Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro N’chiyani?

Kodi Chikhulupiriro N’chiyani?

 Kodi Chikhulupiriro N’chiyani?

KODI inuyo mumaganiza kuti chikhulupiriro n’chiyani? Ena amaganiza kuti kukhala ndi chikhulupiriro kumatanthauza kumangokhulupirira zilizonse. Ndipo pankhani imeneyi, katswiri wina wolemba nkhani wa ku America, yemwenso ndi mtolankhani, dzina lake H. L. Mencken, ananena kuti munthu wachikhulupiriro “amangokhulupirira zilizonse ndi zosatheka zomwe.”

Koma Baibulo limapereka tanthauzo losiyana kwambiri ndi zimenezi. Mawu a Mulungu amati: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”​—Aheberi 11:1.

Popeza kuti anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya chikhulupiriro, tiyeni tikambirane mafunso otsatirawa:

Kodi tanthauzo la m’Baibulo la mawu akuti chikhulupiriro limasiyana bwanji ndi zimene anthu ambiri amaganiza akamva mawuwa?

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chimene Baibulo limafotokoza?

Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba?

Chikhulupiriro Chili Ngati Chikalata Chaumboni

Panthawi yomwe buku la m’Baibulo la Aheberi linkalembedwa, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chiyembekezo chotsimikizika,” ankagwiritsidwa ntchito kawirikawiri. Mawu amenewa nthawi zambiri ankapezeka m’makalata a zamalonda ndipo ankakhala ngati umboni wosonyeza kuti munthu wagula katundu winawake. N’chifukwa chake buku lina limati lemba la Aheberi 11:1 lingalembedwenso kuti: “Chikhulupiriro ndicho chikalata chaumboni wa zinthu zoyembekezeredwa.”

Mwachitsanzo, ngati munagulapo katundu ku kampani inayake kenako n’kumadikirira kuti kampaniyo ikutumizireni katunduyo kunyumba kwanu, ndiye kuti munali ndi chikhulupiriro ngati chimenechi. Simunakayike kuti mulandira katunduyo chifukwa anakupatsani lisiti lotsimikizira kuti mwaguladi katunduyo. Pamenepa, tinganene kuti lisitilo linali ngati chikalata chaumboni chotsimikizira kuti mulandira katundu wanuyo. Koma ngati lisitilo likanasokonekera kapena kutayika, ndiye kuti simukanakhala ndi umboni wotsimikizira kuti katunduyo ndi wanudi. Mofanana ndi zimenezi, anthu amene ali ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzakwaniritsadi malonjezo ake, sakayika kuti adzalandiradi malonjezowo. Koma anthu omwe alibe chikhulupiriro kapena omwe chikhulupiriro chawo chinatha, sadzalandira madalitso amenewa.​—Yakobe 1:5-8.

Mawu otsatira a palemba la Aheberi 11:1, akuti “umboni wooneka,” amatanthauza kupereka umboni wosiyana ndi zimene zikuoneka ngati zenizeni. Mwachitsanzo, dzuwa limaoneka ngati limazungulira dziko lapansi chifukwa chakuti limaoneka ngati likutuluka kum’mawa n’kulowa kumadzulo. Komabe umboni wa akatswiri a sayansi ya zakuthambo ndiponso akatswiri a masamu, umasonyeza kuti dziko ndi limene limazungulira dzuwa, osati dzuwa kuzungulira dziko. Mukadziwa zimenezi ndi kuzivomereza ndiye kuti mungayambe kukhulupirira mfundo imeneyi, ngakhale kuti dzuwa ndi limene limaoneka ngati likuzungulira dziko. Pamenepa sikuti mukungokhulupirira zinthu zopanda umboni kapena chifukwa cha mmene zikuonekera, koma mukukhulupirira zinthuzo chifukwa ndi mmene zililidi.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala ndi Chikhulupiriro Cholimba?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, chomwe tingachipeze ngati tili ndi umboni wamphamvu, ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kusiya zinthu zina zimene timakhulupirira. Kukhala ndi chikhulupiriro chimenechi n’kofunika kwambiri. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Popanda chikhulupiriro n’kosatheka kum’kondweretsa Mulungu. Pakuti amene akum’fikira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amakhala wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.”​—Aheberi 11:6.

Pali zinthu zambiri zimene zingatilepheretse kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe tingakhale ndi chikhulupirirochi tikamatsatira mfundo zinayi zimene zili m’nkhani zotsatirazi.