Kyrgyzstan
Kodi Apolisi Amene Anachitira Nkhanza a Mboni a ku Osh Adzapatsidwa Chilango?
A Mboni za Yehova akupempha ofesi ya loya wamkulu wa boma kuti achitepo kanthu ndipo apereke chilango kwa apolisi amene anachita nkhanzawo.
Akuluakulu a Boma ku Kyrgyzstan Sakumanga Mfundo Imodzi pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo
Pa December 24, 2014, khoti lalikulu linalimbikitsa kuti nzika zonse kuphatikizapo a Mboni za Yehova zili ndi ufulu wouza ena zimene amakhulupirira. Kodi nthawi yakwana yoti a Mboni za Yehova m’madera a kumwera kwa Kyrgyzstan ayambe kuchita zinthu mwaufulu?