Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwapatulidwa

Mwapatulidwa

“Mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa.”—1 AKOR. 6:11.

1. Kodi Nehemiya anapeza zinthu zili bwanji atabwereranso ku Yerusalemu? (Onani chithunzi pamwambapa.)

NEHEMIYA atabwerera ku Yerusalemu pambuyo pa chaka cha 443 B.C.E., anapeza zinthu zitasokonekera kwambiri. Iye anapeza munthu wa mtundu wina, yemwe anali wodziwika kuti ankatsutsa anthu a Yehova, akukhala m’chipinda china cha pakachisi. Alevi anali atasiya ntchito yawo yotumikira Yehova. Nawonso akulu ankachita malonda pa tsiku la Sabata m’malo motsogolera anthu polambira Mulungu. Komanso Aisiraeli ambiri anali atakwatirana ndi anthu a mitundu ina.—Neh. 13:6.

2. Kodi zinakhala bwanji kuti Aisiraeli akhale mtundu wapadera?

2 Mtundu wa Isiraeli unali wosankhidwa ndi Mulungu. Mu 1513 B.C.E., Aisiraeli anavomereza ndi mtima wonse kuti adzamvera Yehova. Iwo anati: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.” (Eks. 24:3) Choncho Mulungu anawapatula kuti akhale anthu ake apadera. Umenewutu unali mwayi waukulu kwambiri. Patapita zaka 40, Mose anawakumbutsa kuti: “Ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, mwa anthu onse okhala padziko lapansi.”—Deut. 7:6.

3. Nehemiya atabwereranso ku Yerusalemu, kodi anapeza Aisiraeli akutumikirabe Mulungu?

3 Koma n’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli sanapitirizebe kukhala ndi mtima womvera. N’zoona kuti nthawi zonse pankakhala anthu ena amene ankatumikirabe Mulungu. Koma Ayuda ambiri sankachita zimene Mulungu amafuna. M’malomwake, ankangochita zinthu kuti anthu ena aziwaona ngati odzipereka polambira Mulungu. Pa nthawi imene Nehemiya anapita ku Yerusalemu kachiwiri, panali patadutsa zaka pafupifupi 100 kuchokera pamene Ayuda ena okhulupirika anabwerera kuchokera ku Babulo kuti akamangenso kachisi wa Yehova. Apanso Aisiraeli anali atasiya kutumikira Mulungu mwakhama.

4. Kodi tikambirana mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tikhalebe anthu opatulika?

4 Mofanana ndi Aisiraeli, tinganene kuti gulu lonse la  Mboni za Yehova ndi lopatulidwa ndi Mulungu. Akhristu odzozedwa komanso anthu a “khamu lalikulu” ndi oyera ndipo apatulidwa kuti atumikire Yehova. (Chiv. 7:9, 14, 15; 1 Akor. 6:11) Ifeyo sitikufuna kuwononga ubwenzi wathu wapadera ndi Mulungu ngati mmene Aisiraeli anachitira. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti zimenezi zisatichitikire koma tikhalebe oyera n’kumatumikira Yehova? M’nkhani ino tikambirana mfundo 4 zimene tingaphunzire m’buku la Nehemiya chaputala 13. Mfundo zake ndi izi: (1) Musamagwirizane ndi anthu oipa; (2) muzithandiza kuti ntchito ya Yehova iziyenda bwino; (3) kulambira Mulungu kuzikhala pa malo oyamba ndiponso (4) musataye mwayi wanu wokhalabe Mkhristu. Tiyeni tsopano tikambirane mfundo zimenezi.

MUSAMAGWIRIZANE NDI ANTHU OIPA

Kodi Nehemiya anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Yehova? (Onani ndime 5 ndi 6)

5, 6. (a) Kodi Eliyasibu ndi Tobia anali ndani? (b) Kodi mwina Eliyasibu ankagwirizana ndi Tobia chifukwa chiyani?

5 Werengani Nehemiya 13:4-9. M’dzikoli muli zinthu zoipa zambirimbiri, choncho kukhalabe oyera si kophweka. Taganizirani za Eliyasibu ndi Tobia. Eliyasibu anali mkulu wa ansembe pomwe Tobia, yemwe anali wachiamoni, ayenera kuti anali ndi udindo winawake mu ulamuliro wa Perisiya ku Yudeya. Pa nthawi ina m’mbuyomo, Tobia ndi anzake anatsutsa Nehemiya pa ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:10) Komanso Aamoni sankaloledwa kupita kukachisi. (Deut. 23:3) Choncho funso n’kumati, N’chifukwa chiyani mkulu wa ansembe analola kuti Tobia akhale m’chipinda chodyera pakachisi?

