Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

 Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza munthu wina amene ananyalanyaza mfundo za m’Mawu a Mulungu zimene makolo ake anamuphunzitsa kuyambira ali mwana kuti ayambirenso kuzitsatira? Kodi mnyamata wina anapeza bwanji bambo wachikondi amene ankalakalaka kuyambira ali mwana? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthu amenewa ananena.

“Ndinazindikira kuti ndiyenera kubwerera kwa Yehova.”​—ELIE KHALIL

CHAKA CHOBADWA: 1976

DZIKO: CYPRUS

POYAMBA: NDINALI MWANA WOLOWERERA

KALE LANGA: Ndinabadwira ku Cyprus koma ndinakulira ku Australia. Makolo anga ndi a Mboni za Yehova ndipo ndili mwana anayesetsa kundiphunzitsa kuti ndizikonda Yehova komanso Mawu ake, Baibulo. Koma nditangopitirira zaka 13, ndinayamba kudana ndi zimene makolo anga ankandiphunzitsa. Ndinkazemba usiku n’kupita kukakumana ndi anzanga ndipo tinkakaba magalimoto. Zimenezi zinkatibweretsera mavuto ambiri.

Poyamba, ndinkachita zimenezi mobisa poopa kukhumudwitsa makolo anga. Koma kenako mantha anandithera. Ndinayamba kucheza ndi anthu aakulu kuposa msinkhu wanga ndipo chifukwa choti anali osakonda Yehova, ndinayamba kuchita zoipa. Kenako ndinawafotokozera makolo anga kuti ndaleka chipembedzo chawo. Iwo anayesetsa kundithandiza mwachikondi koma sindinamvere. Zimenezi zinawakhumudwitsa kwambiri.

Nditachoka pakhomo pa makolo anga, ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Komanso ndinkalima ndi kugulitsa chamba. Ndinayamba kuchita zachiwerewere komanso nthawi zambiri ndinkakhala m’mabala. Ndinkapsa mtima msanga moti munthu akalankhula kapena kuchita zinthu zimene sindinagwirizane nazo, ndinkalusa kwambiri ndipo nthawi zina ndinkamulalatira mwinanso mpaka kumumenya. Mwachidule ndingati ndinkachita zonse zimene ndinaphunzira kuti Mkhristu sayenera kuchita.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndinayamba kucheza ndi mnyamata wina yemwenso ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Bambo ake a mnyamatayu anamwalira iye ali wamng’ono. Nthawi zambiri tinkacheza mpaka usiku ndipo nthawi zina iye ankamasuka n’kumafotokoza kuti amawasowa kwambiri bambo ake. Popeza ndili mwana ndinaphunzira zoti akufa adzauka, ndinapezeka kuti ndayamba kumufotokozera kuti Yesu anaukitsa anthu akufa ndipo analonjeza kuti m’tsogolo adzaukitsanso anthu akufa. (Yohane 5:28, 29) Ndinamufunsa kuti: “Kodi ungamve bwanji utaonananso ndi bambo ako? Tonse tikhoza kudzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansi.” Mfundo zimenezi zinam’gwira mtima kwambiri.

Nthawi zina mnzangayo ankayambitsa nkhani zokhudza masiku otsiriza komanso zokhudza chiphunzitso  cha Utatu. Ndinkagwiritsa ntchito Baibulo lake n’kumusonyeza malemba osiyanasiyana amene amasonyeza zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu, Yesu, komanso masiku otsiriza. (Yohane 14:28; 2 Timoteyo 3:1-5) Ndikamakambirana ndi mnzangayu zokhudza Yehova, m’pamenenso ndinkaganizira kwambiri za Yehova.

Pang’ono ndi pang’ono mbewu za choonadi cha m’Baibulo zimene makolo anga anabzala mu mtima mwanga zinayamba kukula. Mwachitsanzo, nthawi zina ndikamacheza ndi anzanga n’kumagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, mwadzidzidzi ndinkayamba kuganiza za Yehova. Anzanga ambiri ankanena kuti amakonda Mulungu, koma zochita zawo sizinkagwirizana ndi zimene ankanenazo. Popeza sindinkafuna kukhala ngati iwowo, ndinayamba kuona kuti ndiyenera kubwerera kwa Yehova.

Komabe, kudziwa zoyenera kuchita n’kosiyana ndi kuchitadi zinthuzo. Panali zinthu zina zomwe sizinandivute kusiya, monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kucheza ndi anzanga akale. Kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni wina yemwe anali mkulu.

