Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizithokoza Mulungu Chifukwa cha Mvula

Tizithokoza Mulungu Chifukwa cha Mvula

Tizithokoza Mulungu Chifukwa cha Mvula

KODI zinthu zikanakhala bwanji pakanapanda mvula? N’zoona kuti mvula ikachuluka madzi amasefukira ndi kuwononga zinthu. Ndipo anthu amene amakhala m’madera ozizira ndi amvula kapena amene mumagwa mvula yambiri, nthawi zina samasangalala ndi nyengo ya mvula. (Ezara 10:9) Koma anthu amene amakhala m’madera otentha kwambiri amasangalala mvula ikagwa.

Ndi mmene zinalili m’madera otentha otchulidwa m’Baibulo monga ku Asia Minor, kumene mtumwi Paulo anakachita umishonale. Ali kumeneko, Paulo anauza anthu a mumzinda wakale wa Lukaoniya kuti: “[Mulungu] sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zopatsa zipatso. Anadzaza mitima yanu ndee, ndi chakudya ndi chimwemwe.” (Machitidwe 14:17) Onani kuti Paulo anayamba ndi kutchula mvula popeza popanda mvula zinthu sizingamere ndipo sipangakhale “nyengo zopatsa zipatso.”

M’Baibulo muli nkhani zambiri zokhudza mvula. Ndipo mumapezekanso mawu ambirimbiri achiheberi ndi achigiriki onena za mvula. Nkhaniyi ikufotokozerani zambiri za mphatso yapaderayi. Komanso ikuthandizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Baibulo limanena zolondola pankhani za sayansi.

Kodi Baibulo Limanena Chiyani za Mvula?

Yesu Khristu anafotokoza chimene chimathandiza kwambiri kuti tikhale ndi mvula. Iye anati: “Atate wanu wa kumwamba . . . amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyo 5:45) Kodi mwaona kuti Yesu anayamba watchula kaye dzuwa asanatchule mvula? Zimenezi n’zoyenera chifukwa dzuwa limathandiza zomera kuti zikule komanso kuti madzi asinthe m’njira zosiyanasiyana n’kudzagwanso ngati mvula. Inde, kutentha kwa dzuwa n’kumene kumapangitsa madzi a m’nyanja kupanga nthunzi chaka chilichonse. Popeza Yehova Mulungu ndi amene analenga dzuwa, ndi iye amene amasintha madzi kuti akhale mvula.

Baibulo limafotokoza kayendedwe ka madzi motere: “Mulungu . . . akweza madontho a mvula, akhetsa mvula ya m’nkhungu yake imene mitambo itsanulira, nivumbitsira anthu mochuluka.” (Yobu 36:26-28) Ngakhale kuti papita zaka zambirimbiri mawu olondola pankhani za sayansi amenewa atalembedwa, anthu akufufuzabe kuti adziwe zimene zimachitika kuti madzi akhale mvula. Buku lina limene linalembedwa mu 2003 linanena kuti, “mpaka pano anthu ambiri samadziwa bwinobwino mmene madontho a mvula amapangidwira.”​—Water Science and Engineering.

Zimene asayansi akudziwa n’zakuti madontho a mvula amapangidwa ndi tinthu ting’onoting’ono timene timakutidwa ndi nthunzi m’mitambo. Tinthu timeneti tikachulukana kwambiri timapanga dontho limodzi la mvula. Kusintha kumeneku kumatenga maola ambiri. Buku lina la sayansi limanena kuti: “Anthu amanena zambirimbiri zokhudza mmene tinthu ting’onoting’ono timeneti timakulira kuti tifike pokhala madontho a mvula ndipo ofufuza ambiri akuthera nthawi yawo pofuna kudziwa zenizeni zimene zimachitika.”​—Hydrology in Practice.

Mlengi amene anakonza luso limene lagona pa kapangidwe ka mvula anafunsa mtumiki wake Yobu mafunso ogometsa awa: “Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame? Ndani analonga nzeru m’mitambomo? . . . Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani?” (Yobu 38:28, 36, 37) Ngakhale kuti papita zaka 3,500 mawu amenewa atanenedwa, asayansi akulepherabe kupeza mayankho a mafunso ovuta amenewa.

Kodi Zimakhala Bwanji Kuti Mvula Igwe?

Akatswiri achigiriki ankaphunzitsa kuti madzi a m’mitsinje samachokera ku mvula koma kuti ndi madzi a m’nyanja amene amayenda pansi pa nthaka mpaka kufika pamwamba pa mapiri kenako n’kukhala akasupe. Ndipo katswiri wina womasulira Baibulo ananena kuti Solomo ankakhulupiriranso zimenezi. Taonani mawu owuziridwa a Solomo awa: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” (Mlaliki 1:7) Kodi Solomo ankatanthauza kuti madzi a m’nyanja amadutsa kaye m’mapiri asanapite m’mitsinje? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyeni tione zimene anthu anthawi ya Solomo ankakhulupirira pankhani ya kayendedwe kamadzi. Kodi iwo ankakhulupirira mfundo zabodza?

