Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

3 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Yesu

3 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Yesu

 3 Dziwani Zoona Zake Zokhudza Yesu

“Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA ZIMAWAVUTA KUDZIWA ZOONA ZAKE ZOKHUDZA YESU? Anthu ena amatsutsa zoti Yesu anakhalapodi. Ena amavomereza kuti iye analipodi koma amati anali munthu wamba ndipo anamwalira kalekale.

KODI MUNGATANI KUTI MUDZIWE ZOONA ZAKE ZOKHUDZA YESU? Tsatirani chitsanzo cha Natanayeli. * Filipo anauza mnzake Natanayeli kuti wapeza Mesiya, “Yesu, mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.” Komatu Natanayeli sanangokhulupirira zimenezi. Iye anayankha Filipo kuti: “Kodi mu Nazarete mungatuluke kanthu kabwino?” Ngakhale kuti ananena zimenezi, iye anavomera Filipo atamuuza kuti: “Tiye ukaone” wekha. (Yohane 1:43-51) Inunso mukhoza kudziwa zoona zokhudza Yesu ngati mutafufuza nokha umboni wonena za iye. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Fufuzani umboni wotsimikizira kuti Yesu anakhalapodi. Josephus ndi Tacitus anali akatswiri olemba mbiri yakale otchuka kwambiri omwe anakhalapo m’nthawi ya atumwi koma iwo sanali Akhristu. Akatswiriwa analemba nkhani zotsimizikira kuti Yesu anakhalapodi. Tacitus anafotokoza kuti Nero, yemwe anali mfumu ya Roma, ananamizira Akhristu kuti ndi amene anayambitsa moto umene unawononga mzinda wa Roma mu 64 C.E. Iye anafotokoza kuti: “Nero ananamizira Akhristuwo, omwenso anthu ambiri ankawada poganiza kuti anali ochita zoipa kwambiri ndipo ankawazunza zedi. Akhristu anatengera dzinali kwa Khristu, yemwe Pontiyo Pilato, mmodzi mwa olamulira athu, anamulamula kuti azunzidwe ndi kuphedwa mu ulamuliro wa mfumu Tiberiyo.”

Ponena za nkhani zimene akatswiri olemba mbiri yakale analemba zokhudza Yesu ndiponso Akhristu oyambirira, buku lina linati: “Nkhani zolembedwa ndi anthu osiyanasiyana zimenezi zikusonyeza kuti anthu omwe ankadana ndi Akhristu sankakayikira zoti Yesu analipodi. Koma chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700 mpaka kumayambiriro kwa m’ma 1900, anthu anayamba kukayikira zoti Yesu analipodi. Iwo ankachita zimenezi ngakhale kuti analibe umboni wowachititsa kuti ayambe kukayikira.” (Encyclopædia Britannica, 2002 Edition) Poikira ndemanga pa nkhaniyi, mu 2002, nyuzipepala ina ya ku America inati: “Ambiri mwa akatswiri a maphunziro, kupatulapo anthu ochepa amene amati kulibe Mulungu, avomereza kale kuti Yesu wa ku Nazarete anakhalapodi.”​—The Wall Street Journal.

Umboni wotsimikizira kuti Yesu anaukitsidwadi. Yesu atagwidwa ndi adani ake, anzake apamtima  anam’thawa ndipo mnzake wina dzina lake Petulo anakanitsitsa zoti akumudziwa. (Mateyo 26:55, 56, 69-75) Panthawiyi ophunzira ake onse anam’thawa. (Mateyo 26:31) Koma patapita nthawi, ophunzirawa anayamba kulimbikira kwambiri pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino. Kenako, Petulo ndi Yohane analankhula molimba mtima kwambiri pamaso pa anthu omwe anapha Yesu aja. Ophunzira a Yesu analimbikitsidwa kwambiri moti anafalitsa uthenga wabwino m’dera lonse la ufumu wa Aroma. Iwo ankaona kuti ndi bwino kufa m’malo mosiya chikhulupiriro chawo.

Kodi n’chifukwa chiyani ophunzirawa anasintha kwambiri chonchi? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu atauka kwa akufa, “anaonekera kwa Kefa [Petulo], kenako kwa khumi ndi awiri aja.” Paulo anapitiriza kunena kuti: “Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 panthawi imodzi.” Ndipo ambiri mwa anthu omwe anaona Yesu panthawiyi, anali adakali ndi moyo pamene Paulo ankalemba mawuwa. (1 Akorinto 15:3-7) Zikanakhala kuti Yesu anaonekera kwa munthu mmodzi kapena awiri okha, anthu sakanavutika kutsutsa zimenezi. (Luka 24:1-11) Koma umboni wa anthu oposa 500 unali wamphamvu kwambiri moti munthu sakanatha kutsutsa mfundo yoti Yesu anaukitsidwadi.

KODI TIDZAPEZA MADALITSO OTANI? Anthu amene amamvera ndiponso kukhulupirira Yesu, amakhululukidwa machimo awo ndipo amakhala ndi chikumbumtima choyera. (Maliko 2:5-12; 1 Timoteyo 1:19; 1 Petulo 3:16-22) Ngati anthu otere atamwalira, Yesu akulonjeza kuti adzawaukitsa “pa tsiku lomaliza.”​—Yohane 6:40.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * pamutu 4 wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndani,” ndiponso mutu 5, wakuti “Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Zikuoneka kuti Mateyo, Maliko ndi Luka omwe analemba Mauthenga Abwino, anam’tchula Natanayeli ndi dzina lakuti Batolomeyo.

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 7]

Fufuzani umboni wonena za Yesu ngati mmene anachitira Natanayeli