Koma panali zinthu zina zomwe zinandivuta kwambiri kusiya. Mwachitsanzo, zinkandivuta kuti ndisiye kupsa mtima msanga. Nthawi zina ndinkayesetsa kuugwira mtima koma kenako ndinkapezeka kuti ndayambiranso khalidwe lopsa mtima lija. Zikatere ndinkamva udyo ndipo ndinkadziona kuti ndine wolephera. Zoterezi zinkandikhumudwitsa ndipo ndinkapita kwa mkulu amene ankandiphunzitsa Baibulo uja. Mkuluyu ankaleza nane mtima ndiponso ankandilimbikitsa kwambiri. Nthawi ina anandiuza kuti ndiwerenge nkhani ina ya mu Nsanja ya Olonda yomwe imanena za kufunika kosataya mtima. * Tinakambirana zimene ndingachite ndikapsa mtima. Kenako chifukwa choganizira mfundo zimene zili mu nkhani imeneyi komanso chifukwa chopemphera kwa Yehova, ndinayamba kutha kuugwira mtima. Ndiyeno mu April chaka cha 2000 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo makolo anga anasangalala kwambiri.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Tsopano ndili ndi mtendere wa maganizo komanso chikumbumtima chabwino chifukwa ndimadziwa kuti ndinasiya kuipitsa thupi langa ndi mankhwala osokoneza bongo ndiponso chiwerewere. Panopa ndimakhala osangalala kwambiri kuposa kale ndikamagwira ntchito, ndikakhala kumisonkhano yachikhristu komanso ndikamacheza ndi anzanga. Masiku ano moyo ukundikomera kwambiri.

Ndimayamikira kwambiri Yehova chifukwa makolo anga sanatope nane. Ndimaganizanso za mawu a Yesu opezeka palemba la Yohane 6:44 akuti: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” Choncho, ndimayamikira kwambiri kuti Yehova anandikoka kuti ndibwererenso kwa iye.

 “Ndinkalakalaka nditapeza bambo.”​—MARCO ANTONIO ALVAREZ SOTO.

CHAKA CHOBADWA: 1977

DZIKO: CHILE

POYAMBA: NDINKAIMBA NYIMBO ZAPHOKOSO KWAMBIRI KOMANSO ZACHIWAWA

KALE LANGA: Ndinaleredwa ndi mayi anga ku Punta Arenas, mzinda wosangalatsa umene uli kum’mwera kwa dziko la America m’mbali mwa nyanja yotchedwa Strait of Magellan. Makolo anga anasiyana ndili ndi zaka zisanu ndipo izi zinachititsa kuti ndiziona ngati ndilibe bambo.

Mayi anga ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo ankanditenga kupita ku misonkhano yachikhristu ku Nyumba ya Ufumu. Komabe sindinkasangalala nazo ndipo nthawi zambiri tikamapita ku misonkhanoko ndinkavuta chifukwa ndinkafuna kubwerera. Ndili ndi zaka 13 ndinasiyiratu kupita ku misonkhano.

Ndinayamba kukonda nyimbo ndipo ndinazindikira kuti ndili ndi luso loimba. Nditakwanitsa zaka 15, ndinkaimba nyimbo zaphokoso kwambiri komanso zachiwawa pa maphwando, m’mabala komanso pa zochitika zina. Chifukwa choti ndinkacheza ndi anthu omwe anali ndi luso loimba, ndinayamba kukonda nyimbo za classic. Ndinayamba kuphunzira kuimba pasukulu inayake yophunzitsa kuimba yomwe inali kudera lathu. Ndili ndi zaka 20 ndinapita kumzinda wa Santiago kukapitiriza maphunziro anga a zoimbaimba. Kumeneko ndinapitiriza kuimba ndi magulu oimba nyimbo zaphokoso komanso zachiwawa.

Pa nthawi yonseyi, ndinkangoonabe kuti ndikusoweka chinachake m’moyo mwanga. Poyesa kuthetsa vutoli, ndinkamwa mowa mwauchidakwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndinkachita zimenezi ndi anzanga amene ndinkaimba nawo, omwenso ndinkawatenga ngati abale anga. Maonekedwe anga ankachita kusonyezeratu kuti ndinali munthu wovuta. Ndinkakonda kuvala zovala zamtundu wakuda komanso kusunga ndevu ndi tsitsi moti tsitsi langa linatalika mpaka kutsala pang’ono kufika m’chiuno.

Nthawi zambiri, khalidwe langa linkachititsa kuti ndizimenyana ndi anthu komanso kumangidwa ndi apolisi. Mwachitsanzo, tsiku lina nditaledzera ndinayamba kumenyana ndi gulu lina la anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo amene ankavutitsa gulu lathu. Anthu amenewa anandimenya kwambiri moti mpaka anandithyola nsagwada.

Koma anzanga aja anachita zinthu zondikhumudwitsa kwambiri. Tsiku lina, ndinazindikira kuti mtsikana amene ndinali naye pa chibwenzi analinso pa chibwenzi ndi mnzanga wapamtima ndipo chibwenzi chawocho chinali chitatha zaka zingapo. Ndinakhumudwa kwambiri nditazindikira kuti anzanga onse ankadziwa za nkhaniyi, koma ankandibisira.

