Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Yandikirani Mulungu

Amapereka Mphoto kwa Onse Omwe Amamutumikira

Amapereka Mphoto kwa Onse Omwe Amamutumikira

MUNTHU aliyense amasangalala akauzidwa mawu oyamikira zinthu zabwino zimene wachita kapena mphatso imene wapereka kuchokera pansi pa mtima. Aliyense amafuna kuyamikiridwa pa zinthu zimene wayesetsa kuchita. Makamaka timafuna kuyamikiridwa ndi anthu amene timawakonda. Ndipotu Yehova Mulungu ndi amene timamukonda kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Koma kodi iye amayamikira zimene timachita pomutumikira? Tiyeni tione zimene Mulungu anachitira Ebedi-meleki amene analolera kuika moyo wake pa ngozi n’cholinga choti apulumutse mneneri wa Mulungu.​—Werengani Yeremiya 38:7-13; 39:16-18.

Kodi Ebedi-meleki anali ndani? Iye anali nduna m’nyumba ya Mfumu Zedekiya ya Yuda. Ebedi-meleki anakhala ndi moyo mu nthawi ya Yeremiya, amene Mulungu anamutuma kuti achenjeze a Yuda osakhulupirika za chiwonongeko chimene chinali kubwera. Ngakhale kuti Ebedi-meleki ankakhala pakati pa akalonga osaopa Mulungu, iye ankaopa Mulungu ndipo ankalemekeza kwambiri Yeremiya. Akalonga oipawo ananamizira Yeremiya kuti ndi woukira ndipo anamuponya m’chitsime chamatope kuti afe. (Yeremiya 38:4-6) Popeza Ebedi-meleki anali munthu woopa Mulungu, kodi iye akanachita chiyani pamenepa?

Ebedi-meleki anachita zinthu molimba mtima komanso mosazengereza ndipo sanaope zimene akalonga aja akanamuchitira. Iye anapita kwa Zedekiya ndipo anamuuza zinthu zoipa zimene akalongawo anachitira Yeremiya. Mwina iye analoza akalongawo pamene ankauza mfumuyo kuti: “Anthu awa achitira mneneri Yeremiya . . . zoipa.” (Yeremiya 38:9) Mfumu Zedekiya inaona kuti zimene Ebedi-meleki ananena zinali zoona ndipo inalamula kuti iye apite ndi amuna okwanira 30 kukatulutsa Yeremiya m’chitsimemo.

Ebedi-meleki anasonyezanso khalidwe lina labwino kwambiri lomwe ndi kukoma mtima. Iye anatenga “nsanza ndi zidutswa zotha ntchito zansalu. Zimenezi anazitsitsira . . . kwa Yeremiya pogwiritsa ntchito zingwe.” Kodi n’chifukwa chiyani iye anatenga nsanza ndi zidutswa zansalu? Anaona kuti zinthu zimenezi zithandiza kuti Yeremiya asamve ululu m’khwapa mwake akamamukoka kumuchotsa m’matope omwe anali m’chitsimecho.​—Yeremiya 38:11-13.

Yehova anaona zimene Ebedi-meleki anachita ndipo anayamikira. Kudzera mwa Yeremiya, Mulungu anauza Ebedi-meleki kuti mzinda wa Yuda unali utatsala pang’ono kuwonongedwa. Ndiyeno Mulungu anauza Ebedi-meleki kuti adzamupulumutsa ndipo pofuna kutsimikizira kuti adzachitadi zimenezi anamulonjeza zinthu zisanu. Iye anati: “Ndidzakulanditsa . . . Sudzaperekedwa m’manja mwa anthu . . . Ndidzakupulumutsa ndithu . . . Sudzaphedwa ndi lupanga . . . Udzapulumutsa moyo wako.” Kodi n’chifukwa chiyani Yehova analonjeza Ebedi-meleki kuti amuteteza? Yehova anauza Ebedi-meleki kuti: “Chifukwa chakuti wandikhulupirira.” (Yeremiya 39:16-18) Yehova anadziwa kuti sikuti Ebedi-meleki anangopulumutsa Yeremiya chifukwa chomumvera chisoni koma chinalinso chifukwa choti ankakhulupirira Mulungu.

Pamenepatu tikuphunzirapo kuti Yehova amayamikira zimene timachita pomutumikira. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova amakumbukira ngakhale zinthu zochepa zimene tingachite pa kulambira kwathu zosonyeza kuti timamukhulupirira ndi mtima wonse. (Maliko 12:41-44) Kodi mukufuna mutakhala pa ubwenzi ndi Mulungu woyamikirayu? Ngati ndi choncho, tsimikizirani kuti Mawu ake amanena zoona kuti iye “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”​—Aheberi 11:6.

Mavesi amene mungawerenge mu May:

Yeremiya 32-50