Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthawi Yosankha

Nthawi Yosankha

Nthawi Yosankha

“Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”​—Genesis 1:27.

MAWU otchuka amenewa ali m’mavesi oyambirira a m’Baibulo ndipo amanena za chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Mulungu ‘anazikongoletsa pa mphindi yake.’ Chinthu chimenechi ndicho kulenga mwamuna ndi mkazi wangwiro, Adamu ndi Hava. (Mlaliki 3:11) Monga Mlengi wawo, Yehova Mulungu anawauza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”​—Genesis 1:28.

Mulungu ananena mawu amenewa kwa anthu awiri oyambirirawa powauza cholinga chimene anawalengera. Iye anawalenga n’cholinga choti achulukane ndi kusamalira dziko lapansi, kuti lonse lisanduke paradaiso woti iwowo komanso ana awo azikhalamo. Mulungu sanaikiretu nthawi yoti iwowo adzafe. Komano Mulungu anawalonjeza chinthu chosangalatsa kwambiri chakuti akasankha zinthu mwanzeru n’kukhalabe ogwirizana ndi Mulungu, ndiye kuti adzakhala kosatha mwamtendere ndiponso mosangalala.

Koma iwowa sanasankhe zinthu mwanzeru ndipo n’chifukwa chake anthu amakalamba ndi kufa. Ndipotu Yobu ananena kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Kodi chinalakwika n’chiyani makamaka?

Baibulo limalongosola kuti: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Tikudziwa kuti “munthu mmodzi” ameneyu anali Adamu, chifukwa iyeyu anaphwanya mwadala lamulo la Mulungu lomveka bwino. (Genesis 2:17) Pochita zimenezi, Adamu anataya mwayi woti iye ndi ana ake akhale ndi moyo wosatha padziko lapansi. M’malomwake anapatsira ana akewo uchimo ndi imfa. Zinaoneka ngati cholinga cha Mulungu chasokonezeka. Koma ayi si choncho.

Nthawi Yokonzanso Zinthu

Patatha zaka masauzande, Mulungu anauzira wamasalmo kulemba kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Potsimikizira kuti lonjezo limene Mulungu anapereka mu Edeni lidzakwaniritsidwa, Mawu a Mulungu amafotokoza motere zinthu zokhudza mtima zimene Mulungu achite posachedwapa: “Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Kenaka Mulungu ananena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”​—Chivumbulutso 21:4, 5.

Podziwa kuti chilichonse chili ndi nthawi yake, sitingalephere kufunsa kuti, ‘Kodi nthawi yosintha zinthu zonse imeneyi idzafika liti, kuti malonjezo osangalatsa a Mulungu adzakwaniritsidwe?’ A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magazini ino, akhala akuyesetsa kudziwitsa anthu kuti tikukhala m’nthawi imene Baibulo limati ndi “masiku otsiriza” ndi kuti nthawi yayandikira yoti Mulungu achitepo kanthu ‘kupanga zonse kukhala zatsopano.’ (2 Timoteyo 3:1) Tikukulimbikitsani kuti mufufuze bwinobwino m’Baibulo kuti mudziwe malonjezo osangalatsa amene mungapindule nawo. Tikukulimbikitsaninso kumvera mawu akuti: “Funani Yehova popezeka iye, itanani iye pamene ali pafupi.” (Yesaya 55:6) Motero, zochita zanu n’zimene zingakupatseni chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha kapena ayi ndipo Mulungu sanachite kulemberatu zimenezi ayi.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano”