza za kusinthaku, ziyamba kupezeka m’zilankhulo zinanso posachedwapa.
Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 5 la 2026
Mulipotili, tikambirana chifukwa chake tikuyenera kudzidyetsa mwauzimu tsiku lililonse. Tikambirananso zinthu zina zatsopano zimene tingauze anthu tikakhala mu utumiki.
Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 4 la 2026
Mulipotili, timva zinthu zolimbikitsa zokhudza maulendo ochezera nthambi komanso maulendo aubusa amene anachitika posachedwapa. Timvanso mmene milandu yomwe ikukhudza ufulu wathu wolambira yayendera ku Norway ndi ku Sweden.
Lipoti Lachitatu la Bungwe Lolamulira la 2026
Mulipotili, tiona mmene abale ndi alongo athu ku Russia asonyezera kupirira kungochokera pamene ntchito yathu inaletsedwa m’dzikolo zaka 9 zapitazo. Komanso, tilengeza kutulutsidwa kwa Magawo 4, 5 ndi 6 a vidiyo ya Uthenga Wabwino wa Yesu.

