Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo

ANA AZAKA ZOSAPITIRIRA ZITATU

Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo

Kalebe wamva zoti mnzake akudwala.

Iye akuti: “Ndadziwa chochita.

Ndimulembera kalata kuti ndimulimbikitse,  ndipo kenako ndikam’patsa.”

Muzisonyeza ena chifundo ndipo nonse mudzakhala osangalala. 1 Petulo 3:8

ZOTI MAKOLO ACHITE

Muuzeni mwana wanuyo kuti aloze:

Nyumba

Tebulo

Kalebe

Dzuwa

Mbalame

Mtengo

Tchulani munthu amene akudwala ndipo kambiranani ndi mwanayo mmene mungamulimbikitsire.