Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Yesu Anakhala Liti Mfumu?

Kodi Yesu Anakhala Liti Mfumu?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Yesu analonjezedwa kuti adzakhala mfumu ya ufumu uti?

Mulungu analonjeza kuti mbadwa ya Mfumu Davide idzakhala pampando Wake wachifumu mpaka kalekale. Mbadwa ya Mfumu Davideyo ndi Yesu ndipo iye akulamulira kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.​—Werengani Salimo 89:4; Luka 1:32, 33.

Davide adakali mnyamata, Yehova anamusankha kuti akhale mfumu ya Aisiraeli, omwe anali anthu ake. Davide atamwalira, Solomo anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale “pampando wachifumu wa Yehova.” (1 Mbiri 28:4, 5; 29:23) Solomo atamwalira mafumu ena analamulira ku Yerusalemu koma ambiri anali osakhulupirika. Kenako Yehova analola kuti magulu ankhondo a ku Babulo awononge Yerusalemu n’kutengera kuukapolo mfumu imene inkalamulira pa nthawiyo. Zimenezi zinachitika mu 607 B.C.E. Kuchokera nthawi imeneyo palibe mfumu ina yochokera ku banja la Davide imene inalamulira ku Yerusalemu.​—Werengani Ezekieli 21:27.

2. Kodi Ufumu wa Mulungu unakhala usakuimiridwa padziko lapansi kwa nthawi yaitali bwanji?

Yerusalemu atangowonongedwa, Yehova anauza Danieli, yemwe anali mneneri wake, kuti adzasankha mfumu imene idzalamulire dziko lapansi ili kumwamba. Kodi mfumu imeneyo inali yoti idzayamba liti kulamulira?​—Werengani Danieli 7:13, 14.

Danieli anamasulira masomphenya amene Mulungu analamula kuti mtengo waukulu udulidwe. Zimenezi zinali zofanana ndi zimene Mulungu anachita polamula kuti ufumu wa ku Yerusalemu uwonongedwe. Koma chitsa cha mtengowo anayenera kuchisiya n’cholinga choti pakadutsa “nthawi zokwanira 7,” chidzaphukirenso. Baibulo limasonyeza kuti “nthawi” zitatu ndi hafu ndi masiku 1,260, choncho “nthawi zokwanira 7” ndi masiku 2,520. (Chivumbulutso 12:6, 14) M’maulosi a m’Baibulo nthawi zambiri masiku amaimira zaka. (Numeri 14:34) Choncho ulosiwu unasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhala wosaimiridwa padziko lapansi kwa zaka 2,520.​—Werengani Danieli 4:10-17.

  3. Kodi ndi liti pamene Yesu anakhala Mfumu?

Mulungu anaika Yesu kukhala Mfumu kumwamba mu 1914, patatha ndendende zaka 2,520 kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa. Yesu atangokhala Mfumu anachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-10) Anthu sanaone zimene zinachitikazi koma anangoona mavuto amene anachitika chifukwa cha zimenezi. (Chivumbulutso 12:12) Zimene zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914 zimasonyeza kuti Yesu anakhala Mfumu m’chaka chimenechi.​—Werengani Mateyu 24:14; Luka 21:10, 11, 31.

4. Kodi kudziwa kuti Yesu ndi mfumu kungakuthandizeni bwanji inuyo?

Kukwaniritsidwa kwa maulosi onena za ufumu wa Yesu kungakuthandizeni kudziwa kuti Mawu a Mulungu ndi odalirika. Posachedwapa Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake monga mfumu kuthetsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo.​—Werengani Salimo 72:8, 12, 13; Danieli 2:44.

Kuti mudziwe zambiri, werengani tsamba 215 mpaka 218 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Tchati patsamba 16, 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

October

607 B.C.E. ← 2,520 zaka → 1914 C.E.

1000 B.C.E. | 1 B.C.E. | 1 C.E. | 1000 C.E. | 2000 C.E.

← 606.25 zaka →← 1,913.75 zaka →

Ufumu wa ku Yerusalemu unawonongedwa

Werengetserani: 606.25 + 1,913.75 = 2,520

Mulungu anaika Yesu kukhala Mfumu yolamulira mitundu yonse