Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi n’zoyenera kuti makolo achikhristu azikhala pamodzi ndi mwana wawo wochotsedwa pa misonkhano yampingo?

Malo okhala munthu wochotsedwa m’Nyumba ya Ufumu si nkhani yaikulu. Magazini a Nsanja ya Olonda akhala akulimbikitsa makolo achikhristu kuti ngati zili zoyenera, azithandiza ana awo ochotsedwa amene akukhalabe pakhomo. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, patsamba 19 ndi 20, imanena kuti makolo akhoza kumaphunzira Baibulo ndi mwana wawo wachinyamata amene wachotsedwa ngati akukhalabe pakhomopo. Mwina zimenezi zingathandize kuti mwanayo asinthe n’kuyambanso kutumikira Yehova.

Ngati wachinyamata wochotsedwa wabwera ku misonkhano pa Nyumba ya Ufumu, akhoza kukhala limodzi ndi makolo ake. Palibe lamulo loti ochotsedwa azikhala pampando wakumbuyo. Choncho palibe vuto ngati mwana wochotsedwa angakhale pamalo alionse amene makolo ake akhala. Popeza makolo ali ndi udindo wothandiza mwana wawoyo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, iwo angachite bwino kuonetsetsa kuti akupindula ndi misonkhano. Kukhala naye pamalo amodzi kungathandize kuti achite zimenezi.

Koma bwanji ngati wochotsedwayo anachoka kunyumba ya makolo ake? Kodi mfundo imene tikunenayi ingagwirenso ntchito? M’mbuyomu, magazini a Nsanja ya Olonda akhala akufotokozanso zimene Mkhristu ayenera kuchita ngati wachibale wake wochotsedwa sakukhalanso pakhomopo. * Komabe anthu akalola kuti wachibale wochotsedwa akhale phee limodzi nawo pa nthawi ya misonkhano zimakhala zosiyana kwambiri ndi kulankhulana naye popanda zifukwa zomveka. Limeneli si vuto ngati achibalewo amaona munthu wochotsedwayo moyenera ndipo amayesetsa kutsatira malangizo a m’Malemba okhudza kuyanjana ndi ochotsedwa.—1 Akor. 5:11, 13; 2 Yoh. 11.

Choncho, palibe vuto ngati munthu wochotsedwa, yemwe sakuvutitsa aliyense, wakhala limodzi ndi wachibale wake kapena munthu wina aliyense pa misonkhano. Kuletsa munthu kukhala pamalo enaake kungayambitse mavuto ena. Ngati anthu onse pa misonkhano komanso achibale a wochotsedwayo akutsatira malangizo a m’Malemba pa nkhani ya ochotsedwa, ndiponso zochita zawo sizikukhumudwitsa abale ena, palibe chifukwa chodera nkhawa za malo amene anthu akukhala pa misonkhano. *

^ ndime 6 Izi zikusintha zimene zinalembedwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 1, 1953, tsamba 223 ndiponso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2002, tsamba  4, ndime 12.