Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Tiyenera Kulambira Mafano?

Kodi Tiyenera Kulambira Mafano?

Yankho la m’Baibulo

Ayi. Buku lina linanena zokhudza malamulo amene Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli. Bukulo linati: “Nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo zimasonyeza kuti anthu amene ankalambira Mulungu m’njira yovomerezeka sankagwiritsa ntchito mafano.” (New Catholic Encyclopedia) Taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

  • “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira, chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.” (Ekisodo 20:4, 5) Popeza Mulungu amafuna kuti ‘tizidzipereka kwa iye yekha,’ sasangalala tikamalambira mafano, zithunzi kapena zinthu zina.

  • “Sindidzapereka . . . ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.” (Yesaya 42:8) Mulungu amakana kumulambira pogwiritsa ntchito mafano. Aisiraeli atamulambira pogwiritsa ntchito fano la mwana wa ng’ombe, Mulungu anawauza kuti zimene anachitazo ndi “tchimo lalikulu.”Ekisodo 32:7-9, Easy-to-Read Version.

  • “Tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.” (Machitidwe 17:29) Mosiyana ndi anthu achikunja amene amalambira pogwiritsa ntchito mafano ‘osemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu,’ Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera “kuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.”2 Akorinto 5:7.

  • “Pewani mafano.” (1 Yohane 5:21) Malamulo opezeka m’Baibulo opita kwa mtundu wa Isiraeli komanso kwa Akhristu amanena mosapita m’mbali kuti zimene anthu ena amaphunzitsa zakuti Mulungu amavomereza kugwiritsa ntchito mafano pomulambira n’zabodza.