Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzinda wa Korinto “Unali ndi Magombe Awiri Akeake”

Mzinda wa Korinto “Unali ndi Magombe Awiri Akeake”

Mzinda wa Korinto “Unali ndi Magombe Awiri Akeake”

MUKAYANG’ANA mapu a dziko la Greece, mungathe kuona kuti dzikoli limaoneka ngati zilumba ziwiri; china chili kumtunda ndipo china chili kumunsi. Pali kadera (kotchedwa Isthmus of Corinth), kamene kamalumikiza zilumba ziwirizi. Chigawo china cha kaderaka n’chochepa kwambiri pafupifupi makilomita 6 m’lifupi.

Kadera kameneka n’kothandizanso m’njira zina. Kamatchedwa kuti mlatho wowolokera nyanja, chifukwa choti kum’mawa kwake kuli nyanja ya Mediterranean ndi ya Ejani ndipo kumadzulo kwake kuli nyanja ya Iyoni, Adriatic ndi ya Mediterranean. Pakatikati pa nyanja zimenezi panali mzinda wa Korinto. Mtumwi Paulo anakhalapo mumzindawu pa maulendo ake aumishonale ndipo ndi wodziwika kwambiri chifukwa unali wotukuka, anthu ake anali okonda zosangalatsa ndipo analinso amakhalidwe oipa.

Mzindawu Unali Pamalo Abwino

Mzinda wa Korinto unali cha kumadzulo kwenikweni kwa kadera kolumikiza zilumba ziwirizi. Unali ndi magombe awiri. Lina (lotchedwa Lechaeum) linali cha kumadzulo kwa kaderaka ndipo lina lotchedwa Kenkereya linali cha kummawa. N’chifukwa chake katswiri wina wa ku Greece woona za malo, dzina lake Strabo, ananena kuti mzinda wa Korinto “unali ndi magombe awiri akeake.” Chifukwa cha malo amene mzindawu unali, unakhala likulu la zamalonda. Amalonda ochokera kumtunda komanso oyenda panyanja ankakumana pamzindawu.

Kuyambira kalekale, sitima zochokera m’zigawo za kummawa (ku Asia Minor, Suriya, Foinike ndi Iguputo) komanso zochokera m’zigawo za kumadzulo (ku Italy ndi ku Spain) zinkafikira mumzindawu. Zikafika, anthu ankatsitsa katundu n’kuyenda naye pamtunda kupita ku mbali ina ya kaderaka. Kumbali inayo ankalongedza katunduyo mu sitima zina n’kumapitiriza ulendo wawo. Timaboti ting’onoting’ono tinkakokedwa kudutsa kaderaka.​—Onani  bokosi patsamba 27.

N’chifukwa chiyani oyenda panyanjawa ankadzera pakadera kameneka? Ankatero poopa kuyenda ulendo wa makilomita 320 wodutsa m’dera limene kunkakonda kuchitika namondwe, la kum’mwera kwa chilumba cha Peloponnese. M’malo amenewa munkachitika mafunde kawirikawiri. Anthuwa ankaopa kudutsa makamaka kudoko la Malea ndipo ponena za dokoli ankati: “Ukadutsa ku Malea, subwerako wamoyo.”

Gombe la Kenkereya Lomwe Linakwiririka

Gombe la Kenkereya, lomwe lili pa mtunda wa makilomita 11 kum’mawa kwa Korinto, ndi gombe lomaliza limene sitima zapamadzi zopita ku Asia zinkaimapo. Masiku ano, mbali ina ya gombeli inamira chifukwa cha chivomerezi chimene chinachitika cha kumapeto kwa chaka cha 300 C.E. Katswiri woona za malo uja, Strabo, ananena kuti pagombeli panali chuma chambiri ndipo anthu ankakhala pikitipikiti. Ndipo katswiri wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba, dzina lake Lucius Apuleius, anati gombeli ndi “lalikulu ndipo ndi lofunika kwambiri chifukwa pamafika sitima zochokera m’mayiko osiyanasiyana.”

Panthawi ya ulamuliro wa Aroma, pagombeli panali timitunda tiwiri tomwe tinalowa m’nyanja ndipo tinachititsa kuti pakhale malo abwino ofikira ndi kunyamukira sitima. Malowa anali aakulu pafupifupi mamita 150 kapena 200. Ngakhale sitima zazitali mamita 40 zinkatha kufikira pa malo amenewa. Ofukula mabwinja apeza kuti kum’mwera chakumadzulo kunali kachisi amene akumuganizira kuti anali malo opatulika a mulungu wamkazi wotchedwa Isis. Zikuoneka kuti nyumba zomwe zinali kumbali ina ya gombeli zinali malo opatulika a mulungu winanso wamkazi wotchedwa Aphrodite. Anthu ankakhulupirira kuti milungu iwiri imeneyi inkateteza anthu oyenda panyanja.

