Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Pontiyo Pilato anali ndi chifukwa choopera Kaisara?

Pofuna kukakamiza bwanamkubwa wa Roma, dzina lake Pontiyo Pilato, kuti apachike Yesu, atsogoleri achiyuda anati: “Mukam’masula ameneyu, ndiye kuti sindinu bwenzi la Kaisara.” (Yohane 19:12) “Kaisara” ameneyu anali mfumu ya Roma, dzina lake Tiberiyo. Kodi Pilato anali ndi chifukwa choopera Kaisarayu?

Kodi Kaisara Tiberiyo anali munthu wotani? Buku lina limanena kuti zaka zingapo Yesu asanaimbidwe mlandu, Tiberiyo anali atakhala kale “munthu wongofuna kukwaniritsa zokhumba zake, ndipo ankachita chilichonse kuti akwaniritse zokhumba zakezo ngakhale zinthuzo zitakhala zoipa.” (The New Encyclopædia Britannica) Chifukwa choopa anthu, iye ankazunza ndi kupha aliyense amene ankamuganizira kuti angalande ufumu wake. Bukuli linanenso kuti: “Ngati zimene akatswiri a mbiri yakale a m’nthawi [ya Tiberiyo] amanena zili zoona, iye ankakonda masewera achiwawa komanso olaula. Ngakhale pamene zinthu zinali bwino, iye ankapha mwankhanza munthu aliyense amene wafuna kuti amuphe.”

Choncho, mbiri yoipa ya Tiberiyo iyenera kuti inam’chititsa Pilato kumvera zimene atsogoleri achiyuda ananena zoti Yesu apachikidwe.​—Yohane 19:13-16.

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake?

Kale ku Isiraeli, anthu ambiri ayenera kuti sankavala nsapato pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Kwa anthu amene anali ndi nsapato panthawiyo, nsapato zake zinali zongokwana kunsi kwa phazi ndipo pamwamba ankamanga zingwe. Popeza kuti minda ndi misewu ya kumeneko inali yafumbi komanso matope, n’zosakayikitsa kuti anthu ankada kwambiri mapazi.

Choncho, unali mwambo wawo kuti munthu akafika pakhomo avule nsapato zake asanalowe m’nyumba. Kulandira bwino mlendo kunkaphatikizapo kumusambitsa mapazi. Ndipo ntchito imeneyi ankagwira ndi mwininyumba kapena wantchito. Baibulo lili ndi zitsanzo za anthu amene anachita zimenezi. Mwachitsanzo, Abulahamu ananena kwa alendo amene anabwera ku hema wake kuti: “Nditengetu madzi pang’ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; ndipo ndidzatenga chakudya pang’ono, nimutonthoze mitima yanu.”​—Genesis 18:4, 5; 24:32; 1 Samueli 25:41; Luka 7:37, 38, 44.

Mfundo zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chimene Yesu anasambitsira mapazi a ophunzira ake pa Pasika wake womaliza. Pamwambowu, panalibe mwininyumba kapena wantchito kuti agwire ntchito imeneyi, ndipo ophunzira onsewo sanadzipereke kugwira ntchitoyi. Zimene Yesu anachita potenga beseni la madzi ndi thaulo n’kuyamba kusambitsa ndi kupukuta mapazi a atumwi ake, zinawaphunzitsa kufunika kwa chikondi ndi kudzichepetsa.​—Yohane 13:5-17.