Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

 Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chomwe munthu wina wa ku Scotland anaona kuti n’chaphindu komanso chofunika kwambiri kuposa bizinezi yapamwamba imene anali nayo? Nanga n’chiyani chinathandiza munthu wina wa ku Brazil kuti asiye khalidwe lachiwerewere komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo? Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wina wa ku Slovenia kusiya khalidwe lake lomwa mowa mwauchidakwa? Werengani nkhanizi kuti mumve zimene anthu amenewa ananena.

“Zinthu zinkaoneka ngati zikundiyendera bwino.”​—JOHN RICKETTS

CHAKA CHOBADWA: 1958

DZIKO: SCOTLAND

POYAMBA: NDINALI NDI BIZINEZI IMENE INKANDIYENDERA BWINO KWAMBIRI

KALE LANGA: Ndinakulira m’banja lopeza bwino. Bambo anga anali ndi udindo m’gulu la asilikali a dziko la Britain choncho banja lathu linkasamukasamuka. Kuwonjezera pa dziko la Scotland, tinakhalanso ku England, Germany, Kenya, Malaysia, Ireland, komanso ku Cyprus. Kuyambira ndili ndi zaka 8, ndinkaphunzira sukulu zogonera komweko za m’dziko la Scotland. Kenako ndinamaliza maphunziro anga ku yunivesite ya Cambridge.

Ndili ndi zaka 20 ndinayamba ntchito pakampani ina yogulitsa mafuta ndipo ndinagwira ntchito imeneyi kwa zaka 8. Poyamba ndinkagwirira ntchito ku South America, kenako ku Africa, ndipo pamapeto pake ku Western Australia. Nditabwerera ku Australia, ndinakhazikitsa kampani yangayanga ndipo kenako ndinaigulitsa.

Ndalama zimene ndinapeza nditagulitsa kampaniyi zinachititsa kuti ndipume pa ntchito ndili ndi zaka 40. Popeza sindinkagwira ntchito, ndinkagwiritsa ntchito nthawi yanga kuyenda m’madera osiyanasiyana. Ndinayenda pa njinga yamoto kuzungulira dziko la Australia maulendo awiri komanso ndinayendapo kuzungulira dziko lonse lapansi. Pa nthawiyi zinthu zinkaoneka ngati zikundiyendera bwino.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Kuyambira pa nthawi imene ndinali pa ntchito, ndinkafuna nditapeza njira yothokozera Mulungu chifukwa cha moyo wabwino umene ndinali nawo. Choncho ndinayamba kupita kutchalitchi cha Anglican chimene ndinkapita ndili mwana. Koma zinthu zambiri zimene ankaphunzitsa kutchalitchichi sizinkachokera m’Baibulo. Kenako ndinayamba kuphunzitsidwa ndi anthu achipembedzo cha Mormon koma ndinalibe chidwi kwenikweni chifukwa ziphunzitso zawo sankazitenga m’Baibulo.

Tsiku lina a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu. Nditangocheza nawo kanthawi kochepa, ndinaona kuti zonse zimene amaphunzitsa zimachokera m’Baibulo. Lemba lina limene anandisonyeza linali la 1 Timoteyo 2:3, 4. Lembali limanena kuti cholinga cha Mulungu n’choti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti a Mboni za Yehova samangothandiza anthu kuti adziwe zinthu, koma amafuna kuti anthuwo adziwe zinthuzo molondola malinga ndi zimene Baibulo limanena.

Kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kunandithandiza kuti ndidziwe zolondola. Mwachitsanzo,  ndinaphunzira kuti Mulungu ndi Yesu sali mbali ya Utatu wosamvetsetseka, koma kuti iwo ndi munthu payekhapayekha. (Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3) Ndinasangalala kwambiri nditaphunzira mfundo yosavuta kumva imeneyi. Komanso ndinakhumudwa n’tazindikira kuti ndakhala ndikuwononga nthawi yanga poyesetsa kuti ndimvetse chiphunzitso cha Utatu chomwe n’chosamvetsetseka.