6 Tobia ankagwirizana kwambiri ndi Eliyasibu. Tobia ndiponso mwana wake Yehohanani anakwatira akazi achiyuda. Ndipo Ayuda ambiri ankalemekeza Tobia. (Neh. 6:17-19) Mdzukulu wina wa Eliyasibu anakwatira mwana wa Sanibalati, yemwe anali bwanamkubwa wa Samariya komanso mnzake wapamtima kwambiri wa Tobia. (Neh. 13:28) Mwina izi n’zimene zinachititsa kuti Eliyasibu achite zimene Tobia ankafuna ngakhale kuti anali munthu wosakhulupirira ndiponso wotsutsa Yehova. Koma Nehemiya anasonyeza kuti anali wokhulupirika kwa Yehova potulutsa katundu wa Tobia m’chipinda chodyera chija.

7. Kodi akulu ndiponso Akhristu ena amachita chiyani kuti akhalebe opatulika kwa Yehova?

7 Popeza tinadzipereka kwa Mulungu, tiyenera kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova. Tiyenera kutsatira mfundo zake zolungama kuti tikhalebe anthu ake opatulika. Tisalole chibale kutilepheretsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Akulu mumpingo ayenera kuyendera maganizo a Yehova osati maganizo awoawo. (1 Tim. 5:21) Iwo ayenera kuyesetsa kupewa chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wawo ndi Mulungu.—1 Tim. 2:8.

8. Kodi atumiki onse a Yehova ayenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya anthu amene amagwirizana nawo?

8 Tingachite bwino kukumbukira kuti “kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akor. 15:33) Ngakhale achibale athu enieni akhoza kutisokoneza. Mwachitsanzo, m’mbuyomo Eliyasibu anathandiza Nehemiya pa ntchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 3:1) Koma patapita nthawi, Eliyasibu anasokonezedwa chifukwa chogwirizana ndi Tobia ndiponso anthu ena. Iye anayamba kuchita zinthu zimene zinachititsa kuti asakhale woyera pamaso pa Yehova. Anthu abwino amatilimbikitsa kuchita zinthu zofunika monga kuwerenga Baibulo, kupita ku misonkhano ndiponso kulalikira. Timayamikira ndiponso kukonda kwambiri achibale athu amene amatilimbikitsa kuchita zinthu zabwino.

MUZITHANDIZA KUTI NTCHITO YA YEHOVA IZIYENDA BWINO

9. N’chiyani chinachititsa kuti zinthu zisokonekere kukachisi ndipo Nehemiya ananena kuti anayambitsa vutoli ndi ndani?

9 Werengani Nehemiya 13:10-13. Zikuoneka kuti pa nthawi imene Nehemiya anabwerera  ku Yerusalemu, zopereka zinali zitasiya kufika kukachisi. Chifukwa chosowa thandizo, Alevi ankasiya utumiki kuti akalime minda yawo. Nehemiya ananena kuti atsogoleri ndi amene anayambitsa vutoli. Zikuoneka kuti iwo sankagwira bwino ntchito zawo. Mwina sankatolera zopereka za anthu, apo ayi sankazipereka kukachisi. (Neh. 12:44) Ndiyeno Nehemiya anakonza zoti anthu azitolera zopereka. Iye anasankha amuna odalirika kuti aziyang’anira malo osungira zinthu kukachisi ndiponso ntchito yogawa zinthuzo.

10, 11. Kodi atumiki a Mulungu angathandize bwanji gulu la Yehova?

10 Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikukumbutsidwa kuti tiyenera kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali. (Miy. 3:9) Tikamapereka zinthu zothandiza pa ntchito ya Yehova, timakhala kuti tikumupatsa zinthu zake zomwe. (1 Mbiri 29:14-16) Mwina tingaganize kuti tilibe zinthu zambiri zoti n’kupereka koma ngati tili ndi mtima wofuna kumupatsa iye adzasangalala ndi chilichonse chimene tingapereke.—2 Akor. 8:12.

11 Kwa zaka zambiri, banja lina lalikulu linkaitana banja la apainiya apadera achikulire kuti lidzadye nawo chakudya kamodzi pa mlungu. Banja locherezalo linali ndi ana 8. Koma mayi a m’banjalo ankakonda kunena kuti: “Kuchereza anthu awiri okha si nkhani.” Kuwaitana kuti adzadye chakudya kamodzi pa mlungu kungaoneke ngati nkhani yaing’ono koma apainiyawo ankayamikira kwambiri. Nawonso apainiyawo anathandiza kwambiri banjalo. Ankalifotokozera zinthu zolimbikitsa kwambiri moti ana a m’banjalo anayamba kuchita bwino kwambiri mumpingo. Patapita nthawi, ana onsewo anayamba utumiki wa nthawi zonse.

