Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zokhudza “Mapeto”

Zokhudza “Mapeto”

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zokhudza “Mapeto”

Kodi adzakhala mapeto a chiyani?

Panthawi ina, ophunzira a Yesu anam’funsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” (Mateyo 24:3) Poyankha, Yesu sananene kuti dziko lenilenili ndi limene lidzathe. Ndipotu panthawi ina m’mbuyomo, iye anali atanena za “dongosolo lino la zinthu,” ndipo anagwiritsa ntchito mawu amenewa ponena za dongosolo lonse la zandale, zamalonda ndiponso la zipembedzo, lomwe mwini wake ndi Satana. (Mateyo 13:22, 40, 49) Choncho, pamene Yesu ananena kuti “mapeto adzafika,” ankatanthauza kuti dongosolo limeneli ndi limene lidzathe.​—Mateyo 24:14.

Kodi Yesu ananena kuti mapetowa ndi chiyani?

Yesu anasonyeza kuti nkhani yonena za mapeto a dongosolo loipali ndi “uthenga wabwino.” Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” Ndipo ponena za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anati: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zoona, kupanda kufupikitsa masikuwo, palibe aliyense akanapulumuka.”​—Mateyo 24:14, 21, 22.

Ndani amene adzawonongedwe?

Omwe adzawonongedwe ndi anthu okhawo amene sakonda Yehova komanso Mwana wake. Yesu anati: “Pakuti monga analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. Pakuti m’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu . . . sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo.” (Mateyo 24:36-39) Yesu ananena kuti anthu ambiri ali pa msewu wa kuchiwonongeko. Komabe, iye ananenanso kuti pali ‘msewu wina wolowera ku moyo.’​—Mateyo 7:13, 14.

Kodi dongosolo lino la zinthu lidzatha liti?

Yesu atafunsidwa za chizindikiro cha kukhalapo kwake “ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu,” anayankha kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina, ndiponso kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. . . . Ndipo chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, ochuluka chikondi chawo chidzazirala.” (Mateyo 24:3-12) Motero, zinthu zonse zoipa zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti posachedwapa, boma la Ufumu wa Mulungu libweretsa mtendere kwa anthu onse omvera. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.”​—Luka 21:31.

Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani?

Yesu ananena kuti Mulungu “anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kuti munthu akhulupirire Mulungu ndi Mwana wake, ayenera kuwadziwa bwino awiriwa. N’chifukwa chake Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Choncho samalani kuti mavuto ndiponso nkhawa za pamoyo zisakulepheretseni kuphunzira zimene mungachite kuti muzikonda Mulungu. Yesu anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi . . . nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pa nkhope ya dziko lonse lapansi.” Mukatsatira malangizo amenewa, ‘mudzatha kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika.’​—Luka 21:34-36.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pamutu wakuti, “Kodi ‘Tili M’masiku Otsiriza’?” *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.