N’kutheka kuti Paulo ankagwira ntchito yosoka mahema ku Korinto chifukwa cha malonda amene ankachitika padokoli. (Machitidwe 18:1-3) Buku lina linati: “Nthawi yozizira ikafika, anthu osoka mahema ku Korinto amenenso ankayenda panyanja ankakhala ndi chintchito chadzaoneni. M’nyengoyi, madoko onse awiri ankadzaza ndi sitima zoti azikonze ndi kuikamo zinthu zonse zofunikira chifukwa panthawiyi panyanja sipankayenda sitima iliyonse. Zikatero anthu ochokera ku Lechaeum ndi ku Kenkereya amene ankagulitsa masipeyala a sitima ankafuna anthu ambiri otha kusoka nsalu za sitima zoyendera mphepo.”​—In the Steps of St. Paul.

Atakhala ku Korinto kwa chaka chimodzi ndi theka, Paulo anachoka ku Kenkereya n’kupita ku Efeso cha m’ma 52 C.E. (Machitidwe 18:18, 19) Patapita zaka zinayi mpingo unakhazikitsidwa ku Kenkereya. Baibulo limanena kuti Paulo anapempha Akhristu a ku Roma kuti athandize Febe amene anali “mumpingo wa ku Kenkereya.”​—Aroma 16:1, 2.

Masiku ano alendo ofika ku gombe la Kenkereya amasambira m’madzi oyera bwino cha kudera limene gombeli silinakwiririke lonse. Koma ambiri sadziwa kuti derali kale linali lodzaza ndi amalonda komanso Akhristu amene ankalalikira. Izi n’zimene zimachitikanso ku gombe la Lechaeum limene lili cha kumadzulo kwa Korinto.

Msewu Wotchedwa Lechaeum

Kuchokera ku malo a zamalonda ku Korinto panali msewu wotchedwa Lechaeum, umene unkafika ku gombe la kumadzulo ndipo ndi wautali makilomita awiri. Akatswiri ena anakumba m’mphepete mwa gombeli n’kuunjika dothilo kumtunda. Izi zinathandiza kuti pakhale malo ofikira sitima, abwino ndi otetezeka ku mphepo. Panthawi ina doko limeneli linali limodzi mwa madoko aakulu kwambiri m’nyanja ya Mediterranean. Akatswiri a mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi anafukula zidutswa za nsanja yolondolera anthu oyenda panyanja yomwe inali ndi chiboliboli cha mulungu wotchedwa Poseidon atatenga lawi la moto.

M’mphepete mwa msewu wa Lechaeum, womwe unali pakati pa makoma awiri, munali tinjira, nyumba za boma, akachisi komanso munayalana masitolo ambirimbiri. N’kutheka kuti Paulo anakumana ndi anthu ogula malonda, eni sitolo, akapolo, ogulitsa malonda ndi anthu ena. Awa anali anthu abwino kwambiri kuwalalikira.

Gombe la Lechaeum linali malo a zamalonda komanso likulu la sitima za nkhondo. Ena amati sitima zankhondo zamphamvu kwambiri komanso zokhala ndi mizere itatu ya opalasa zinakonzedwa ku gombe la Lechaeum ndi katswiri wina wa ku Korinto dzina lake Ameinocles cha m’ma 700 B.C.E. Anthu a ku Atene anagwiritsa ntchito sitima zamtunduwu pogonjetsa asilikali a panyanja a ku Perisiya pa Salami mu 480 B.C.E.

Poyamba, malowa anali doko lokhala ndi amalonda yakaliyakali koma panopa pali bango lokhalokha. Palibe chilichonse chosonyeza kuti kalelo linali limodzi mwa madoko akuluakulu kwambiri pa nyanja ya Mediterranean.

Mavuto Amene Akhristu Anakumana Nawo ku Korinto

Magombe a ku Korinto anali malo a malonda komanso anachititsa kuti anthu atengere kwambiri zochita za alendo obwera mumzindawu. Magombewa anachititsa kuti malonda aziyenda bwino m’derali komanso kuti litukuke. Mzinda wa Korinto unkapeza ndalama chifukwa anthu ofika ndi katundu komanso ofuna kudutsa ndi katundu mumzindawo ankalipira msonkho wokwera kwambiri. Anthu odutsa ndi katundu m’misewu ya mumzindawu ankalipiranso misonkho. Chakumapeto kwa zaka za m’ma 600 B.C.E., mzindawu unatolera ndalama zambiri za misonkho moti unasiya kutolera ndalama za misonkho kuchokera kwa nzika zake.

Mzinda wa Korinto unapeza ndalama zina kuchokera kwa amalonda okhala mumzindawu. Ambiri mwa anthu amenewa anali olemera ndipo ankakonda kukonza mapwando n’kumachita makhalidwe oipa. Anthu ambiri oyenda panyanja ankafikanso kumzindawu ndipo ankabweretsa chuma. Strabo anati anthuwa ankasakaza ndalama kwambiri. Anthu a mumzindawu ankagwira ntchito zosiyanasiyana kuphatikizapo kukonza sitima.