12. Kodi akulu ndi atumiki othandiza amapereka chitsanzo chotani?

12 Kodi tikuphunziranso chiyani pa nkhani ya Nehemiya? Mofanana ndi Nehemiya, akulu ndi atumiki othandiza amatsogolera pochita zinthu zothandiza kuti ntchito ya Yehova iziyenda bwino. Abale ndi alongo amathandizidwa ndi chitsanzo chawo. Nayenso mtumwi Paulo anali chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ankachita zinthu zothandiza kuti ntchito ya Yehova iziyenda bwino ndipo ankapereka malangizo abwino kwambiri. Mwachitsanzo, anapereka malangizo othandiza okhudza zopereka.—1 Akor. 16:1-3; 2 Akor. 9:5-7.

KULAMBIRA MULUNGU KUZIKHALA PA MALO OYAMBA

13. Kodi Ayuda ena ankachita zinthu zotani zosalemekeza Sabata?

13 Werengani Nehemiya 13:15-21. Tikamaganizira kwambiri za ndalama ndiponso  katundu, ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kusokonezeka. Mogwirizana ndi lemba la Ekisodo 31:13, kusunga Sabata mlungu uliwonse kunkakumbutsa Aisiraeli kuti ndi anthu opatulika. Pa tsikuli, Aisiraeli ankayenera kulambira Mulungu monga banja, kupemphera ndiponso kuganizira mozama za Chilamulo cha Mulungu. Koma m’nthawi ya Nehemiya, Aisiraeli ena sankasunga Sabata, m’malomwake ankachita zinthu zawo za tsiku ndi tsiku. Iwo sankaonanso kuti kulambira Yehova ndi nkhani yofunika. Nehemiya ataona zimenezi, analamula kuti Sabata lisanayambe, zipata za mzindawo zitsekedwe ndipo anthu ochita malonda ochokera m’mayiko ena athamangitsidwe.

14, 15. (a) N’chiyani chingachitike ngati tikuika malonda kapena ntchito yathu pa malo oyamba? (b) Kodi tingatani kuti tilowe mu mpumulo wa Mulungu?

14 Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Nehemiya? Chinthu chimodzi n’chakuti sitiyenera kulola ntchito kapena malonda kutisokoneza pa nkhani yolambira Yehova. Zimenezi zikhoza kuchitika makamaka ngati timakonda kwambiri malonda kapena ntchito yathu. Kumbukirani chenjezo la Yesu lakuti sitingatumikire ambuye awiri. (Werengani Mateyu 6:24.) Nehemiya anali ndi ndalama ndithu, komabe sanalole zimenezi kumusokoneza pamene anali ku Yerusalemu. (Neh. 5:14-18) M’malo mochita malonda ndi anthu a ku Turo kapena anthu ena, anadzipereka pothandiza abale ake ndiponso poyeretsa dzina la Yehova. Masiku anonso, akulu ndi atumiki othandiza amadzipereka ndi mtima wonse pothandiza mpingo. Izi zimachititsa kuti Akhristu anzawo aziwakonda kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, anthu a Mulungu amakondana ndipo mumpingo mumakhala mtendere.—Ezek. 34:25, 28.

15 Ngakhale kuti Akhristu safunikira kutsatira lamulo losunga Sabata, Paulo anatiuza kuti: “Mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu. Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake, monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.” (Aheb. 4:9, 10) Akhristufe tingalowe mu mpumulo wa Mulungu ngati timamumvera n’kumachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Kodi inuyo pamodzi ndi banja lanu mumaika pa malo oyamba zinthu monga kuphunzira Baibulo, kusonkhana ndiponso kulowa mu utumiki? Tingafunike kufotokoza molimba mtima kwa abwana athu kapena anzathu abizinezi ngati sakutipatsa mpata wochita zimenezi. Nthawi zina tingafunike kuchita zinthu ngati Nehemiya amene ‘anatseka zipata n’kuthamangitsa anthu a ku Turo’ n’cholinga choti aike zinthu zopatulika pa malo oyamba. Popeza Mulungu anatipatula, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimachita pa moyo wanga zimasonyeza kuti Yehova anandisankha kuti ndimutumikire?’—Mat. 6:33.

