Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Mayankho

Kufunafuna Mayankho

Kufunafuna Mayankho

“Pafupifupi munthu aliyense ali ndi maganizo akeake ponena za [Yesu]. Kaya timakhulupirira Yesu kapena ayi, tonsefe timadzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu ndi ndani?’”​—STAN GUTHRIE, WOLEMBA MABUKU.

ANTHU ambiri amafuna kudziwa za Yesu. Mabuku onena za iye amayenda malonda. Komanso mafilimu onena za Yesu amapezeka paliponse. Komabe anthu ali ndi mafunso ambirimbiri onena za Yesu ndipo ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani yoti iye anali ndani.

Zaka zingapo zapitazi, atolankhani awiri anapempha anthu kuti ayankhe kudzera pa Intaneti funso lakuti, “Kodi Yesu anali ndani?” Ena mwa mayankho amene anthu analemba anali awa:

● “N’kutheka kuti anali rabi (mphunzitsi) amene ankakonda anthu n’cholinga choti anthuwo atengere chitsanzo chake.”

● “Anali munthu wamba koma ankakhala moyo wosiyana ndi wina aliyense.”

● “Palibe umboni uliwonse woti Yesu anakhalakodi padziko lapansili.”

● “Yesu ndi Mwana wa Mulungu yemwe anabadwa, kufa ndi kuukitsidwa n’cholinga chakuti atipulumutse ku machimo athu. Panopa Iye ali moyo ndipo adzabweranso padziko lapansili.”

● “Ndimakhulupirira kuti Yesu Khristu ndi mwana yekhayo wa Mulungu ndipo iye ndi munthu komanso mulungu.”

● “Nkhani zonena za Yesu si zenizeni koma ndi nthano za ana.”

Popeza pali maganizo osiyanasiyana, n’zoonekeratu kuti maganizo onsewa sangakhale olondola. Ndiye kodi n’kuti kumene tingapeze mayankho olondola a mafunso onena za Yesu? Amene amafalitsa magazini ino amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo ndi lokhalo limene lingatiuze zoona pa nkhani ya Yesu. *​—2 Timoteyo 3:16.

M’nkhani yotsatira tikambirana mayankho a m’Baibulo a mafunso omwe anthu ambiri amakonda kufunsa onena za Yesu. Yesu ananena kuti “aliyense wokhulupirira iye” ali ndi mwayi wodzapulumuka. (Yohane 3:16) Tikukupemphani kuti muwerenge bwinobwino mayankho a mafunso amene ali m’nkhaniyi ndipo kenako musankhe ngati mukufuna kuphunzira zambiri ponena za Yesu komanso zimene mungachite kuti muzimukhulupirira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 2 wakuti, “Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.