Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | YESU ANATIPULUMUTSA KU UCHIMO NDI IMFA

Kodi Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Udzachitika Liti?

Kodi Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Udzachitika Liti?

Usiku woti afa mawa lake, Yesu analamula ophunzira ake kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Anawauza kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—Luka 22:19.

Chaka chino, mwambowu udzachitika Lachisanu pa 3 April, dzuwa litalowa. A Mboni za Yehova akukuitanani inuyo limodzi ndi banja lanu kuti mudzabwere kumwambowu. Padzakambidwa nkhani yomwe idzafotokoze kufunika kwa imfa ya Yesu komanso kuti ingakupindulitseni bwanji.