KHALANIBE MKHRISTU WABWINO

16. Pa nthawi ya Nehemiya, kodi n’chiyani chikanachititsa kuti Aisiraeli asakhalenso anthu osankhidwa ndi Mulungu?

16 Werengani Nehemiya 13:23-27. M’nthawi ya Nehemiya, Ayuda ankakwatira akazi a mitundu ina. Nehemiya atafika nthawi yoyamba ku Yerusalemu, anauza amuna onse achikulire kuti asaine chikalata cholonjeza kuti sadzakwatira akazi a mitundu ina. (Neh. 9:38; 10:30) Koma atabweranso patapita zaka zochepa, anapeza kuti Ayuda ena anali atakwatira akazi a mitundu ina ndipo pakanapita nthawi yaitali sakanadziwikanso kuti ndi anthu osankhidwa ndi Mulungu. Ana a akazi a mitundu ina amenewa sankawerenga kapena kulankhula Chiheberi. Kodi anawo atakula, akanaganiza kuti ndi Aisiraeli? Kapena akanaganiza kuti ndi achiasidodi, achiamoni kapena achimowabu? Kodi ngati sankadziwa Chiheberi, akanadziwa bwanji Chilamulo cha Mulungu? Kodi akanatha bwanji kudziwa Yehova n’kumamutumikira m’malo molambira milungu yonyenga ya amayi awo? Panafunika kukonza zinthu mwamsanga  ndiponso mosanyengerera. Nehemiya anachitadi zimenezi.—Neh. 13:28.

Thandizani ana anu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova (Onani ndime 17, 18)

17. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?

17 Ifenso tiyenera kuyesetsa kwambiri pothandiza ana athu kuti adzakhale Akhristu abwino. Makolo ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ana anga amalankhula bwino “chilankhulo choyera” cha mfundo zoona za m’Baibulo? (Zef. 3:9) Kodi zolankhula za ana anga zimasonyeza kuti amatsogoleredwa ndi mzimu wa Yehova kapena wa dzikoli?’ Koma ngati mwaona kuti pali mavuto ena, musafulumire kutaya mtima. Zimatenga nthawi kuti munthu aphunzire chilankhulo makamaka ngati pali zododometsa zambiri. Ana anu amakumana ndi zinthu zambiri zimene zingawasokoneze. Choncho muyenera kugwiritsa ntchito nthawi ya Kulambira kwa Pabanja komanso mipata ina kuti muwathandize moleza mtima kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Deut. 6:6-9) Athandizeni kudziwa ubwino wokhala osiyana ndi anthu a m’dziko la Satanali. (Yoh. 17:15-17) Choncho muziyesetsa kuwaphunzitsa mowafika pa mtima.

18. N’chifukwa chiyani makolo ndi amene angathandize kwambiri ana awo kusankha kuti atumikire Yehova?

18 Mwana aliyense akakula ayenera kusankha yekha kutumikira Mulungu kapena ayi. Komabe pali zinthu zambiri zimene makolo angachite pothandiza ana. Iwo ayenera kupereka chitsanzo chabwino, kuwapatsa malangizo omveka bwino ndiponso kukambirana nawo mavuto amene angakumane nawo ngati atasankha zinthu molakwika. Makolo, musaiwale kuti inuyo ndi amene mungathandize kwambiri ana kuti asankhe kutumikira Yehova. Muyenera kuthandiza anawo kuti akhalebe Akhristu abwino. Tonsefe tiyenera kusamala kuti tisataye ‘malaya athu akunja,’ omwe akuimira mfundo zimene timayendera komanso makhalidwe amene amasonyeza kuti ndifedi Akhristu.—Chiv. 3:4, 5; 16:15.

MULUNGU SADZAIWALA ‘ZABWINO ZIMENE MUMACHITA’

19, 20. Kodi tingatani kuti Yehova adzatikumbukire ‘pa zabwino zimene timachita’?

19 Mneneri Malaki, amene anatumikira pa nthawi yofanana ndi Nehemiya, anati: “Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa . . . lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.” (Mal. 3:16, 17) Mulungu sadzaiwala anthu amene amamuopa ndiponso kumukonda.—Aheb. 6:10.

20 Popemphera, Nehemiya ananena kuti: “Mundikumbukire pa zabwino zimene ndinachita.” (Neh. 13:31) Mofanana ndi Nehemiya, mayina athu akhoza kulembedwa m’buku la Mulungu la chikumbutso. Izi zingatheke ngati sitigwirizana ndi anthu oipa, timathandiza kuti ntchito ya Yehova iziyenda bwino, timaika zinthu zokhudza kulambira pa malo oyamba ndiponso ngati timayesetsa kuti tikhalebe Akhristu abwino. Tiyeni tipitirize ‘kudziyesa kuti tione ngati tikadali olimba m’chikhulupiriro.’ (2 Akor. 13:5) Tikamayesetsa kukhalabe anthu a Yehova opatulika, iye adzatikumbukira pa zabwino zimene timachita.