Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anaphunzira pa Zolakwa Zake

Anaphunzira pa Zolakwa Zake

 Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Anaphunzira pa Zolakwa Zake

YONA analakalaka ataletsa chiphokoso choboola m’khutucho. Linali phokoso la chimphepo chadzaoneni chomwe chinali kuwomba mwamphamvu sitima imene anakwera komanso cha zimafunde zazikulu ngati mapiri zomwe zinali kukwechesa matabwa a sitimayo. Koma chimene chinam’boola m’mimba kwambiri Yona chinali kukuwa kwa anthu oyendetsa sitimayo, omwe anali kuyesa izi ndi izi pofuna kuti sitimayo isamire. Mumtima mwake Yona ankangoti anthu onsewa afa chifukwa cha iyeyo basi.

Kodi zinatani kuti Yona apezeke m’vuto lalikulu chonchi? Iye anam’lakwira kwambiri Mulungu wake, Yehova. Kodi analakwa chiyani? Kodi palibe chimene akanachita kuti zinthu zisinthe? Tingaphunzire zambiri poona mayankho a mafunso amenewa. Mwachitsanzo, nkhani ya Yona imatithandiza kuona kuti ngakhale anthu amene ali ndi chikhulupiriro chenicheni angathe kulakwitsa, komanso imatithandiza kuona mmene angakonzere zolakwa zawozo.

Mtumiki wa ku Galileya

Anthu akamaganizira za Yona, nthawi zambiri amaganizira za zolakwa zake, mwina zokhudza kusamvera kwake kapena kuumitsa khosi kwake. Komatu Yona analinso ndi makhalidwe ambiri abwino. Kumbukirani kuti Yehova Mulungu anam’sankha kuti akhale mneneri wake. Yona akanakhala wosakhulupirika kapena wochita zoipa, Yehova sakanam’patsa udindo waukulu ngati umenewu.

Pa 2 Mafumu 14:25, timapezapo mfundo zina zokhudza mbiri ya Yona. Iye anali wochokera ku Gati-heferi, dera lomwe linali pamtunda wa makilomita anayi kuchokera ku tauni ya Nazareti. Yesu Khristu anakulira ku Nazareti komweku. Apa n’kuti patapita zaka pafupifupi 800 kuchokera panthawi ya Yona. * Yona anali mneneri muulamuliro wa mfumu Yerobiamu Wachiwiri, yemwe anali kulamulira mafuko khumi a Isiraeli. Apa n’kuti Eliya komanso Elisa, yemwe anadzam’lowa m’malo, atafa kalekale muulamuliro wa bambo ake a Yerobiamu. Ngakhale kuti Yehova anagwiritsira ntchito anthu amenewa kuthetsa kulambira Bala, mtundu wa Isiraeli unasocheranso mwadala. Tsopano dzikolo linali kulamulidwa ndi mfumu imene ‘inachita choipa pamaso pa Yehova.’ (2 Mafumu 14:24) Motero, tingathe kuona kuti ntchito ya Yona siinali yophweka kapena yokondweretsa ayi. Komabe iye anachita ntchitoyi mokhulupirika.

Komabe, tsiku lina moyo wa Yona unasintha kwambiri. Yehova anam’patsa ntchito imene Yonayo anaona kuti imuvuta kwambiri. Kodi inali ntchito yotani?

“Nyamuka, Pita ku Nineve”

Yehova anauza Yona kuti: “Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukuluwo, nulalikire motsutsana nawo; pakuti choipa chawo chandikwerera pamaso panga.” (Yona 1:2) N’zosavuta kumvetsa chimene chinam’chititsa Yona kuopa ntchito imeneyi. Mzinda wa Nineve unali pamtunda wa makilomita 800 kulowera kum’mawa. Iye akanatha mwezi wathunthu akuyenda wapansi. Koma kwenikweni, izi si zimene zinali kumuopsa. Zimene anayenera  kuchita akakafika ku Nineveko ndizo zinamuopsa kwambiri. Iye anayenera kukalalikira zoti Yehova akufuna kulanga anthuwo. Anthu amenewa anali Asuri ndipo anali anthu oopedwa chifukwa anali ouma mtima kwambiri ndiponso okonda zachiwawa. Ngakhale pakati pa Aisiraeli, omwe anali anthu a Mulungu, ndi anthu ochepa chabe amene anamvetsera uthenga wa Yona, ndiye kuli bwanji anthu akunja amenewa? Kodi mneneri wa Yehova mmodzi yekha zikanamuyendera bwanji mumzinda waukulu wa Nineve, womwe unatchedwa kuti “mudzi wa mwazi”?​—Nahumu 3:1, 7.

Sitikudziwa ngati Yona ankaganizira zonsezi kapena ayi. Koma zimene tikudziwa n’zakuti iye anathawa. Yehova anam’tuma kuti apite ku Nineve, komwe kunali kum’mawa, koma Yona analowera kumadzulo ndipo ankafuna kupita kutali kwambiri. Iye anapita mumzinda wa Yopa n’kukwera sitima yapamadzi yopita ku Tarisi. Akatswiri ena amati dera la Tarisi linali ku Spain. Ngati zimenezi n’zoona, ndiye kuti Yona ankathawira ku dera limene linali pamtunda wa makilomita 3,500 kuchokera ku Nineve. Ulendowu ukanam’tengera chaka chathunthu, chifukwa ukanam’fikitsa kumapeto kwenikweni kwa nyanja ya Mediterranean, yomwe masiku amenewo ankaitcha kuti Nyanja Yaikulu. Apatu tingaone kuti Yona anatsimikizadi zothawa ntchito imene Yehova anam’patsa.

Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yona anali munthu wamantha? Tisafulumire kumuweruza choncho. M’nkhani ino tiona kuti iye anachitanso zinthu zosonyeza kulimba mtima kwambiri. Kungoti, mofanana ndi tonsefe, Yona nayenso anali ndi zofooka zosiyanasiyana. (Salmo 51:5) Kodi ndani wa ife amene sanayambe wachitapo mantha?

Nthawi zina tingaone kuti Mulungu akufuna kuti tichite chinthu chinachake chimene tikuona kuti n’chovuta kwambiri, mwinanso chosatheka. Mwinanso timaopa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, imene Mkhristu aliyense ayenera kuchita. (Mateyo 24:14) N’zosavuta kuiwala mfundo yofunika kwambiri imene Yesu ananena yakuti: “Zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.” (Maliko 10:27) N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina timatha kuiwala mfundo imeneyi ndipo izi n’zimenenso zinam’chitikira Yona. Komano kodi pamene Yona ankathawa anakumana ndi zotani?

Yehova Anam’phunzitsa Mneneri Wosamverayo

Tangoganizirani mmene zinalili paulendowu. Yona analowa m’sitima yonyamula katundu n’kupeza malo abwino okhala. N’zotheka kuti sitimayi inali ya ku Foinike. Yona anangokhala duu n’kumaonerera anthu oyendetsa sitimayo ali pakalapakala kukonzekera kuchoka padokopo. Sitimayi itanyamuka, doko linayamba kuzimiririka pang’onopang’ono kenako osaonekanso ndipo mwina Yona ankangoti basi pamenepa wathawa. Koma mwadzidzidzi panyanja panaipa.

 Madzi anawinduka mochititsa nthumanzi chifukwa cha chimphepo champhamvu. Ndiyetu panabadwa zimafunde zadzaoneni zazitali ngakhale kuposa sitima zikuluzikulu za masiku ano. Pasanapite nthawi n’komwe, sitima yawo yamatabwayo mwina inkangooneka ngati kabokosi ka machesi, pakati pa zimafunde zazikulu ngati mapiri. Sitikudziwa ngati panthawiyo Yona ankadziwa mfundo imene anadzailemba patsogolo, yakuti ‘Yehova ndiye anautsa chimphepo chachikulucho panyanja.’ Komabe Yona anaona akatswiri oyendetsa sitimayo akufuula kuti milungu yawo iwathandize, ndipo iye ankadziwa kuti milungu yawoyo siingawathandize. Iye analemba kuti: “Chombo chikadasweka.” (Yona 1:4; Levitiko 19:4) Ndipotu Yona zinam’vuta kuti apemphere kwa Mulungu amene anali kum’thawa.

Pothedwa nzeru, Yona anapita m’chipinda cha pansi pasitimayo kuti akagone. Ndiyetu anagona tulo tofa nato. * Mkulu wa oyendetsa sitimayo atam’peza, anamudzutsa n’kumulimbikitsa kuti apemphere kwa mulungu wake, monga aliyense anali kuchitira. Poona kuti chimphepochi chinali chodabwitsa, anthuwo anachita maere kuti adziwe munthu amene wawabweretsera tsoka limeneli. N’zachidziwikire kuti mtima wa Yona unagunda kwambiri ataona kuti maerewo sakugwera aliyense mwa anthuwo. Posakhalitsa iye anadziwa kuti Yehova ndi amene anali kuchititsa chimphepocho ndi kutsogolera maerewo n’cholinga choti aliyense adziwe kuti wolakwa sanali wina ayi koma Yonayo.​—Yona 1:5-7.

Kenaka Yona anaulula zonse kwa oyendetsa sitimawo. Anawauza kuti iye ndi mtumiki wa Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, ndipo anam’chimwira pothawa. Anatinso zimene anachitazo n’zimene zinabweretsa tsoka kwa aliyense m’sitimamo. Amunawo anagwidwa mantha aakulu ndipo ngakhale Yona anaona kuti zimenezi zawaopsa kwambiri. Iwo anam’funsa zimene angachite kuti apulumutse sitimayo komanso miyoyo yawo. Kodi Yona anawayankha bwanji? Iye anaganiza zoti aponyedwe m’nyanja, komano n’kutheka kuti maganizo amenewa anam’ziziritsa nkhongono kwabasi chifukwa nyanjayo inali yozizira komanso yoopsa kwambiri. Komabe iye sanafune kuphetsa anthu onsewo akudziwa kuti angathe kuwapulumutsa. Motero Yona anati: “Mundinyamule ndi kundiponya m’nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu [ameneyu] wakugwerani chifukwa cha ine.”​—Yona 1:12.

Yona akanakhala munthu wamantha sakananena mawu ngati amenewa. Yehova ayenera kuti anasangalala poona kulimba mtima kwake, komanso mtima wake wololera kufera ena panthawi yoopsa ngati imeneyi. Apatu tingathe kuona kuti Yona anali ndi chikhulupiriro chachikulu kwambiri. Ifenso masiku ano tingathe kutsanzira chikhulupiriro choterechi pokhala okonzeka kuvutikira ena. (Yohane 13:34, 35) Tikaona anzathu akufunikira kulimbikitsidwa, thandizo lauzimu, kapena thandizo lina lililonse, kodi timayesetsa kudzipereka kuwathandiza ndi mtima wonse? Yehova amasangalala kwambiri tikamatero.

N’kutheka kuti oyendetsa sitima aja anakhudzidwa mtima kwambiri, chifukwa poyamba anakana kumuponya Yona m’nyanja. M’malomwake anayesetsa ndi mphamvu zawo zonse kuzemba chimphepocho, koma analephera. Anangokhala ngati kuti chimphepocho akuchiwonjezera mphamvu. Potsiriza pake anaona kuti panalibenso chimene angachite. Choncho, iwo anafuula kwa Yehova, Mulungu wa Yona, kuti awachitire chifundo ndipo anam’nyamula Yonayo, kumukokera m’mphepete mwa sitimayo, n’kumuponyera m’nyanja.​—Yona 1:13-15.

Yehova Anam’chitira Chifundo N’kumupulumutsa

Yona anagwa kuti phwafaa m’nyanja yolusayo. N’kutheka kuti anayesa umu ndi umu kuti asambire, kwinaku akuona sitimayo ikupita poteropo. Koma mwamsanga Yona anakwiririka m’zimafunde zija n’kuyamba kumira. Iye anayamba kumira ndipo ankangoona kuti basi kwake kwatha.

Patsogolo pake, Yona anafotokoza mmene anamvera panthawiyo. Iye ankangoona nyenyezi zokhazokha m’mutu mwake. Anadandaula kwambiri poganiza kuti sadzaonanso kachisi wokongola wa  Yehova ku Yerusalemu. Kenako anangozindikira kuti wafika pansi penipeni panyanja, pafupi ndi tsinde la mapiri a m’nyanja. Ziyangoyango za m’nyanja zinam’kolakola. Iye ankangoona kuti manda ake akhala amenewo.​—Yona 2:2-6.

Koma mwadzidzidzi anangoona chinthu chinachake chachikulu, chabii chikubwera poteropo. Kenako chinam’thamangira kukamwa kwake kuli yasaa ndipo Yona anangozindikira kuti cham’meza.

Apa anaona kuti basi wajiwa. Komabe Yona anadabwa kuti adakali moyo. Sanalumidwe kapena kugayidwa m’mimbamo ndipo ankapuma bwinobwino ngakhale kuti amenewa anayenera kukhala manda ake. Kenaka Yona anayamba kuchita mantha kwambiri. Iye sanakayikirenso kuti Mulungu wake,Yehova, ndi amene ‘anaikiratu chinsomba chachikulu kuti chim’meze.’ *​—Yona 1:17.

Yona anakhala m’mimba mwa chinsombacho kwa maola ambiri. Muchimdima cha ndiweyani chimenechi, iye anayamba kusinkhasinkha ndiponso kupemphera kwa Yehova Mulungu. Pemphero lake, lomwe lili m’chaputala chachiwiri cha buku la Yona, limatithandiza kum’dziwa bwino Yonayu. Limasonyeza kuti Yona ankadziwa bwino Malemba chifukwa anatchula mfundo zambiri za m’buku la Masalmo. Limasonyeza kuti iye anali ndi mtima woyamikira kwambiri. Yona ananena kuti: “Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mawu akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso n’cha Yehova.”​—Yona 2:9.

Yona anaphunzira kuti Yehova angathe kupulumutsa munthu aliyense, kulikonse ndiponso nthawi ina iliyonse. Ngakhale kuti mtumiki wakeyu anali ‘m’mimba mwa nsomba,’ Yehova anam’pulumutsa. (Yona 1:17) Ndi Yehova yekha amene akanatha kusunga munthu m’mimba mwa chinsomba n’kukhala bwinobwino kwa masiku atatu, usana ndi usiku. Masiku ano ndi bwino kuti tizikumbukira kuti Yehova ndi “Mulungu amene m’dzanja mwake muli mpweya wanu.” (Danieli 5:23) Popanda Yehova sibwenzi tikumapuma n’kukhala ndi moyo. Kodi timayamikira zimenezi? Ndiyetu tizimumvera Yehovayo nthawi zonse.

Nanga kodi Yona uja anatani? Kodi anayamba kumvera Yehova posonyeza kuyamikira kwake? Inde. Patatha masiku atatu, nsomba ija inam’pititsa m’mphepete mwa nyanja ndipo “inam’sanzira Yona kumtunda. (Yona 2:10) Tangoganizirani kuti Yona anayenda ulendo wonsewo popanda ngakhale kusambira. Komabe, atafika kumtundako anafunika kudziwa kolowera. Pasanapite nthawi, Yona anakumananso ndi chiyeso china chimene chinaonetsa kuti iyeyu analidi munthu woyamikira. Lemba la Yona 3:1, 2, limati: “Ndipo mawu a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.” Kodi Yona anatani?

Iye sanazengereze ayi. Baibulo limati: “Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Nineve, monga mwa mawu a Yehova.” (Yona 3:3) Yona anamvera Mulungu, zomwe zikusonyezeratu kuti anali ataphunzira pa zolakwa zake. Apanso tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Yona. Tonse ndife ochimwa ndipo timalakwitsa zinthu zina. (Aroma 3:23) Komano kodi tikatero, timangogweratu ulesi kapena timaphunzirapo kanthu pa zolakwa zathu n’kuyamba kumvera Mulungu?

