Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Yandikirani Mulungu

“Ndithandizeni Kubwerera”

“Ndithandizeni Kubwerera”

Kodi pa nthawi ina munkatumikira Yehova? Kodi mumafuna mutayambiranso kumutumikira koma n’kumakayikira ngati angakulandireni? Ngati ndi choncho, werengani mofatsa nkhaniyi komanso inzake imene idzatuluke m’magazini yotsatira. Nkhanizi zalembedwera inuyo.

“NDINAPEMPHERA kwa Yehova kuti andilole kubwereranso kwa iye ndiponso kuti andikhululukire chifukwa chochita zinthu zomukhumudwitsa.” Mawu amenewa ananenedwa ndi mayi wina amene anasiya kutumikira Mulungu ngakhale kuti anaphunzitsidwa mfundo za m’Baibulo kuyambira ali mwana. Kodi mukumva chisoni ndi zimene anachita mayiyu? Kodi munayamba mwaganizira mmene Mulungu amamvera akamaona anthu amene asiya kumutumikira? Kodi iye amawakumbukirabe? Kodi Mulungu amafuna anthu amenewa ‘atabwerera’ kwa iye? Kuti tidziwe mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tikambirane mawu amene Yeremiya analemba. Tikukhulupirira kuti mayankho a mafunsowa akulimbikitsani kwambiri.​—Werengani Yeremiya 31:18-20.

Tiyeni tikambirane chimene chinachititsa Yeremiya kulemba mawu amenewa. Zaka zambiri Yeremiya asanakhalepo, mu 740 B.C.E., Yehova analola kuti ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli ugonjetsedwe ndi Asuri ndipo Aisiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo. * Mulungu analola kuti anthu ake akumane ndi tsoka limeneli ngati chilango chifukwa cha machimo akuluakulu amene ankachita ngakhale kuti anali atachenjezedwa mobwerezabwereza ndi aneneri a Mulungu. (2 Mafumu 17:5-18) Kodi anthuwa anasintha chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo ku ukapolo, pamene anasiyanitsidwa ndi Mulungu wawo komanso anali kutali ndi dziko lawo? Kodi Yehova anangowaiwaliratu basi? Kodi iye akanawalandiranso ngati iwo akanafuna kubwerera kwa iye komanso kudziko lawo?

“Ndinadzimvera Chisoni”

Ali ku ukapolo, anthuwa anazindikira kulakwa kwawo ndipo analapa. Yehova anaona kuti alapadi kuchokera pansi pa mtima ndipo ananena mawu otsatirawa pofotokoza za maganizo amene Aisiraeli anali nawo ali ku ukapolo. Ponena za Aisiraeli onse, iye akungowatchula kuti Efuraimu.

Yehova anati: “Ndamva Efuraimu akudzilirira.” (Vesi 18) Mulungu anamva pamene Aisiraeli ankadandaula chifukwa cha zotsatira za machimo awo. Katswiri wina ananena kuti mawu akuti “akudzilirira” angatanthauze “kupukusa mutu.” Iwo anali ngati mwana wolowerera amene akupukusa mutu wake akaganizira zokhoma zimene wakumana nazo ndipo akulakalaka moyo umene ankakhala poyamba ali kwawo. (Luka 15:11-17) Kodi iwo ankanena kuti chiyani?

“Mwandidzudzula . . . ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa.” (Vesi 18) Aisiraeli anavomereza kuti ankayeneradi kulandira chilango. Ndipotu iwo anali ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa. Buku lina linanena kuti fanizo limeneli lingatanthauze kuti iwo anali ngati ng’ombe yokoka ngolo yomwe “sikanakwapulidwa ikanakhala kuti sinakhotere kosiyana ndi kumene ngoloyo imayenera kupita.”

 “Ndithandizeni kubwerera ndipo ndidzabwereradi, pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.” (Vesi 18) Anthuwa anadzichepetsa ndipo anapempha Mulungu kuti awathandize. Anali ngati anthu osochera ndipo anachonderera Yehova kuti awakhululukire n’kuyambiranso kuwakonda.

“Ndinadzimvera chisoni. . . . Ndinachita manyazi ndipo ndinanyazitsidwa.” (Vesi 19) Anthuwa atazindikira kulakwa kwawo, anadzimvera chisoni. Iwo anavomereza kuti analakwadi ndipo chilango chimene analandira chinawachititsa kudziona kuti ndi onyozeka ndiponso osafunika.​—Luka 15:18, 19, 21.

Aisiraeli analapa mochokera pansi pa mtima moti anamva chisoni chifukwa cha machimo awo ndipo anasiya njira zawo zoipa. Kodi Mulungu anakhudzidwa mtima ndi kulapa kwawoku n’kuwalola kuti abwererenso kwa iye?

“Mosalephera Ndidzamumvera Chisoni”

Yehova ankawakonda kwambiri Aisiraeli. Iye anati: “Ine ndakhala Tate wa Isiraeli, ndipo Efuraimu ndi mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa.” (Yeremiya 31:9) Kodi bambo wachikondi angalephere bwanji kulandira mwana wake woti walapa kuchokera pansi pa mtima? Tiyeni tione mmene Yehova anafotokozera chikondi chimene anali nacho pa anthu ake.

“Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa? Pamlingo umene ndalankhula zomulanga, ndidzakumbukira kumuchitira zabwino pamlingo womwewo.” (Vesi 20) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yehova ankawakonda kwambiri Aisiraeli. Monga kholo lachikondi koma losalekerera ana, Mulungu anaona kuti anayenera ‘kuwalanga’ Aisiraeli. Iye anawachenjeza mobwerezabwereza kuti asiye makhalidwe awo oipa. Koma iwo atakana kusintha, iye analola kuti atengedwe kupita ku ukapolo. Zinakhala ngati kholo lalola kuti mwana wake wosamvera achoke pakhomo. Komabe ngakhale kuti anafunika kuwapatsa chilango, iye sanawaiwale. Monga kholo lachikondi, iye sangaiwale ana ake. Ndiyeno kodi Yehova anamva bwanji ataona kuti Aisiraeli alapa kuchokera pansi pa mtima?

“M’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye. * Mosalephera ndidzamumvera chisoni.” (Vesi 20) Yehova ankafunitsitsa ana ake atabwerera. Iye anakhudzidwa kwambiri ataona kuti ana akewa alapa mochokera pansi pa mtima. Mofanana ndi bambo wa mu fanizo la Yesu la mwana wolowerera, Yehova “anagwidwa chifundo” ndipo anali wofunitsitsa kuwalandiranso.​—Luka 15:20.

‘Yehova Anandilola Kubwerera kwa Iye’

Mawu a palemba la Yeremiya 31:18-20 akutithandiza kumvetsa chikondi komanso chifundo chachikulu chimene Yehova ali nacho. Iye saiwala anthu amene poyamba ankamutumikira. Kodi Yehova amatani anthu oterewa akafuna kubweranso kwa iye? Iye ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Sanganyalanyaze anthu amene alapa ndipo akufuna kubwerera kwa iye. (Salimo 51:17) Choncho iye amakhala wokonzeka kuwalandiranso.​—Luka 15:22-24.

Mayi amene tamutchula koyamba kwa nkhani ino uja anachita zinthu zosonyeza kuti ankafuna kubwerera kwa Yehova. Iye anapita kwa akulu a mpingo wa Mboni za Yehova wa kudera lakwawo. Poyamba anafunika kuthana ndi maganizo olakwika amene anali nawo. Iye anati: “Ndinkadziona kukhala wosafunikira.” Koma akulu a mpingo anamulimbikitsa komanso kumuthandiza kuti akhalenso wolimba mwauzimu. Mayiyo moyamikira anati: “Ndinasangalala kwambiri Yehova atandilola kubwerera kwa iye.”

Ngati pa nthawi inayake munatumikirapo Yehova ndipo mukufuna kuyambiranso kumutumikira, tikukulimbikitsani kuti mupite ku mpingo wa Mboni za Yehova umene uli m’dera lanu. Musaiwale kuti Yehova amasonyeza chifundo kwa munthu amene walapa ndipo akumupempha kuti, “Ndithandizeni kubwerera.”

Mavesi amene mungawerenge mu April:

Yeremiya 17-31

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Zaka zambiri izi zisanachitike, mu 997 B.C.E., Aisiraeli anagawikana n’kukhala maufumu awiri. Ufumu wina unali wakum’mwera wa mafuko awiri wa Yuda. Wachiwiri unali wakumpoto wa mafuko 10 ndipo unkatchedwa Efuraimu, chifukwa fuko limeneli ndi limene linali lalikulu.

^ ndime 6 Pofotokoza zimene ankatanthauza ponena kuti m’mimba mukubwadamuka, buku lina lothandiza anthu omasulira Baibulo linati: “Ayuda ankakhulupirira kuti munthu amakhudzika kuchokera m’mimba.”