Pasanathe zaka 100 kuchokera m’nthawi ya Solomo, mneneri wa Mulungu, Eliya anasonyeza kuti ankadziwa kumene kumachokera mvula. Mu nthawi yake, m’dzikolo munali chilala kwa zaka zoposa zitatu. (Yakobe 5:17) Yehova Mulungu anabweretsa chilala chimenechi pa anthu ake chifukwa anamukana n’kuyamba kulambira Baala, mulungu wa Akanani amene ankati amabweretsa mvula. Koma Eliya anathandiza Aisiraeli kuti alape ndipo anapemphera kuti kugwe mvula. Eliya akupemphera anauza mnyamata wake kuyang’ana “kunyanja.” Atauzidwa kuti “kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu,” Eliya anadziwa kuti pemphero lake layankhidwa. Nthawi yomweyo, “thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu.” (1 Mafumu 18:43-45) Zimenezi zikusonyeza kuti Eliya ankadziwa mmene madzi amayendera kuti afike pokhala mvula. Iye ankadziwanso kuti mitambo ikapangidwa pamwamba pa nyanja, iwombedwa ndi mphepo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Ndipo mpaka pano zimenezi ndi zimene zimachitika kuti m’derali mugwe mvula.

Patatha zaka pafupifupi 100 Eliya atapempherera mvula, mlimi wina dzina lake Amosi anatchula mfundo yofunika yonena za kumene madzi amvula amachokera. Amosi anatumidwa ndi Mulungu kuti aletse Aisiraeli kuzunza anthu osauka komanso kulambira milungu yonyenga. Kuti Mulungu asawaononge, Amosi anawalimbikitsa ‘kufuna Yehova kuti akhale ndi moyo.’ Ndiyeno Amosi anafotokoza kuti woyenera kulambiridwa ndi Yehova yekha chifukwa ndiye Mlengi “wakuitana madzi a m’nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi.” (Amosi 5:6, 8) Patapita nthawi Amosi anabwerezanso mfundo imeneyi. (Amosi 9:6) Choncho, Amosi anasonyeza kuti nyanja ndi zimene zimathandiza kwambiri kuti m’dzikoli muzigwa mvula.

Mu 1687, Edmond Halley anapereka umboni wa sayansi wotsimikizira mfundo imeneyi. Komabe, zinatenga nthawi yaitali kuti anthu akhulupirire zimene Halley ananena. Buku lina linati: “Mpaka kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1700, anthu ankakhulupirirabe mfundo yakuti madzi amayenda pansi pa nthaka kupita pamwamba pa mapiri n’kukhala kasupe.” Koma masiku ano anthu ambiri amadziwa mmene madzi amayendera kuti afike pogwa ngati mvula. Bukuli linanenanso kuti: “Madzi a m’nyanja amauluka ngati nthunzi, kenako amazizira kukhala mitambo, ndipo amadzagwa ngati mvula, zikatere amayenda m’mitsinje kubwereranso kunyanja.” (Encyclopædia Britannica Online) Choncho, mawu a Solomo onena za kayendedwe kamadzi, opezeka pa Mlaliki 1:7, amanena za kapangidwe ka mitambo ndi mvula kameneka.

Kodi Zimenezi Ziyenera Kutilimbikitsa Kuchita Chiyani?

Taona kuti kayendedwe kamadzi kanafotokozedwa bwino ndi olemba Baibulo osiyanasiyana. Umenewu ndi umboni umodzi wapadera wosonyeza kuti Baibulo linauziridwa ndi amene analenga anthu, Yehova Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) N’zoona kuti kusasamala kwa anthu kwapangitsa kuti nyengo isinthe ndipo zimenezi zimachititsa kuti m’madera ena madzi azisefukira komanso m’madera ena muzikhala chilala. Koma Yehova Mulungu amene analenga kayendedwe kamadzi analonjeza kalekale kuti ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’​—Chivumbulutso 11:18.

Kodi panopa mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatso zimene Mulungu watipatsa monga mvula? Mungachite zimenezi mwa kuphunzira Mawu ake, Baibulo, ndi kugwiritsira ntchito zimene mukuphunzirazo. Mukatero, mungayembekezere kupulumuka ndi kulowa m’dziko latsopano la Mulungu limene mudzasangalala kosatha ndi mphatso zimene Mulungu amapereka. Ndithudi, “mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro” zimachokera kwa Yehova Mulungu amene amapereka mvula.​—Yakobe 1:17.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MITAMBO

MVULA

NTHUNZI

NTHUNZI

MADZI A PANTHAKA

MADZI APANSI PANTHAKA

[Zithunzi patsamba 16]

Eliya akupemphera, mnyamata wake ankayang’ana “kunyanja.”