Pasanapite nthawi ndinayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Anthu amenewa anali aubwenzi kwambiri komanso anali amakhalidwe abwino ndipo zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. Chikondi chenicheni chimene anthu amenewa anali nacho chinandipangitsa kukhulupirira kuti ndapeza chipembedzo choona.​—Yohane 13:35.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nditabatizidwa ndinakumana ndi mtsikana wina wokongola dzina lake Diane. Iye anakulira m’banja la Mboni za Yehova ndipo anali ndi makhalidwe abwino ambiri amene anandisangalatsa. Patapita nthawi tinakwatirana. Kukwatirana ndi Diane komanso thandizo limene ankandipatsa ndinaziona kuti ndi dalitso lochokera kwa Yehova.

Ine ndi Diane tinkafunitsitsa kukatumikira kumene kunkafunikira olalikira ambiri a uthenga wabwino wa m’Baibulo. Choncho, m’chaka cha 2010, tinasamukira ku Belize, ku Central America. M’dziko limeneli timakumana ndi anthu amene amakonda Mulungu ndipo ali ndi ludzu la choonadi cha m’Baibulo.

Panopo ndili ndi mtendere wa m’maganizo chifukwa chodziwa choonadi chonena za Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo. Popeza tsopano ndimalalikira nthawi zonse, ndakhala ndi mwayi wophunzitsa Baibulo kwa anthu ena ambiri. Palibe chinthu chosangalatsa kuposa kuona anthu akusintha moyo wawo chifukwa chophunzira Baibulo ngati mmene inenso ndinasinthira. Tsopano ndazindikira kuti kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo ndi njira yabwino imene ndingathokozere Mulungu chifukwa cha moyo wabwino umene ndili nawo.

“Anandikomera mtima kwambiri.”​MAURÍCIO ARAÚJO

CHAKA CHOBADWA: 1967

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: NDINALI NDI KHALIDWE LACHIWEREWERE

KALE LANGA: Ndinakulira m’tauni yaing’ono yotchedwa Avaré, imene ili m’chigawo cha São Paulo. Anthu ambiri a m’tauniyi ndi osauka.

Bambo anga anamwalira pamene mayi anga anali ndi pakati pa ineyo. Ndili mnyamata ndinkavala zovala za mayi anga akachokapo. Ndinayamba kuchita zinthu ngati mkazi ndipo anthu ankandiyesa kuti ndili m’gulu la anthu amene amagonana ndi amuna anzawo. Patapita nthawi, ndinayamba kugonana ndi anyamata anzanga komanso azibambo.

Nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20, nthawi zambiri ndinkafunafuna anthu oti ndizigonana nawo (amuna ndi akazi omwe). Choncho ndinayamba kupita kulikonse kumene ndingapeze anthuwo, monga m’mabala kapena m’matchalitchi. Pa nthawi ya zikondwerero ndinkavala ngati mzimayi n’kumavina magule. Zimenezi zinachititsa kuti nditchuke kwambiri.

Ena mwa anthu amene ndinkakonda kucheza nawo anali mahule, anthu okonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, komanso amuna omwe amagonana ndi amuna anzawo. Anthu amenewa anachititsa kuti ndiyambe kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo pasanapite nthawi, ndinayamba kugwiritsa ntchito kwambiri mankhwalawa. Nthawi zina tinkasuta usiku wonse. Masiku ena ndinkakhala ndekhandekha tsiku lonse n’kumasuta  mankhwala osokoneza bongo. Ndinaonda kwambiri moti anthu anayamba kufalitsa mphekesera zoti ndili ndi edzi.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Pa nthawiyi ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anandikomera mtima kwambiri. Limodzi mwa mavesi a m’Baibulo amene anandiwerengera linali la Aroma 10:13, lomwe limati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Mawu amenewa anandithandiza kudziwa kufunika kogwiritsira ntchito dzina la Yehova. Nthawi zambiri, pambuyo posuta mankhwala osokoneza bongo usiku wonse, ndinkatsegula windo n’kuyang’ana kumwamba ndipo ndinkapemphera uku ndikulira kuti Yehova andithandize.