M’nthawi ya Paulo mzindawu unali ndi anthu pafupifupi 400,000. Mizinda imene inali ndi chiwerengero choposa chimenechi inali ya Roma, Alesandriya ndi Antiokeya wa ku Suriya. Ku Korinto kunkakhala Ayuda komanso anthu ochokera ku Girisi, ku Roma ndi ku Suriya. Chifukwa cha madoko ake, mumzindawu munkafika anthu apaulendo, okaonerera masewero othamanga, aluso losiyanasiyana, akatswiri a maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba, anthu amalonda ndi ena. Anthu amenewa ankapereka mphatso ku akachisi komanso kupereka nsembe kwa milungu. Zinthu zonsezi zinachititsa kuti mzinda wa Korinto utukuke kwambiri. Koma zinabweretsanso mavuto ena.

Buku lina linati: “Popeza mzinda wa Korinto unali pakati pa magombe awiri unatukuka kwambiri komanso anthu ake anatengera makhalidwe oipa a alendo amene ankafika ndi sitima zawo m’magombewo.” Makhalidwe oipa onse a m’mayiko a kummawa ndi kumadzulo anafika mumzindawu. Izi zinachititsa kuti anthu a mumzinda wa Korinto azikhala moyo wosakaza ndalama kwabasi komanso kuti muzichitika chiwerewere chosaneneka poyerekezera ndi mizinda ina yonse ya ku Girisi. Moti moyo wotayirira ndiponso wachiwerewere unafika pomatchulidwa kuti Chikorinto.​—In the Steps of St. Paul.

Kukonda chuma ndiponso chiwerewere zinaika pangozi moyo wauzimu wa Akhristu ambiri. Akhristu a ku Korinto anafunika kulangizidwa kuti akhalebe ndi khalidwe lovomerezeka pamaso pa Mulungu. N’chifukwa chake Paulo analemba kalata kwa Akorinto yodzudzula makhalidwe monga dyera, kulanda ena zinthu ndiponso dama. Mukamawerenga makalata ouziridwa amenewa, mungathe kuoneratu kuti Akhristu anayenera kulimbana ndi zinthu zambiri zomwe zikanawononga khalidwe lawo.​—1 Akorinto 5:9, 10; 6:9-11, 18; 2 Akorinto 7:1.

Komabe, chifukwa chokhala ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, mzinda wa Korinto unali ndi zabwino zake. Nthawi zonse mumzindawu munkabwera anthu okhala ndi nzeru zatsopano. Anthu ake anali ochangamuka kuposa anthu am’mizinda ina imene Paulo anafikako. Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anati: “Anthu a m’mayiko akum’mawa ndi akumadzulo ankakumana patawuni imeneyi ndipo izi zinachititsa kuti anthu amumzindawu atengere maganizo, nzeru komanso zipembedzo za m’mayiko osiyanasiyana.” Chifukwa cha zimenezi zipembedzo zambiri zinali zololeka mumzindawu ndipo izi zinachititsa kuti ulaliki wa Paulo uyende bwino kumeneku.

Magombe awiri a ku Korinto, omwe ndi Kenkereya ndi Lechaeum, anachititsa kuti mzindawu ukhale wotukuka komanso wotchuka. Magombewa anachititsanso kuti moyo wauzimu wa Akhristu a ku mzindawu ukhale pa ngozi. Ndi mmene zililinso masiku ano. Moyo wa anthu ambiri oopa Mulungu uli pa ngozi chifukwa chakuti dzikoli limalimbikitsa kukondetsa chuma ndiponso chiwerewere. Choncho ifenso tiyenera kumvera malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Korinto.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 27]

 MSEWU WODUTSA SITIMA ZAPAMADZI

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 600 B.C.E., bwanamkubwa wa mzinda wa Korinto dzina lake Periander, mwa luso lake anakonza njira yonyamulira katundu mu sitima zapamadzi, podutsa kadera ka pakati pa Girisi ndi Korinto. * Anachita zimenezi atalephera kukonza ngalande yoti sitima zizidutsa bwinobwino m’kaderako. Anatenga zimiyala zikuluzikulu n’kukonza msewu woti muzidutsa katundu wodutsa pakati pa zilumba ziwirizi. Akapolo ndiwo ankakoka ngolo za matayala zonyamula katundu amene watsitsidwa m’sitima kuti akalowe m’sitima ina. Sitima zing’onozing’ono zinkatha kukokedwanso mumsewu umenewu n’kupita mbali ina ya nyanja.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 29 Kuti mumve zambiri zokhudza kukonzedwa kwa ngalande yatsopano onani Galamukani! ya Chingelezi ya December 22, 1984, tsamba 25-27 pa kamutu kakuti, “The Corinth Canal and Its Story.”

[Mapu patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

GREECE

Gulf of Corinth

Gombe la Lechaeum

Korinto wakale

Kenkereya

Isthmus of Corinth

Saronic Gulf

Peloponnese

NYANJA YA IYONI

Doko la Malea

NYANJA YA EJANI

[Chithunzi patsamba 25]

Masiku ano sitima zonyamula katundu zimadutsabe mu ngalande ya ku Korinto

[Chithunzi patsamba 26]

Gombe la Lechaeum

[Chithunzi patsamba 26]

Gombe la Kenkereya

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Todd Bolen/​Bible Places.com