Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake

Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake

 Yandikirani Mulungu

Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake

Eksodo 34:6, 7

KODI munthu atakufunsani za Mulungu, mungafotokoze kuti ndi wotani ndiponso kuti ali ndi makhalidwe otani? Tayerekezerani kuti inuyo mwapatsidwa mwayi wofunsa Mulungu kuti akufotokozereni makhalidwe ake. Izi n’zimene zinachitikira mneneri Mose, ndipo tili ndi mwayi wodziwa zimene zinachitikazo, chifukwa iye anauziridwa kulemba nkhaniyo.

Mose ali paphiri la Sinai, anapempha Yehova kuti: “Ndionetsenitu ulemerero wanu.” (Eksodo 33:18) Tsiku lotsatira, mneneriyu anapatsidwa mwayi woona mbali yochepa chabe ya ulemelero wa Mulungu. * Mose sanafotokoze mwatsatanetsatane zonse zimene anaona m’masomphenya aulemerero wa Mulungu. M’malomwake, iye analemba zimene Mulungu ananena, chifukwa n’zimene zinali zofunika kwambiri. Tiyeni tione zimene Yehova ananena zokhudza makhalidwe ake, palemba la Eksodo 34:6, 7.

Choyamba, Yehova anauza Mose kuti iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo.” (Vesi 6) Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo ananena kuti mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “wachifundo,” amanena za “chifundo chachikulu cha [Mulungu] ngati chimene bambo amachitira ana ake.” Ndipo mawu amene anawamasulira kuti “wachisomo,” amafanana ndi mawu omwe “amanena za munthu yemwe ali ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza munthu amene wakumana ndi mavuto.” N’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tidziwe kuti iye amasamalira atumiki ake mofanana ndi mmene makolo amasamalirira ana awo mwachikondi ndiponso kuwapezera zofunika pamoyo.​—Salmo 103:8, 13.

Kenako Yehova anauza Mose kuti iye ndi “wolekereza.” (Vesi 6) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu ndi wosakwiya msanga. Atumiki ake a padziko lapansi akalakwitsa zinthu, Iye amaleza nawo mtima ndipo amawapatsa nthawi yoti alape.​—2 Petulo 3:9.

Mulungu ananenanso kuti iye ndi “waukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Vesi 6) Kukoma mtima kapena kuti chikondi chosatha, ndi khalidwe la Yehova lapamwamba kwambiri limene limachititsa kuti iye azigwirizana kwambiri ndi anthu ake, ndipo chikondi chimenechi sichilephera. (Deuteronomo 7:9) Ndiponso Yehova ndiye kuchimake kwa choonadi. Choncho, iye sanganame kapenanso kunamizidwa. Popeza kuti iye ndi “Mulungu wa choonadi,” timakhulupilira ndi mtima wonse zimene amanena, kuphatikizapo zimene watilonjeza zokhudza mtsogolo.​—Salmo 31:5.

Mfundo inanso yofunika kwambiri imene Yehova amafuna kuti tidziwe ndi yakuti iye ‘amakhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.’ (Vesi 7) Iye ndi wokonzeka ‘kukhululukira’ anthu ochimwa omwe alapa. (Salmo 86:5) Komabe Yehova sasangalala ndi uchimo. N’chifukwa chake iye anati ‘samasula wopalamula.’ (Vesi 7) Mulungu yemwe ndi woyera ndiponso wachilungamo sadzalekerera mpaka kalekale anthu amene amachimwa mwadala, koma tsiku lina adzawalanga.

Zimene Yehova ananena zokhudza makhalidwe ake zikusonyezeratu kuti iye amafuna kuti timudziwe ndiponso kuti tiphunzire makhalidwe ake onse. Kodi zimenezi sizikukuchititsani kufuna kuphunzira zochuluka zokhudza makhalidwe a Mulungu amenewa?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Sikuti Mose anaonadi Yehova, chifukwa palibe munthu yemwe angaone Mulungu n’kukhalabe ndi moyo. (Eksodo 33:20) Koma Yehova anaonetsa Mose masomphenya a ulemerero Wake, ndipo analankhula naye kudzera mwa mngelo.