Mayi anga ankadandaula kwambiri chifukwa ankaona kuti ndikuwononga moyo wanga ndi mankhwala osokoneza bongo. Chifukwa cha zimenezi ndinaganiza zosiya kugwiritsira ntchito mankhwalawo. Pasanapite nthawi ndinavomera kuti a Mboni za Yehova aziphunzira nane Baibulo. Iwo ananditsimikizira kuti kuphunzira Baibulo kundithandiza kusiya kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndipo kunandithandizadi.

Pamene ndinkapitiriza kuphunzira Baibulo ndinazindikira kuti ndiyenera kusintha khalidwe langa. Kunali kovuta kwambiri kuti ndisiye khalidwe logonana ndi amuna anzanga chifukwa ndinakhala ndikuchita zimenezi kuyambira ndili wamng’ono. Chinthu chimodzi chimene chinandithandiza chinali kusiya zinthu zonse zimene zinkapangitsa kuti ndizichita khalidweli. Ndinasiya kucheza ndi anzanga akale komanso ndinasiya kupita kumabala.

Ngakhale kuti zinali zovuta kwambiri kuti ndisinthe, ndinalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amandikonda ndipo akumvetsa mmene ndikuvutikira kuti ndisinthe. (1 Yohane 3:19, 20) Pofika m’chaka cha 2002 n’kuti nditasiyiratu zogonana ndi amuna anzanga ndipo m’chaka chomwechi ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Mayi anga anasangalala kwambiri chifukwa cha mmene ndinasinthira moti nawonso anayamba kuphunzira Baibulo. Chomvetsa chisoni n’chakuti pasanapite nthawi anadwala matenda opha ziwalo. Komabe, iwo anapitiriza kukonda Yehova ndiponso choonadi cha m’Baibulo.

Patha zaka 8 tsopano ndikugwira ntchito yolalikira nthawi zonse ndipo ndimagwiritsa ntchito nthawi yanga kuphunzitsa anthu ena Baibulo. Komabe nthawi zina ndimalimbana ndi maganizo olakalaka zoipa zimene ndinkachita poyamba. Ngakhale zili choncho, ndimalimbikitsidwa kudziwa kuti ndikapanda kuchita zoipazo, Yehova amasangalala nane.

Kuyandikira kwa Yehova komanso kuchita zinthu zimene amasangalala nazo, kwachititsa kuti ndisamadzione ngati wosafunikira. Panopa ndine munthu wosangalala kwambiri.

“Ndinali mbiyang’ambe.”​—LUKA ŠUC

CHAKA CHOBADWA: 1975

DZIKO: SLOVENIA

POYAMBA: NDINKAMWA MOWA MWAUCHIDAKWA

KALE LANGA: Ndinabadwira mumzinda wa Ljubljana, womwe ndi likulu la dziko la Slovenia. Ndinkakula mosangalala kufikira pamene bambo anga anadzipha ndili ndi zaka 4. Zimenezi zitachitika, amayi anga ankavutika kuti apeze ndalama zosamalirira ineyo ndi mchimwene wanga.

Nditafika zaka 15, ndinayamba kukhala ndi agogo anga aakazi. Ndinkasangalala kukhala ndi agogo angawo chifukwa anzanga ambiri ankakhala kufupi ndi kumene iwowo ankakhala. Komanso kumeneku ndinkakhala  mwaufulu kusiyana ndi mmene ndimakhalira ndi amayi. Ndili ndi zaka 16, ndinayamba kucheza ndi anthu amene ankakonda kumwa mowa Loweruka ndi Lamlungu. Komanso ndinayamba kusunga tsitsi, kuvala mosonyeza kuti ndine munthu wovuta, ndipo kenako ndinayamba kusuta.

