Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Akhristu a M’nthawi ya Atumwi Ankachita Nawo Ndale?

Kodi Akhristu a M’nthawi ya Atumwi Ankachita Nawo Ndale?

▪ Yesu asanabwerere kumwamba, anapereka malangizo omveka bwino kwa ophunzira ake okhudza mmene ayenera kuchitira utumiki wawo, koma iye sanapereke malangizo alionse okhudza ndale. (Mateyu 28:18-20) Choncho, ophunzira a Yesu anapitiriza kutsatira mfundo imene iye anali atanena m’mbuyomo yakuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”​—Maliko 12:17.

Kodi mfundo imene Yesu ananenayi inathandiza bwanji otsatira ake kuti asakhale mbali ya dziko ngakhale kuti iwo ankakhala m’dziko lomweli? Nanga kodi iwo ankadziwa bwanji kuti zinthu izi n’zoyenera kuperekedwa kwa Mulungu ndipo izi n’zoyenera kupita kwa Kaisara, kapena kuti boma?

Mtumwi Paulo ankaona kuti kulowerera ndale ndi kudumpha malire ndipo n’kosagwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa. Buku lina linanena kuti: “Popeza Paulo anali nzika ya Roma, iye anagwiritsa ntchito mwayi umenewu kupempha kuti malamulo a boma amuteteze koma iye sanachite chilichonse chosonyeza kuchemerera malamulowo.”​—Beyond Good Intentions​—A Biblical View of Politics.

Kodi Paulo anapereka malangizo otani kwa Akhristu anzake? Bukuli linanenanso kuti: “Makalata amene iye analembera okhulupirira omwe ankakhala m’mizinda ikuluikulu monga Korinto, Efeso komanso ngakhale Roma, sanatchulemo chilichonse chokhudza ndale.” Buku lomweli linanenanso kuti Paulo “ankalimbikitsa anthu kugonjera boma koma m’makalata ake onse iye sanatchulemo ngakhale pang’ono zoti mpingo uzipereka maganizo kwa anthu olamulira onena za mmene boma liyenera kuyendera.”​—Aroma 12:18; 13:1, 5-7.

Akhristu amene anakhalako patatha zaka zambiri kuchokera pamene Paulo anamwalira anapitirizabe kutsatira malangizo onena za zinthu zimene anayenera kupereka kwa Mulungu ndi zinthu zimene anayenera kupereka ku boma. Iwo ankalemekeza olamulira komabe ankapewa kulowerera nkhani zandale. Ponena za okhulupirira amenewa, buku lija linanena kuti: “Akhristu oyambirira ankadziwa kuti anali ndi udindo wolemekeza akuluakulu a boma, komabe iwo sankakhulupirira kuti ayenera kulowerera nkhani zandale.”

Koma zinthu zinasintha patadutsa zaka pafupifupi 300 kuchokera pamene Yesu anafa. Katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu, dzina lake Charles Villa-Vicencio, anati: “Pamene Constantine anasintha zinthu m’boma, Akhristu ambiri anayamba kugwira ntchito za boma, kulowa usilikali komanso kukhala m’maudindo osiyanasiyana a ndale.” (Between Christ and Caesar) Kodi zotsatira za zimenezi zinali zotani? Pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 300 C.E., chipembedzo chosakanikirana ndi ndalechi n’chimene chinakhala chovomerezeka mu Ufumu wa Roma.

Masiku ano zipembedzo zambiri zimene zimati zimatsatira Khristu zimalimbikitsa otsatira awo kuti azichita ndale. Koma zipembedzo zimenezi sizitsatira zimene Khristu anaphunzitsa ndiponso sizitengera chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi.