Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mnyamata Wolimba Mtima

Mnyamata Wolimba Mtima

 Zoti Achinyamata Achite

Mnyamata Wolimba Mtima

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera. Nkhaniyi ikhale ngati ikuchitika panopa.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI 1 SAMUELI 17:1-11, 26, 32-51.

Kodi mukuganiza kuti Goliati ankaoneka bwanji ndipo mawu ake ankamveka bwanji?

․․․․․

Ngakhale kuti Davide sanali m’gulu la asilikali a Isiraeli, n’chifukwa chiyani analowerera nkhondo yolimbana ndi Goliati? (Onani vesi 26.)

․․․․․

N’chiyani chinam’limbitsa mtima Davide kuti Yehova amuthandiza? (Werenganinso vesi 34 mpaka 37.)

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Pogwiritsa ntchito mabuku oyenerera, fufuzani ndi kulemba zotsatirazi mkalembedwe kamakono:

(1) Kutalika kwa Goliati. (1 Samueli 17:4)

Mikono isanu ndi umodzi ndi chikhato = ․․․․․.

(2) Kulemera kwa malaya aunyolo a Goliati. (1 Samueli 17:5)

Masekeli a mkuwa 5,000 = ․․․․․.

(3) Kulemera kwa khali kapena kuti mutu wa mkondo wa Goliati. (1 Samueli 17:7)

masekeli a chitsulo 600 = ․․․․․.

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Kulimba mtima.

․․․․․.

Kudalira Yehova osati mphamvu zanu.

․․․․․.

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Tchulani zinthu zovuta zimene mungakumane nazo zofuna kuti mulimbe mtima mofanana ndi mmene Davide anachitira polimbana ndi Goliati?

․․․․․.

Kodi ndi zinthu ziti zimene zinakuchitikirani inuyo kapena anthu ena zimene zimakutsimikizirani kuti Yehova sadzakutayani?

․․․․․.

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․.