Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Chinsinsi cha Banja Losangalala

Thandizani Ana Anu Achinyamata Kuti Akule Bwino

Thandizani Ana Anu Achinyamata Kuti Akule Bwino

“Kale ndinkalankhulana bwino kwambiri ndi ana anga. Ankamvetsera mwachidwi ndikamalankhula ndipo iwo ankachita zimene ndawauza nthawi yomweyo. Koma masiku ano pamene afika paunyamata, sitigwirizana pachilichonse. Ndipo safuna n’komwe kuti tizichita zinthu zauzimu pabanja pathu. Poyamba, anawa asanafike paunyamata, sindinkaganiza n’komwe kuti iwo angadzasiye kundimvera, ngakhale kuti ndinkaona ana ochokera ku mabanja ena akusiya kumvera makolo awo.”​—Anatero bambo wina dzina lake Reggie. *

KODI muli ndi mwana yemwe akufika paunyamata? Ngati zili choncho, ndiye kuti mukuona kusintha kofunika kwambiri kumene kumachitika mwana akamakula. Komabe, nthawi imeneyi ingakhalenso yovuta kwambiri. Mwachitsanzo kodi zinthu ngati zotsatirazi zimakuchitikirani?

 • Panthawi imene mwana wanu wamwamuna anali wamng’ono, ankakonda kukhala nanu pafupi nthawi zonse. Koma masiku ano pamene wafika paunyamata, safuna n’komwe kukuyandikirani.

 • Pamene mwana wanu wamkazi anali wamng’ono, ankakuuzani chilichonse. Koma masiku ano pamene wafika pazaka zaunyamata, akakhala ndi nkhani inayake, amakauza anzake osati inuyo.

Ngati zinthu zimenezi zikuchitika pabanja panu, musafulumire kuganiza kuti mwana wanuyo wasiyiratu kukumverani. Nangano kodi n’chiyani chikumuchitikira? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione mfundo yofunika kwambiri yokhudza zimene zimachitika mwana akafika paunyamata.

Zaka Zaunyamata N’zofunika Kwambiri Pamoyo Wamunthu

Mwana akabadwa, m’kupita kwanthawi amayamba kuphunzira zinthu zambiri monga kulankhula, kuyenda ndiponso amayamba sukulu. Makolo amasangalala kwambiri mwana wawo akayamba kuchita zimenezi chifukwa amadziwa kuti mwanayo akukula.

Nthawi inanso yosangalatsa kwambiri pamoyo wa mwana ndi pamene wafika paunyamata. Komabe, makolo ena amaona kuti nthawi imeneyi ndi yovuta kwambiri. Ndipotu zimenezi n’zomveka chifukwa palibe makolo amene angakonde kuona mwana wawo akusintha n’kukhala wosamvera ndiponso wosachedwa kukwiya. Ngakhale zili choncho, zaka zaunyamata n’zofunika kwambiri pamoyo wamunthu. N’chifukwa chiyani tikutero?

Baibulo limati m’kupita kwa nthawi “mwamuna adzasiya atate wake ndi amake.” (Genesis 2:24) Motero, zaka zaunyamata zimathandiza kwambiri mwana wanu kukonzekera nthawi yovuta komanso yosangalatsa yomwe adzachoke panyumba panu n’kukakhala payekha. Panthawi imeneyo, mwana wanu angadzathe kunena mawu ngati a mtumwi Paulo akuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.”​—1 Akorinto 13:11.

Choncho tinganene kuti zimenezi n’zimene mwana wanu wachinyamata akuchita. Iye akusiya  zachibwana ndipo akuyamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu yemwe angathe kuchoka panyumba n’kukakhala payekha. Pamfundo yomweyi, buku lina limati nthawi yaunyamata ndi nthawi imene mwana amakonzekera kukaima payekha.

Komabe, makolo amada nkhawa kwambiri akaganiza zoti tsiku lina mwana wawo adzachoka n’kukakhala payekha. Mwina makolowo angadzifunse kuti:

 • “Ngati mwana wanga akulephera kusamalira chipinda chake, kodi adzakwanitsa kukhala ndi nyumba yakeyake n’kumaisamalira?”

