Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Umboni Woti Zozizwitsa Zotchulidwa M’Baibulo Zinachitikadi

Umboni Woti Zozizwitsa Zotchulidwa M’Baibulo Zinachitikadi

Umboni Woti Zozizwitsa Zotchulidwa M’Baibulo Zinachitikadi

TIYEREKEZE kuti mwauzidwa nkhani inayake yodabwitsa kwambiri. N’kutheka kuti musanaikhulupirire, mungaganizire kaye za munthu amene wakuuzani nkhaniyo. Mwina mungaganizire mmene munthuyo akufotokozera nkhaniyo komanso ngati ali ndi mbiri yoti amanena zoona. Ngati munthuyo nthawi zonse amanena zoona muyenera kuti mungakhulupirire kuti nkhani imene akunenayonso ndi yoona.

N’chimodzimodzinso ndi zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo. Zozizwitsa zimenezi zinachitika ife tisanabadwe. Koma n’zotheka kudziwa ngati nkhani za m’Baibulo zilidi zoona. Kodi tingadziwe bwanji? Mfundo zotsatirazi zingatithandize kudziwa kuti nkhani zomwe zili m’Baibulo zonena za zozizwitsa zinachitikadi.

Zozizwitsa zambiri zinkachitika pamaso pa anthu ambiri. Nthawi zambiri zozizwitsazi zinkachitika pali anthu ambirimbiri oonerera, osati mobisa.​—Ekisodo 14:21-31; 19:16-19.

Ochita zozizwitsawo sankachita zinthu mokokomeza. Iwo sankavala mwapadera, kuchita zinthu mongofuna kudzionetsera komanso sankachita zowaphimba anthu m’maso kuti asazindikire chimene chikuchitika. Nthawi zambiri anthu amene anachita zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo sankachita kukonzekera kuti achita zozizwitsa ndipo nthawi zina ankangochita chifukwa choti anthu awapempha. (Maliko 5:25-29; Luka 7:1-10; Luka 7:11-16) Pa zochitika ngati zimenezi, anthuwa ankakhala oti mwinanso akanapanda kukumana ndi zimene zachititsa kuti apange zozizwitsazo, sakanachita n’komwe zozizwitsa.

Cholinga cha anthu amene anachita zozizwitsazo sichinali kufuna kutchuka, kutamandidwa kapena kupeza ndalama. Anthuwa ankachita zozizwitsazi n’cholinga choti Mulungu alemekezeke. (Yohane 11:1-4, 15, 40) Munthu aliyense amene ankafuna kupeza chuma chifukwa cha zozizwitsa ankadzudzulidwa.​—2 Mafumu 5:15, 16, 20, 25-27; Machitidwe 8:18-23.

Zozizwitsa zosiyanasiyana zimene zili m’Baibulo zimasonyeza kuti sizinachitike ndi mphamvu za munthu. Zina mwa zozizwitsa zimenezi ndi kuletsa mafunde panyanja, kusandutsa madzi kukhala vinyo, kuletsa ndi kuyambitsa mvula ndiponso kuchiritsa odwala ndi osaona. Zozizwitsa zimenezi, komanso zina zambiri, zimasonyeza kuti panali mphamvu inayake yoposa ya munthu imene inachititsa kuti zichitike.​—1 Mafumu 17:1-7; 18:41-45; Mateyu 8:24-27; Luka 17:11-19; Yohane 2:1-11; 9:1-7.

Otsutsa amene anaona zozizwitsazo sanakane kuti zinachitikadi. Yesu ataukitsa bwenzi lake Lazaro, atsogoleri achipembedzo amene ankadana ndi Yesuyo sanatsutse zoti Lazaro anafadi. Ndipotu iwo sakanatsutsadi chifukwa Lazaro anali atakhala m’manda masiku anayi. (Yohane 11:45-48; 12:9-11) Komanso patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, Ayuda amene analemba buku lina lotchedwa Talmud sanatsutse zoti Yesu ankachita zozizwitsa. Iwo anangotsutsa kuti mphamvu yochitira zozizwitsayo sinachokere kwa Mulungu. Chimodzimodzinso pa nthawi imene ophunzira a Yesu anawatengera kukhothi la Ayuda. Iwo sanafunsidwe kuti, “Kodi munachitadi zozizwitsa?” M’malomwake anawafunsa kuti: “Kodi mwachita zimenezi ndi ulamuliro uti kapena m’dzina la ndani?”​—Machitidwe 4:1-13.

Choncho, muyenera kukhulupirira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zozizwitsa. Malinga ndi zimene takambirana m’nkhaniyi, taona kuti pali umboni woti nkhani za m’Baibulo zonena za zozizwitsa zinachitikadi. Koma palinso zifukwa zina zomwe zingatichititse kuti tizikhulupirira nkhani za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Baibulo likamafotokoza nkhani limatchula malo, nthawi komanso mayina a anthu okhudzidwa ndi nkhaniyo. Ngakhale anthu amene amatsutsa Baibulo amachita chidwi chifukwa cha mmene limafotokozera mwatsatanetsatane komanso molondola mbiri yakale. Maulosi ambiri a m’Baibulo anakwaniritsidwa ndipo ngakhale zinthu zing’onozing’ono zinachitika mmene Baibulo linanenera. Komanso Baibulo lili ndi malangizo othandiza anthu kukhala bwino ndi anzawo. Malangizo a m’Baibulo pa nkhaniyi ndi othandiza kwambiri kuposa malangizo amene amapezeka m’mabuku ena onse. Ndipotu malangizo amenewa athandiza anthu osiyanasiyana, ana ndi akulu omwe.

Ngati inuyo simunayambebe kukhulupirira Baibulo, mungachite bwino kupeza nthawi yoliphunzira bwinobwino. Mukalidziwa bwino m’pamenenso mungayambe kulikhulupirira kwambiri. (Yohane 17:17) Kulidziwa bwino Baibulo kudzakuthandizani kukhulupirira kuti zozizwitsa zimene limafotokoza zinachitikadi. Kukhulupirira zimenezi kudzakuthandizaninso kukhulupirira kuti zimene limanena kuti zichitika posachedwapa, zichitikadi.

[Chithunzi patsamba 7]

Anthu amene ankam’tsutsa Yesu sanakane zoti Lazaro anafadi