Kodi Mukudziwa?
Kodi kukhala nzika ya Roma kunathandiza bwanji mtumwi Paulo?
Munthu akakhala nzika ya Roma ankakhala ndi mwayi komanso ufulu wambiri. Nzika ya Roma inkatsatira malamulo a boma la Roma osati a mizinda ina yomwe inali pansi pa ufumuwo. Munthu yemwe ndi nzika ya Roma akakhala ndi mlandu, ankatha kuvomera kuti aimbidwe mlanduwo motsatira malamulo a dera limene akukhala. Koma analinso ndi ufulu wosankha kukaweruzidwa potsatira malamulo a Roma. Akakhala kuti wapatsidwa chilango choti aphedwe, anali ndi ufulu wochita apilo kuti akaweruzidwe ndi mfumu ya Roma.
Chifukwa cha ufulu womwe nzika ya Roma inkakhala nawowu, mkulu wina wa boma wachiroma dzina lake Cicero anati, kumanga ndiponso kuzunza nzika ya Roma unali mlandu. Komanso kupha nzika ya Roma kunali ngati kupha kholo lawo kapena m’bale wawo.
Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito ufulu wake monga nzika ya Roma pamene ankalalikira ku Roma. Baibulo limatchula maulendo atatu pamene Paulo anagwiritsa ntchito ufulu wakewu. Koyamba anauza akuluakulu a ku Filipi kuti anamuphwanyira ufulu wake pomukwapula. Kachiwiri, ali ku Yerusalemu ananena kuti ndi nzika ya Roma n’cholinga choti asakwapulidwe. Ndipo kachitatu anapanga apilo mlandu wake kuti ukaweruzidwe ndi Kaisara.—Machitidwe 16:37-39; 22:25-28; 25:10-12.
Kodi kale abusa ankawalipira bwanji?
Yakobo anagwira ntchito yoweta ziweto za amalume ake a Labani kwa zaka 20. Pa zaka 14 zimene anagwira ntchitoyi, Labani anamupatsa ana ake aakazi awiri ngati malipiro ake. Ndipo malipiro a zaka 6 zinazo, anali ziweto. (Genesis 30:25-33) Magazini ina inanena kuti: “Mgwirizano wa malipiro wangati umene anachita Labani ndi Yakobo, ndi umene anthu ambiri ankakonda kuchita. Unali wodziwika bwino kwa anthu amene analemba Baibulo komanso amene ankawerenga Malemba.”—Biblical Archaeology Review.
Mapale ena omwe panalembedwa malipiro amene eni nkhosa ndi abusa ankagwirizana, anawapeza kumalo ofufuzira zinthu zakale otchedwa Nuzi, ku Larsa komanso kumadera ena a ku Iraq. Nthawi zambiri mgwirizano unkakhala wachaka chimodzi, kuyambira pa nthawi yometa ubweya wa ziweto kudzafikanso pa nthawiyi chaka chotsatira. Abusa akagwirizana ndi mwini ziweto, ankakhala ndi udindo wosamalira ziweto zonse zimene agwirizana. Posankha ziweto, m’busa ankaganiziranso zaka za ziwetozo komanso kuti ndi zazikazi kapena zazimuna. Chaka chikatha, m’busa ankafunika kupereka kwa mwini ziweto zinthu zomwe anagwirizana monga ubweya, mkaka, ana amene ziweto zaswa ndi zinthu zina. Ngati ziwetozo zatulutsa ubweya, mkaka komanso ana oposa omwe anagwirizana, zotsalazo zinkakhala za m’busayo.
Ziweto zinkachuluka kwambiri zikakhala kuti m’busa anapatsidwa ziweto zazikazi zambiri. Mwachitsanzo ngati m’busa wapatsidwa nkhosa zazikazi 100, ankayembekezera kuti zibereka ana 80. Koma ngati ana omwe nkhosa zabereka sanakwane chiwerengero chomwe anagwirizana, m’busa ankayenera kulipira kotsalako. Choncho m’busa ankafunika kusamalira bwino nkhosa zake pofuna kupewa zimenezi.