Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amatenga Ana Kuti Akakhale Angelo Kumwamba?

Kodi Mulungu Amatenga Ana Kuti Akakhale Angelo Kumwamba?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Amatenga Ana Kuti Akakhale Angelo Kumwamba?

Popepesa maliro a mwana, achinansi ena amanena kuti: “Mulungu wamutenga kuti akakhale mngelo kumwamba.” Kodi inuyo mukuganiza kuti zimenezi n’zoona?

Ngati n’zoona kuti Mulungu ndiye amachititsa kuti ana azifa chifukwa choti akusowa angelo kumwamba, ndiye kuti Mulunguyo ndi wokakala mtima. Komatu zimene Baibulo limanena sizigwirizana ndi mfundo imeneyi. (Yobu 34:10) Bambo wachifundo sangalande mwana wa banja lina pofuna kukulitsa banja lake. Komatu palibe kholo lililonse lachifundo koposa Yehova chifukwa khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndilo chikondi. (1 Yohane 4:8) Chikondi chake n’chachikulu zedi moti n’zosatheka kuti achite zinthu zankhanza ngati zimenezi.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi Mulungu akusowekera angelo kumwamba?’ Baibulo limanena kuti ntchito zonse zimene Mulungu anachita n’zangwiro. (Deuteronomo 32:4) Ntchito yake yolenga mwachindunji angelo mamiliyoni ambirimbiri inali yangwiro, ndipo sipanaperewere mngelo aliyense. (Danieli 7:10) Kodi n’zotheka kuti Mulungu sanawerengetsere bwinobwino polenga angelowo? Zimenezo n’zosatheka ngakhale pang’ono. Mulungu Wamphamvuyonse sangalakwitse powerengetsera. N’zoona kuti Yehova wasankha anthu ena kuti akakhale anthu auzimu odzalamulira mu Ufumu wake wakumwamba. Komatu anthu amenewa sapita kumwamba ali ana ayi, chifukwa amafa ali anthu aakulu.​—Chivumbulutso 5:9, 10.

Chifukwa china chosonyeza kuti Mulungu sangatenge ana padziko pano kuti akakhale angelo kumwamba n’chakuti zimenezi n’zosagwirizana ndi cholinga chake polenga anthu kuti azibereka ana. M’munda wa Edeni, Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Ana ndi mphatso imene Mulungu amapereka mogwirizana ndi cholinga chake choti dziko lapansi lidzaze ndi anthu olungama. Iye sankafuna kuti ana azifa asanadyerere n’komwe kenaka n’kuwasandutsa angelo kumwamba. Baibulo limanena momveka bwino kuti “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Kodi Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, angawalande makolo mphatso imene anawapatsa yekha? Ayi ndithu, sangatero.

Mwana akamwalira mwadzidzidzi, timakhala ndi chisoni chosaneneka ndipo mtima wathu umawawa kwambiri. Komano kodi makolo amene akulira maliro a mwana wawo angakhale ndi chiyembekezo chotani? Baibulo limalonjeza kuti Mulungu adzaukitsa anthu ambirimbiri m’paradaiso padziko lapansi pompano. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona ana amene anamwalira ataukitsidwa ndiponso ali ndi thanzi labwino n’kukumananso ndi makolo awo. (Yohane 5:28, 29) Cholinga cha Mulungu n’chakuti ana azikula, kusangalala ndi moyo, n’kumaphunzira za iye ndiponso za cholinga chake polenga dziko lapansi. Motero ana amene anamwalira sanasanduke angelo kumwamba ayi koma akudikira kudzaukitsidwa m’paradaiso padziko pompano. Panthawiyo, mu ulamuliro wa Mlengi wathu wachikondi, anthu onse akulu ndi ana omwe, adzasangalala kulambira Yehova Mulungu kwamuyaya.