Kodi Yehova anam’dalitsa Yona chifukwa cha kumvera kwake? Inde, anatero. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti patsogolo pake Yona anadziwa kuti, iye atangodzipereka kuti aponyedwe m’madzi, chimphepo chija chinasiya ndipo anthu aja anakafika kwawo bwinobwino. Moti onse “anaopa Yehova ndi mantha aakulu,” n’kupereka nsembe kwa Iye, m’malo mwa milungu yawo.​—Yona 1:15, 16.

Komanso Yona anadalitsidwa kwambiri patsogolo pake, chifukwa Yesu anagwiritsira ntchito nkhani ya Yona m’mimba mwa chinsomba pofotokoza mophiphiritsira mmene iye adzakhalire m’manda. (Mateyo 12:38-40) Yona akadzauka kuti akhale ndi moyo padziko pano, adzasangalala kwambiri akadzamva zoti anadalitsidwa m’njira imeneyi. (Yohane 5:28, 29) Dziwani kuti Yehova amafunitsitsanso kukudalitsani. Chotero mofanana ndi Yona, inunso muziyesetsa kuphunzira pa zolakwa zanu ndipo muzisonyeza mzimu womvera ndiponso wololera kuvutikira ena.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 N’zochititsa chidwi kuti Yona anachokera m’tauni ya ku Galileya chifukwa choti, ponyoza Yesu Afarisi ananena kuti: “Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.” (Yohane 7:52) Omasulira mabuku ndiponso ofufuza ambiri amati ponena mawu amenewa, Afarisi anali kutanthauza kuti m’mbuyomo kapena panthawiyo panalibiretu mneneri aliyense amene anachokera m’chigawo chonyozeka cha Galileya. Ngati izi n’zimene Afarisiwo anali kutanthauza ndiye kuti iwo anali kuthawa dala chilungamo chifukwa mawu amenewa anali otsutsana ndi mbiri komanso ulosi wa m’Baibulo.​—Yesaya 9:1, 2.

^ ndime 17 Baibulo la Septuagint limanena kuti Yona anagona tulo mpaka kufika poliza nkonono. Komabe tisaganize kuti Yona anagona chifukwa choti analibe nazo ntchito zimene zimachitikazo. Tisaiwale kuti anthu amatha kukhala ndi tulo kwambiri chifukwa cha nkhawa. Mwachitsanzo, panthawi imene Yesu anali pachipsinjo chachikulu kwambiri m’munda wa Getsemane, Petulo, Yakobe, ndi Yohane “anagona chifukwa cha chisoni.”​—Luka 22:45.

^ ndime 25 Mawu a Chiheberi akuti “nsomba,” m’Chigiriki anawamasulira kuti “chilombo cha m’nyanja,” kapena “chinsomba chachikulu.” Sitingathe kudziwa kuti imeneyi inali nsomba yamtundu wanji kwenikweni, komabe tikudziwa kuti m’nyanja ya Mediterranean muli nsomba zikuluzikulu zotchedwa shaki zimene zingathe kumeza munthu wathunthu. M’nyanja zina nsomba zimenezi zimatha kukula kwambiri moti zina zimakhala zazitali mamita 15, kapenanso kuposa.

 [Bokosi/​Chithunzi patsamba 29]

Anthu Ena Amatsutsa Nkhani ya Yona

▪ Kodi nkhani zimene zili m’buku la Yona zinachitikadi? Kuyambira kale anthu ena akhala akutsutsa nkhani za m’bukuli. Masiku ano maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo achititsa anthu ena kutsutsa buku la Yona n’kumati nkhani zake n’zongopeka basi. Munthu wina wolemba mabuku m’zaka za m’ma 1800, analemba zimene m’busa wina ananena pankhani ya Yona. M’busayo anati nkhani ya Yona ndi yophiphiritsa. Iye ananena kuti kwenikweni Yona anakhala mu hotela ina ya ku Yopa yotchedwa Chizindikiro cha Chinsomba. Ndalama zitamuthera anamuthamangitsa pa hotelayo. Malingana ndi m’busayo, Yona ‘anamezedwa’ kenako ‘n’kusanzidwa’ ndi chinsomba m’njira yophiphiritsa imeneyi. N’zoonekeratu kuti cholinga cha anthu amenewa ndi kungotsutsa nkhani ya Yona basi.