 • “Kodi mwana wanga azidzakwanitsa kufika kuntchito panthawi yake ngati panopa akulephera kufika panyumba nthawi yabwino?”

Ngati zimenezi zikukudetsani nkhawa, kumbukirani kuti sikuti mwana wanu angaime payekha lero ndi lero, koma pamatenga nthawi yaitali, ngakhalenso zaka zimene. Koma panopa, mukutha kuona kuti zochita za mwanayo n’zogwirizana ndi mfundo yakuti, “utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.”​—Miyambo 22:15.

Komabe, mukamam’langiza ndi kumutsogolera bwino, n’zosakayikitsa kuti iye akadzakula adzakhala munthu wodalirika amene ‘waphunzitsa luntha lake kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’​—Aheberi 5:14.

Mfundo Zimene Zingakuthandizeni

Kuti mwana wanu wachinyamata akule bwino, muyenera kumuthandiza kuti akhale ndi “luntha la kulingalira,” limene lingamuthandize kuti azisankha yekha zochita mwanzeru. (Aroma 12:1, 2) Mungagwiritse ntchito mfundo za m’Baibulo zotsatirazi pothandiza mwanayo.

Afilipi 4:5: “Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse.” Tiyerekezere kuti mwana wanu wachinyamata wakupemphani kuti azifika panyumba mochedwerapo, koma inu mwamukaniza. Ndiyeno mwanayo akunyinyirika n’kukufunsani kuti: “N’chifukwa chiyani mumanditengabe ngati mwana wamg’ono?” Zikatere musafulumire kunena kuti: “Ukuchita zinthu ngati mwana wamg’ono kumene.” M’malomwake, kumbukirani mfundo iyi: Achinyamata amafuna kuti apatsidwe ufulu wochuluka kwambiri kuposa umene amafunikiradi, ndipo makolo amapereka ufulu wochepa kwambiri kusiyana ndi umene ayenera kupereka. Motero, zingakhale bwino kuti muzisintha malamulo nthawi ndi nthawi n’cholinga choti azigwirizana ndi msinkhu wa mwana wanu. Ndipo zingakhale bwinonso kuganizira zimene mwanayo akunena.

TAYESANI IZI: Lembani mbali zingapo zimene mungawonjere ufulu kwa mwana wanu. Koma muuzeni kuti mukum’patsa ufuluwo kwa nthawi yochepa chabe. Muuzeninso kuti ngati angaugwiritse ntchito moyenera mumuonjezera ufulu wina, koma akapanda kutero, mudzamulanda.​—Mateyo 25:21.

Akolose 3:21: “Atate inu, musamakwiyitse ana anu, kuti asakhale opsinjika mtima.” Makolo ena amapanikiza kwambiri ana awo. Pofuna kutetezera mwana wawo, makolowo amamuuza kuti asamayende, koma azingokhala panyumba nthawi zonse. Iwo amafika pomusankhira anthu oti azicheza nawo ndiponso akamalankhula pafoni amamubisalira n’kumamvetsera zimene akunena. Komabe kumuchitira zimenezi mwana kumabweretsa mavuto nthawi zambiri. Kumuletsa kuti asamayende ngakhale pang’ono kungachititse kuti mwanayo aganize zothawa panyumbapo. Ndipo kumangomuletsa nthawi zonse kuti asamacheze ndi anzake kungamuchititse kuti azilakalaka kwambiri kucheza nawo. Komanso kumubisalira kuti muzimvetsera zimene akulankhula pafoni kungamuchititse kuti mwanayo apeze njira ina yolankhulira ndi anzake imene inuyo simungaidziwe. Kumbukirani kuti kupanikiza kwambiri mwana wanu sikuthandiza chilichonse, koma kumangochititsa kuti mwanayo apeze njira zina zochitira zinthu zimene mukumuletsazo. Zimenezi n’zoona chifukwa ngati mwana wanu simukumulola kuti azisankha yekha zinthu zina panthawi imene ali panyumba panu, sangadzathe kusankha zinthu mwanzeru akadzachoka panyumbapo.

