Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Isitala?

Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Isitala?

Buku lina limanena kuti Isitala ndi “chikondwerero chofunika kwambiri chimene matchalitchi achikhristu amachita pokumbukira kuuka kwa Yesu Khristu.” (Encyclopædia Britannica) Koma kodi Akhristu ayeneradi kukondwerera Isitala?

Anthu akafuna kudziwa zoona za nkhani inayake, amafufuza mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. Choncho kuti tidziwe ngati Akhristu ayenera kukondwerera Isitala kapena ayi, tiyenera kudziwa zambiri zokhudza chikondwerero chimenechi.

Choyamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti azikumbukira imfa yake, osati kuuka kwake. Mtumwi Paulo anatchula mwambo wokumbukira imfa ya Yesuwu kuti, “chakudya chamadzulo cha Ambuye.”—1 Akorinto 11:20; Luka 22:19, 20.

Chachiwiri, buku lomwe talitchula lija linanenanso kuti miyambo yambiri yomwe imachitika pa Isitala “ndi yochokera ku miyambo ya anthu ndipo ndi yosagwirizana n’komwe” ndi nkhani ya kuuka kwa Yesu. Mwachitsanzo, buku lina linanena za zinthu zomwe zimagwiritsidwa ntchito pa Isitala zomwe ndi mazira komanso akalulu. Linati: “Amagwiritsa ntchito mazira chifukwa dzira limasweka n’kutulutsa chamoyo, choncho amati mazirawo amaimira kuyambika kwa moyo. Pomwe kalulu, popeza amadziwika kuti amaswa ana ambiri, amati amaimira chiyambi cha nyengo imene mitengo yambiri imayamba kuphuka masamba ndi kuchita maluwa.”—The Encyclopedia of Religion.

Pulofesa wina dzina lake Philippe Walter, yemwe amafufuza nkhani za m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500 AD, anafotokoza zomwe zinachitika kuti Akhristu ayambe kuchita chikondwerero cha Isitala. Analemba kuti, “Akhristu atayamba kutengera miyambo yazipembedzo zachikunja,” anayambanso kugwirizanitsa kuuka kwa Yesu ndi mwambo wokondwerera chiyambi cha nyengo yomwe mitengo imachita maluwa.” Walter ananena kuti Akhristu anachita zimenezi pofuna kukopa anthu ambiri akunja kuti alowe Chikhristu.

Zimenezi sizinkachitika pa nthawi imene atumwi anali moyo chifukwa atumwiwo anali ngati “choletsa” kuti miyambo yachikunja isalowe mu mpingo wachikhristu. (2 Atesalonika 2:7) Mtumwi Paulo anali ataneneratu kuti ‘akachoka,’ anthu ena “adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (Machitidwe 20:29, 30) Chitatsala pang’ono kukwana chaka cha 100 C.E., mtumwi Yohane analemba kuti anthu ena anali atayamba kale kusocheretsa Akhristu. (1 Yohane 2:18, 26) Zimenezi zinachititsa kuti zikondwerero zachikunja zilowe mu mpingo wachikhristu.

“Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira.”—2 Akorinto 6:14.

Koma anthu ena angaganize kuti kuchita miyambo ya Isitala kunalibe vuto chifukwa izi zinathandiza kuti anthu achikunja amvetse bwino nkhani ya kuuka kwa Yesu. Koma mtumwi Paulo sakanagwirizana ndi maganizo amenewa. Mwachitsanzo, pa nthawi yomwe anali ku Roma, komwe kunkachitika miyambo yambiri yachikunja, sanayambe kuchita nawo miyamboyo poganiza kuti kuchita zimenezi kuthandiza kuti Aroma adziwe Yesu. M’malomwake iye anachenjeza Akhristu kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima? ‘Choncho tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa.’”—2 Akorinto 6:14, 17.

Kodi zimene takambirana m’nkhaniyi zikutiuza chiyani za Isitala? Zikutiuza kuti Akhristu oona sayenera kuchita chikondwerero cha Isitala.