N’chifukwa chiyani anthu ambiri amatsutsa nkhani imeneyi? N’chifukwa choti ndi yozizwitsa. Anthu oterewa amatsutsa zozizwitsa zonse ndipo amati sizingachitike. Koma kodi maganizo amenewa ndi omveka? Taganizirani funso ili: ‘Kodi inuyo panokha mumakhulupirira mawu oyambirira a m’Baibulo?’ Mawuwa amati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Anthu ambiri ozindikira amavomereza mfundo yoona imeneyi. Komatu zoona zake n’zakuti chiganizo chimenechi chimanena zinthu zozizwitsa kwambiri kuposa zozizwitsa zina zonse zotchulidwa m’Baibulo.

Ndiyeno taganizirani izi: Kodi amene analenga kumwamba ndi zamoyo zonse za padzikoli angalephere kuchititsa zinthu zimene zafotokozedwa m’buku la Yona? Kodi angalephere kuyambitsa chimphepo, kuchititsa kuti chinsomba chimeze munthu, kenako n’kukamusanza? Mulungu amene ali ndi mphamvu zopanda malire sangalephere kuchititsa zimenezi.​—Yesaya 40:26.

Ndipotu zinthu zina zodabwitsa zimachitika popanda mphamvu ya Mulungu. Mwachitsanzo, akuti mu 1758, munthu wina anagwa m’sitima yomwe inkayenda pa nyanja ya Mediterranean ndipo anamezedwa ndi chinsomba cha mtundu wa shaki. Anthu anachiwombera chinsombacho ndipo chinalavula munthuyo asanavulale paliponse ndipo anapulumuka. Ngati izi zinachitikadi ndiye kuti n’zodabwitsa kwambiri koma si zozizwitsa. Ndiyeno kodi Mulungu sangagwiritse ntchito mphamvu zake m’njira yoposa pamenepa?

Anthu otsutsawa amanenanso kuti munthu sangakhale moyo kwa masiku atatu m’mimba mwa chinsomba. Koma tikudziwa kuti anthu amatha kuika mpweya m’mathanki kuti azitha kupuma ali pansi pa nyanja. Ndiyeno kodi Mulungu akanalephera kugwiritsa ntchito mphamvu zake ndi nzeru zake zapamwamba kuti Yona akhalebe moyo kwa masiku atatu? Pajatu mngelo wa Yehova anauza mayi wa Yesu Mariya kuti, “pakuti zimene Mulungu wanena, sizilephereka.” (Luka 1:37)

Kodi n’chiyaninso chimene chimatsimikizira kuti nkhani ya Yona inachitikadi? Yona anafotokoza momveka bwino za sitima kapena kuti chombo komanso anthu amene anali m’chombocho. Lemba la Yona 1:5 limasonyeza kuti anthuwo anaponya m’nyanja katundu wina pofuna kuchipepuza. Akatswiri a mbiri yakale komanso malamulo a arabi amasonyeza kuti anthu ankachitadi zimenezi akakumana ndi namondwe panyanja. Komanso zimene Yona ananena zokhudza Nineve zimagwirizana ndi zimene zalembedwa m’mbiri yakale komanso zimene akatswiri a mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi anapeza. Koma koposa zonsezi, Yesu Khristu ananena kuti Yona anakhala m’mimba mwa chinsomba kwa masiku atatu ndipo izi zinaphiphiritsira nthawi imene Yesuyo anali m’manda. (Mateyo 12:38-40) Umboni wa Yesu umatsimikizira kuti nkhani ya Yona ndi yoona.

“Pakuti zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”​—LUKA 1:37

[Chithunzi patsamba 26]

Yona anauza oyendetsa sitima kuti am’ponyere m’nyanja