TAYESANI IZI: Mukamakambirana ndi mwana wanu, muthandizeni kuti aone mmene zimene akufunazo zingakhudzire mbiri yake. Mwachitsanzo, m’malo momuletsa kucheza ndi mnzake wina wake, mungachite bwino kumufunsa kuti: “Kodi ukuganiza kuti anthu angaone kuti ndiwe munthu wotani ngati mnzako uja [tchulani dzina la mnzakeyo] atamangidwa chifukwa cha khalidwe lake lija?” Muthandizeni kuona kuti zimene iye angasankhe kuchita zingakhudze mbiri yake.​—Miyambo 11:17, 22; 20:11.

Aefeso 6:4: “Musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova ndi  kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” Mawu akuti “malango” sakungotanthauza kuuza mwana wanu mfundo zoti azitsatira basi. Koma amatanthauzanso kumulangiza pomusonyeza kufunika kotsatira malangizowo ndipo zimenezi zingachititse kuti asinthe khalidwe lake. Kulangiza mwana m’njira imeneyi n’kofunika kwambiri makamaka mwanayo akafika paunyamata. Pamfundo imeneyi, bambo wina dzina lake Andre, ananena kuti: “Mwana wanu akamakula, muyenera kumamulangiza mokambirana naye m’malo mongomuuza zochita.”​—2 Timoteyo 3:14.

TAYESANI IZI: Ngati mwana wanu akufuna kuchita chinthu chinachake cholakwika kapena ngati wachichita kale, mulangizeni mwa kuyerekezera kuti mwanayo ndi inuyo, ndipo inuyo ndi mwanayo. Kenako m’funseni kuti anene malangizo amene akanakupatsani mukanakhala kuti inuyo ndi mwana wake. Ndiyeno muuzeni kuti akafufuze mfundo za m’Baibulo zimene zikugwirizana kapena kutsutsana ndi malangizo oterowo ndipo onetsetsani kuti mwakambirananso nkhaniyi pasanathe mlungu umodzi.

Agalatiya 6:7: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” Mwana wamng’ono angaphunzitsidwe mwa kupatsidwa chilango, monga kumuletsa kuti asamachite zinthu zina zake zimene amazikonda kwambiri. Koma polangiza mwana wachinyamata, muyenera kukambirana naye kuti aganizire mavuto amene angabwere chifukwa cha khalidwe lakelo.​—Miyambo 6:27.

TAYESANI IZI: Mwana wanu akakhala ndi ngongole, musamamulipirire. Komanso ngati akulephera kusukulu, musamuyikire kumbuyo. Musiyeni kuti aone mavuto omwe angabwere chifukwa cha zochita zakezo ndipo zimenezo zingam’thandize kuti aphunzirepo kanthu.

Monga makolo, mwina mukanakonda kuti musamakumane ndi mavuto ena alionse mwana akafika paunyamata. Koma zimenezi si zimene zimachitika chifukwa mwana akafika msinkhu umenewu, mavuto amakhala ambiri. Ngakhale zili choncho, mwana wanu akafika paunyamata, imakhala nthawi yabwino yoti ‘mum’phunzitse poyamba njira yake.’ (Miyambo 22:6) Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri kuti banja lanu likhale losangalala.

^ ndime 3 Mayina a m’nkhani ino asinthidwa.

DZIFUNSENI KUTI . . .

Panthawi imene mwana wanga adzachoke panyumba, kodi adzakhala akutha kuchita zinthu zotsatirazi?

 • kuchita zinthu zauzimu nthawi zonse

 • kusankha zinthu mwanzeru

 • kulankhulana bwino ndi anthu ena

 • kusamalira thanzi lake

 • kusamalira ndalama

 • kusamalira nyumba yake

 • kuchita zinthu mosadalira munthu wina