Ngakhale kuti ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osiyanasiyana osokoneza bongo, koma kwenikweni ndinkakonda kumwa mowa chifukwa ndi umene unkandikomera kwambiri. Kenako ndinayamba kumwa mowa kwambiri. Ndinali ndi luso lochita zinthu ngati sindinaledzere moti nthawi zambiri anthu ankangodziwa kuti ndamwa mowa chifukwa cha fungo. Ngakhale pa nthawiyi, palibe ankadziwa kuti ndinkakhala nditamwa mowa wambirimbiri, kuphatikizapo mowa wamphamvu kwambiri.

Tikamachokera ku dansi, koti tachezera usiku wonse, nthawi zambiri ineyo ndi amene ndinkathandiza anzangawo kuti azitha kuyenda ngakhale kuti kawirikawiri ineyo ndinkakhala nditamwa mowa wambiri kuposa iwowo. Tsiku lina ndinamva mnzanga wina akulankhula ndi munthu wina za ineyo ndipo anandipatsa dzina linalake lachipongwe la m’Chisiloveniya limene limatanthauza mbiyang’ambe. Zimene ananenazo zinandikhumudwitsa kwambiri.

Ndinayamba kuganizira zimene ndinkachita pa moyo wanga ndipo ndinayamba kuona kuti moyo wanga ulibe phindu. Ndinkaona kuti palibe chaphindu chilichonse chimene ndinkachita pa moyo wanga.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Pa nthawiyi ndinaona kuti mnzanga wina amene ndinaphunzira naye sukulu anali atasintha khalidwe lake. Ndinkafunitsitsa kudziwa chimene chinamuthandiza kuti asinthe, choncho ndinam’tengera kumalo ena odyera kuti ndikacheze naye. Tikucheza, iye anandiuza kuti anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anandifotokozera zina mwa zinthu zimene ankaphunzira. Zonse zimene anandifotokozera zinali zachilendo kwa ine chifukwa ndinali ndisanakhalepo m’chipembedzo chilichonse. Kenako ndinayamba kusonkhana komanso kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kudziwa mfundo zambiri zothandiza. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti tikukhala nthawi imene Baibulo limati ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Ndinaphunziranso kuti posachedwapa Mulungu adzawononga anthu onse oipa ndipo anthu abwino adzawapatsa mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. (Salimo 37:29) Ndinkafunitsitsa kusiya makhalidwe anga oipa n’cholinga choti ndikhale m’gulu la anthu abwinowo.

Ndinayamba kuuzako anzanga choonadi cha m’Baibulo chimene ndinkaphunzira. Anzanga ambiri ankandiseka ndikamawafotokozera zimene ndinkaphunzirazo, koma zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti iwo sanali anzanga abwino. Ndinayamba kuona kuti anthu amene ndinkacheza nawo ndi amenenso ankachititsa kuti ndizimwa mowa kwambiri. Iwo nthawi zonse ankangodikira kuti mapeto a mlungu afike n’cholinga choti akaledzerenso.

Ndinasiya kucheza ndi anthu amenewa ndipo ndinayamba kucheza ndi a Mboni za Yehova chifukwa ndi amene ankandilimbikitsa. Kucheza ndi anthu amenewa kunandithandiza chifukwa iwo amakonda kwambiri Mulungu ndipo amayesetsa kutsatira malamulo ake. M’kupita kwa nthawi, ndinasiya chizolowezi chomwa mowa mwauchidakwa chija.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndikuyamikira Yehova chifukwa masiku ano ndimakhala wosangalala ngakhale ndisamwe mowa. Sindikudziwa kuti chikanandichitikira n’chiyani ndikanakhala kuti sindinasinthe khalidwe langa. Koma panopa ndikuona kuti ndili ndi moyo wosangalala kuposa kale.

Tsopano ndatha zaka 7 ndikutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la Slovenia. Kudziwa Yehova ndiponso kumutumikira kwandithandiza kukhala ndi moyo wabwino.