Ndinabwereranso ku Punta Arenas ndipo ndinayamba kugwira ntchito yophunzitsa anthu kuimba komanso ndinkaimba chipangizo chinachake chokhala ngati gitala. Ndinapezanso magulu ena amene ndinkaimba ndi kujambula nawo nyimbo. Kenako ndinakumana ndi mtsikana wokongola kwambiri dzina lake Sussan ndipo tinayamba kukhala limodzi. Sussan atazindikira kuti ine sindinkakhulupirira chiphunzitso cha Utatu chimene mayi ake ankakhulupirira anandifunsa kuti: “Nanga zoona ndi ziti?” Ndinamuyankha kuti ndimadziwa kuti chiphunzitso cha Utatu n’chabodza koma sindingathe kumufotokozera umboni wa m’Baibulo. Komabe ndinamuuza kuti a Mboni za Yehova angathe kumufotokozera zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Kenako ndinachita chinthu chomwe ndinali ndisanachitepo pa moyo wanga. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize.

Patangodutsa masiku ochepa, ndinaona munthu wina amene ankaoneka ngati wa Mboni za Yehova ndipo ndinamufunsa ngati analidi wa Mboni. Ngakhale kuti ankaoneka kuti akuchita mantha chifukwa cha mmene ndinkaonekera, iye anayankha mokoma  mtima mafunso anga okhudza misonkhano ya Mboni za Yehova imene imachitika ku Nyumba ya Ufumu. Ndinaona kuti limeneli linali yankho la pemphero langa lija. Ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo ndinakhala mpando wakumbuyo n’cholinga chakuti aliyense asandizindikire. Komabe anthu ambiri anakumbukira kuti nthawi ina ndili mwana, ndinkabwera ku misonkhano ndi mayi anga. Anthuwa anandilandira ndi manja awiri ndipo anandikumbatira mwachikondi. Zimenezi zinandisangalatsa kwambiri ndipo ndinangoona ngati ndabwereranso kunyumba. Nditamuona munthu amene ankandiphunzitsa Baibulo ndili mwana, ndinamupempha kuti ayambirenso kundiphunzitsa.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Tsiku lina ndinawerenga lemba la Miyambo 27:11 limene limati: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.” Ndinachita chidwi kudziwa kuti munthu wamba ngati ine ndingathe kusangalatsa Mlengi wa chilengedwe chonse. Ndinazindikira kuti Yehova ndiye Bambo amene ndakhala ndikufunafuna kuyambira ndili mwana.

Ndinkafuna kusangalatsa Atate wanga wakumwamba komanso kuchita chifuniro chake. Koma kwa zaka zambiri ndinali kapolo wa mankhwala osokoneza bongo komanso mowa. Ndinazindikira kuti mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:24 ndi oona. Lembali limati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Pomwe ndinkayesetsa kuti ndisiye kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa, ndinakumbukira mfundo ya palemba la 1 Akorinto 15:33, lomwe limati: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” Ndinadziwa kuti sindingathe kusiya khalidwe loipa ngati ndingapitirize kucheza ndi anzanga aja komanso kupita nawo kumalo amene tinkapita aja. Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kuzindikira kuti ndiyenera kusiya kuchita zinthu zimene zingandilepheretse kupita patsogolo mwauzimu.​—Mateyu 5:30.

Chifukwa choti ndinkakonda kwambiri nyimbo, zinali zovuta kuti ndisiye kuimba ndi kumvera nyimbo zoipa zija. Koma mothandizidwa ndi anzanga a ku mpingo ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa. Ndinameta tsitsi ndi ndevu zanga komanso ndinasiya kumangovala zovala zamtundu wakuda zokha. Nditamufotokozera Sussan kuti ndikufuna kumeta tsitsi langa, anadabwa kwambiri. Iye anati: “Ndipita nawo ku Nyumba ya Ufumuko kuti ndikaone zimene mumachita.” Iye anasangalala ndi zimene anaona ku Nyumba ya Ufumu ndipo pasanapite nthawi anayamba kuphunzira Baibulo. Kenako ine ndi Sussan tinakwatirana ndipo m’chaka cha 2008 tinabatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova. Panopa tikusangalala kuti tonse limodzi ndi mayi anga tikulambira Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinasiya kucheza ndi anthu oipa ndipo ndapeza chimwemwe chenicheni osati chimene dzikoli limapereka. Panopa ndimakondabe nyimbo koma ndimasankha nyimbo zabwino zoyenera kumvera. Ndimagwiritsa ntchito zimene zinandichitikirazi kuthandiza anthu a m’banja langa ndiponso anthu ena, makamaka achinyamata. Ndimawathandiza kudziwa kuti zinthu zambiri zimene zimaoneka ngati zosangalatsa m’dzikoli, kwenikweni zili ngati “mulu wa zinyalala.”​—Afilipi 3:8.

Ndapeza mabwenzi enieni mu mpingo wachikhristu ndipo anthu amenewa amakondanadi komanso amakhala mwamtendere. Koposa zonse, kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kwandithandiza kupeza Bambo amene ndinkafuna.

[Mawu a M’munsi]

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Yehova anandikoka kuti ndibwererenso kwa iye”