Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sinali Nthawi Yanga”

“Sinali Nthawi Yanga”

 “Sinali Nthawi Yanga”

Dalaivala wa chigalimoto chachikulu chotaya zinyalala analephera kuchiwongolera bwinobwino. Ndiye chinachoka mumsewu n’kuwomba munthu ndi mkazi wake komanso mnyamata wina wa zaka 23. Nyuzipepala ina ya mumzinda wa ku New York inati banjalo linafera pomwepo koma mnyamatayo anangokomoka. Atadzidzimuka n’kuona zimene zinachitikazo, mnyamatayo anati: ‘Sindikumvetsa ayi. Mulungu, ndithandizeni chonde.’ Iye anatinso: “Ndiye kuti sinali nthawi yanga yakufa.”

N’KUTHEKA kuti nanunso mwamvapo nkhani ngati zimenezi. Munthu akapulumuka lokumbakumba, anthu amakonda kunena kuti, ‘Sinali nthawi yake,’ koma munthu akafa mwadzidzidzi pangozi, amati, ‘Nthawi yake inakwana’ kapena amati, ‘Ndi chikonzero cha Mulungu mwiniwake.’ Anthu onsewa mfundo yawo imakhala yofanana ndithu. Anthu ambiri amakhulupirira kuti zinthu zimene zimachitika pa moyo wawo ndiponso zotsatirapo za zochitika zimenezi zinalembedweratu ndiponso kuti palibe chilichonse chimene angachite kuti azisinthe. Sikuti anthu amanena zimenezi pankhani ya imfa kapena ngozi yokha, ndipo zimenezi sizinayambe lero ayi.

Mwachitsanzo, kale ku Babulo anthu ankakhulupirira kuti zochita zonse za anthu zimatengera kayendedwe ka nyenyezi. Motero ankayang’ana nyenyezi kuti aone zizindikiro ndiponso kuti adziwe za tsogolo lawo. Agiriki ndi Aroma ankalambira milungu yaikazi ya mwayi imene iwowa ankakhulupirira kuti inali ndi mphamvu zambiri zopatsa anthu mwayi kapena tsoka, kuposa mphamvu za milungu yawo ikuluikulu monga Zeu ndi Jupita.

M’mayiko a ku Asia, Ahindu ndi Abuda amakhulupirira kuti munthu aliyense anakhalaponso moyo wina kalelo ndiyeno zimene zikum’chitikira panopo ndi malipiro a zochita zake pa moyo woyambawo. Amakhulupiriranso kuti zochita zake panopo zidzakhudzanso zimene zidzam’chitikire pa moyo umene adzakhale nawonso m’tsogolo. Zipembedzo zina, kuphatikizapo matchalitchi ambiri Achikhristu, zimakhulupiriranso mfundo zofanana ndi zimenezi.

Motero n’zosadabwitsa kuti ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri ndi ozindikira, pali anthu ambiri amene amakhulupirirabe kuti moyo wawo, zochita zawo ndiponso tsogolo lawo lonse zinalembedweratu ndi kuti palibe chimene angachite kuti asinthe zimenezi. Kodi inunso mumakhulupirira zimenezi? Kodi zochitika zonse pa moyo, zabwino ndi zoipa, ngakhale kubadwa kwa munthu kapena kufa kwake, zinalembedweratu? Kodi Mulungu anakonzeratu zochitika zonse za pa moyo wanu? Tiyeni tione mmene Baibulo lingatithandizire kuyankha mafunso amenewa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Ken Murray/​New York Daily News