Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | YESU ANATIPULUMUTSA KU UCHIMO NDI IMFA

N’chifukwa Chiyani Tikufunika Kupulumutsidwa?

N’chifukwa Chiyani Tikufunika Kupulumutsidwa?

“Munthu wobadwa kwa mkazi, amakhala ndi moyo waufupi, wodzaza ndi masautso. Amaphuka ngati duwa n’kuthotholedwa. Amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalaponso.”—Yobu 14:1, 2.

Kuyambira kale, anthu amafuna kukhala ndi thanzi labwino ndipo safuna kukalamba. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthufe timakalamba komanso timafa. Mawu a Yobu amene ali pamwambawa, omwe analembedwa zaka 3,000 zapitazo, adakali oona masiku ano.

Padziko lonse anthu amafuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale ndipo Mulungu ndi amene anatipatsa mtima umenewu. (Mlaliki 3:11) Mulungu amafunanso kuti tizisangalala ndi moyo. Kodi zikanakhala kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo mpaka kalekale, Mulungu akanatipatsa mtima umenewu? Ayi. Baibulo limanena kuti imfa ndi mdani ndipo limanenanso kuti “idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

Imfa ndi mdani wa anthu kuyambira kalekale ndipo palibe munthu wabwinobwino yemwe angafune kufa. Tikaona zoopsa timathawa kapena kubisala. Tikadwala timayesetsa kuchita zinthu zoti tichire. Komanso timayesetsa kupewa zinthu zomwe zingaike moyo wathu pachiswe.

Koma kodi n’zoona kuti imfa idzawonongedwa? Inde n’zoona. Mlengi wathu, Yehova, sanatilenge kuti tizikhala ndi moyo zaka zochepa kenako n’kumwalira. Sichinali cholinga chake kuti anthu azifa. Ankafuna kuti anthu azikhala padzikoli mpaka kalekale ndipo zimenezi zidzachitikadi popeza nthawi zonse amakwaniritsa cholinga chake.—Yesaya 55:11.

Kodi imfa idzathetsedwa bwanji? Kale anthu anayesetsa kuthetsa imfa koma analephera. Masiku anonso anthu ena sakugona tulo pofuna kuthetsa imfa. Asayansi apanga akatemera komanso mankhwala omwe athandiza kuti matenda ena athe. Aphunziranso zambiri zokhudza mmene thupi la munthu limagwirira ntchito. Panopa anthu m’mayiko ambiri akumakhala ndi moyo wotalikirapo poyerekeza ndi zaka 100 zapitazo. Koma ngakhale zili chonchi, anthu akufabe chifukwa palibe wakwanitsa kuthetsa imfa. Zimenezi zikungogwirizana ndi zomwe Baibulo limanena kuti, “zonse zimabwerera kufumbi.”—Mlaliki 3:20.

Izi zikusonyeza kuti sitingadalire anthu kuti athetse imfa. Koma n’zosangalatsa kuti Yehova adzathetsa imfa. Yehova wakonza zoti adzatipulumutse kwa mdani ameneyu ndipo adzachita zimenezi kudzera mwa Yesu Khristu.