Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zoti Achinyamata Achite

Mose Anapatsidwa Ntchito Yapadera

Mose Anapatsidwa Ntchito Yapadera

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezani kuti inuyo mukuona pamene nkhaniyo ikuchitika. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a mu nkhaniyi akumvera mu mtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Yehova Mulungu ndi Mose

Chidule cha Nkhaniyi: Yehova anatuma Mose kuti akatulutse Aisiraeli ku Iguputo.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI EKISODO 3:1-14; 4:1-17.

Kodi mukuganiza kuti chitsamba chimene chinkayakacho chinkaoneka bwanji? Fotokozani.

․․․․․

Malinga ndi zimene zalembedwa pa Ekisodo 3:4, kodi mukuganiza kuti nkhope ya Mose inkaoneka bwanji pamene anamva Mulungu akulankhula? Nanga pamene ankayankha, mawu ake ankamveka bwanji?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Mose ankamva bwanji mu mtima mwake pamene ankafunsa Yehova mafunso amene ali pa Ekisodo 3:11, 13 komanso chaputala 4:1, 10?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Gwiritsani ntchito zinthu zofufuzira zimene muli nazo kuti mudziwe zambiri zokhudza mawu akuti, “ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” (Ekisodo 3:14) N’chifukwa chiyani Yehova ananena mawu amenewa poyankha funso limene Mose anamufunsa lokhudza dzina Lake? *

․․․․․

 Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Mose ankaopa kukalankhula ndi Farao? (Zokuthandizani: Werengani Numeri 12:3.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Mose ankaopa kulankhula ndi Aisiraeli anzake?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Chizolowezi cha anthu chodzikayikira.

․․․․․

Yehova amakhulupirira kuti mungakwanitse ntchito zimene amakupatsani.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Ndi zinthu ziti zimene mumaona kuti simungakwanitse?

․․․․․

Kodi ndi zinthu ziti zimene mumaona kuti mungakwanitse kuchita potumikira Yehova Mulungu ngakhale kuti simungakwanitse kuchita zinthu zina?

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Mukhoza kukopera kapena kusindikiza nkhaniyi pa Intaneti pa adiresi iyi: www.jw.org/ny.

Ngati Mulibe Baibulo, Uzani a Mboni za Yehova, Kapena Kawerengeni Baibulo pa Adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org/ny.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 A Mboni za Yehova ali ndi mabuku amene angakuthandizeni kufufuza kuti mumvetse bwino nkhani za m’Baibulo. Kuti mudziwe zambiri funsani a Mboni za Yehova kudera lanu kapena lemberani kalata amene amafalitsa magaziniyi.