Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 5, 2015
ARMENIA

Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Okana Kulowa Usilikali

Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Okana Kulowa Usilikali

Kuyambira chaka chatha, boma la Armenia linayamba kupereka ntchito zina kwa anthu amene akana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo. Panopa zikuoneka kuti zinthu zikuyenda bwino kwambiri. Anthu oyambirira kupatsidwa ntchito zina anali anyamata a Mboni za Yehova ndipo anapatsidwa ntchito ya zomangamanga m’malo mopita kundende chifukwa chokana kulowa usilikali.

Kungochokera mu 1985, achinyamata a Mboni za Yehova ankamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo. Zimenezi zinkachitika chifukwa m’dzikoli munalibe malamulo opereka ntchito zina kwa anthu okana kulowa usilikali, moti kungochokera nthawi imeneyi a Mboni oposa 450 anamangidwa ndipo anaikidwa m’ndende zoipa kwambiri. Koma mavuto amenewa anatha mu June 2013, pamene boma la Armenia linakhazikitsa malamulo opereka ntchito zina kwa anthu amene akana kulowa usilikali.

Choncho pofika pa 23 October, 2013, boma la Armenia linayamba kulola anthu amene akana kulowa usilikali pa zifukwa za chipembedzo kuti afunsire ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. Anthu oyambirira kupatsidwa mwayiwu analipo 57 ndipo onse anali a Mboni za Yehova. a Kenako bomali linkalola a Mboni enanso kufunsira nawo ntchitozi. Achinyamata a Mboni okwana 71 anayamba kugwira ntchitozi pa 13 January, 2014. Pofika chakumapeto kwa chaka cha 2014, anyamata a Mboni oposa 126 ankagwira nawo ntchitozi.

Njira Yothandiza Kwambiri

Ntchitoyi ikuyenda bwino kwambiri ndipo ngakhale amene akuyang’anira anyamatawa komanso azinzawo akumanena kuti anyamata a Mboniwo ndi akhalidwe labwino ndiponso olimbikira ntchito. Anthu ena a m’komiti imene ikuyang’anira ntchitoyi anayamikira anyamata a Mboniwa chifukwa cha khama lawo akamagwira ntchitoyi. Anenanso kuti ntchitoyi ikuthandiza kwambiri pa chitukuko cha dzikolo.

  • Woyang’anira ntchito wina wa mu mzinda wa Yerevan wa m’dera la Shengavit anati: “Anyamata inu mukuigwira ntchito ngakhale kuti mukulandira malipiro ochepa kwambiri. Aliyense akuona kuti ndinu olimbikira ntchito zedi.”

  • Namwino wina wa pamalo ena osungira ana amasiye omwe a Mboni ena anauzidwa kuti azikagwirapo ntchito anati: “Ndinu anthu abwino kwambiri. Mumayesetsa kutsatira zimene mumaphunzira kuchipembedzo chanu komanso mumathandiza kwambiri pa chitukuko.”

  • Woyang’anira ntchito wina wa mu mzinda wa Yerevan m’dera la Arabkir anati: “Ndinu anyamata olimbikira ntchito kwambiri. Kodi mulinso ndi anzanu ena? Ndingakonde atabwera kuti adzagwire ntchito kunoko.

Achinyamata a Mboni za Yehova anakonza komanso kukongoletsa malo ena mumzinda wa Yerevan.

A Mboni amene akugwira ntchito yosagwirizana ndi usilikali ananenanso kuti dongosololi ndi labwino kwambiri.

  • A Gevorg Taziyan omwe amagwira ntchito yothandiza dalaiva m’dipatimenti ina yoona zopulumutsa anthu pangozi anati: “Anzanga amene ndimagwira nawo ntchito ndi achikondi ndiponso ndi aulemu kwambiri. Tsiku lina ndinadwala moti sindikanatha kupita kuntchito. Anzangawo atamva zimenezi anandiimbira foni kuti amve kuti ndikupeza bwanji. Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira ntchitoyi chifukwa sitsutsana ndi zimene ndimakhulupirira.”

  • “A Samvel Abrahamyan omwe amagwira ntchito yosamalira malo pachipatala china anati: “Timagwirizana kwambiri ndi mabwana komanso anthu ena ogwira ntchito pachipatalachi. Anthu ake amatiganizira kwambiri ndipo nafenso timachita zimene tingathe kuti tiwasangalatse. Mwachitsanzo, nthawi zina timatha kudzipereka kuti tithandize nawo kugwira ntchito zina.”

  • A Artsrun Khachatryan omwe amagwira ntchito yosamalira malo pa ofesi ya unduna woona za zinthu zogwa mwadzidzidzi anati: “Tilipo anthu 13 amene timagwira ntchito pamalo amenewa ndipo tinayamba pa 14 January, 2014. Kungochokera nthawi imeneyi timasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi aliyense. Sitinayambe takanganapo ndi mabwana athu. Onse amasangalala kwambiri chifukwa amaona kuti timagwira ntchito molimbikira komanso mogwirizana.”

Zimene anthuwa ananena zikusonyeza kuti dongosolo loti anthu amene akana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zina likuyenda bwino ku Armenia. Zimenezi zikutheka chifukwa cha mgwirizano womwe ulipo pakati pa woyang’anira ndi a Mboni za Yehova omwe akumagwira ntchitoyi mokhulupirika komanso mwakhama. A Mboni za Yehova ku Armenia akusangalala kwambiri ndi zimene bomali lachita chifukwa panopa akutha kulambira Mulungu mwaufulu osamaopa kuti amangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali.