Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ganizirani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala

Ganizirani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala

“Ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.”—2 PET. 3:11.

1, 2. Kodi tiyenera kukhala anthu otani ngati tikufuna kuti Mulungu azisangalala nafe?

TONSEFE timafuna kuti anthu azitiona kuti ndife abwino. Koma popeza ndife Akhristu, tiyenera kufunitsitsa kuti Yehova azitiona kuti ndife anthu abwino. Tikutero chifukwa chakuti Yehova ndi wapamwamba kwambiri m’chilengedwe chonse ndipo iye ndi “kasupe wa moyo.”—Sal. 36:9.

2 Ponena za ‘mtundu wa anthu amene tiyenera kukhala’ kuti tisangalatse Yehova, mtumwi Petulo amatilimbikitsa kuti tikhale ‘anthu akhalidwe loyera ndipo tizichita ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’ (Werengani 2 Petulo 3:11.) Kuti Mulungu azisangalala nafe, tiyenera kukhala anthu “akhalidwe loyera.” Zimenezi zikutanthauza kuti kulambira kwathu, zimene timachita ndiponso zimene timaganiza ziyenera kukhala zoyera. Tiyeneranso kuchita ‘ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu’ chifukwa chakuti timamuopa komanso ndife okhulupirika kwa iye. Choncho kuti tisangalatse Mulungu tiyenera kukhala ndi khalidwe loyera komanso mtima wabwino. Popeza kuti Yehova ‘amasanthula mitima,’ amadziwa ngati tili ndi khalidwe loyera ndiponso ngati ndife odzipereka kwa iye yekha kapena ayi.—1 Mbiri 29:17.

3. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati okhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu?

3 Satana Mdyerekezi safuna kuti tizisangalatsa Mulungu. Ndipotu amachita zonse zimene angathe kuti asokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Satana amagwiritsa ntchito mabodza ndiponso chinyengo pofuna kutikopa kuti tisiye kulambira Mulungu wathu. (Yoh. 8:44; 2 Akor. 11:13-15) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Satana amapusitsa bwanji anthu? Nanga ndingateteze bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova?’

 KODI SATANA AMAPUSITSA BWANJI ANTHU?

4. Pofuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu, kodi Satana amalimbana ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?

4 Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo. Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” (Yak. 1:14, 15) Pofuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu, Satana amalimbana kwambiri ndi mtima wathu chifukwa ndi umene umalakalaka zinthu.

5, 6. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito chiyani pofuna kusokoneza mtima wathu? (b) Kodi iye amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kuti tizilakalaka zinthu zoipa? (c) N’chifukwa chiyani tinganene kuti panopa Satana ali ndi luso pogwiritsa ntchito njirazi?

5 Kodi Satana amagwiritsa ntchito chiyani pofuna kusokoneza mtima wathu? Baibulo limanena kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Choncho Satana amagwiritsa ntchito ‘zinthu za m’dzikoli.’ (Werengani 1 Yohane 2:15, 16.) Kwa zaka zambiri, iye wakhala akuyesetsa kuti zinthu za m’dzikoli zikhale zokopa kwambiri kwa anthu. Popeza tili m’dziko lomweli, tiyenera kusamala kwambiri kuti asatipusitse.—Yoh. 17:15.

6 Satana amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pofuna kusokoneza mtima wathu kuti tizilakalaka zinthu zoipa. Mtumwi Yohane anatchula njira zitatu zimene iye amagwiritsa ntchito. Njira zake ndi: (1) “chilakolako cha thupi,” (2) “chilakolako cha maso” ndi (3) “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” Satana anagwiritsa ntchito njira zitatuzi poyesa Yesu m’chipululu. Popeza wakhala akuzigwiritsa ntchito kwa zaka zambiri, panopa amatha kusintha mwaluso njirazo kuti zigwirizane ndi zofuna za munthu aliyense. M’nkhani ino tikambirana mmene tingadzitetezere kwa Satana. Koma tisanatero, tiyeni tione mmene anagwiritsira ntchito njirazi popusitsa Hava komanso mmene analepherera kupusitsa Mwana wa Mulungu.

“CHILAKOLAKO CHA THUPI”

Hava anapusitsidwa ndi “chilakolako cha thupi” (Onani ndime 7)

7. Kodi Satana anagwiritsa ntchito bwanji “chilakolako cha thupi” popusitsa Hava?

7 Anthu amafunikira kudya kuti akhalebe moyo. Ndipotu Mlengi wathu analenga dzikoli kuti lizitipatsa chakudya chambiri. Koma Satana angayese kutikopa pogwiritsa ntchito chilakolako chofuna kudya n’cholinga choti tisiye kuchita zimene Mulungu amafuna. Tiyeni tione mmene anachitira zimenezi ndi Hava. (Werengani Genesis 3:1-6.) Iye anauza Hava kuti akhoza kudya chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Anamuuza kuti sadzafa koma pa tsiku limene adzadye chipatsocho, adzafanana ndi Mulungu. (Gen. 2:9) Ponena zimenezi, Satana ankatanthauza kuti Hava sayenera kumvera Mulungu kuti akhalebe ndi moyo. Limeneli linali bodza lamkunkhuniza. Hava atamva zimenezi, anayenera kusankha zochita. Iye akanasankha kukana  kumvera Satana kapena akanapitiriza kuganizira zimene Satana ananena kenako n’kuyamba kulakalaka chipatsocho. Ngakhale kuti panali zipatso zambiri zimene akanadya, anapitiriza kuganizira zimene Satana ananena ndipo kenako “anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya.” Satana anachititsa kuti Hava ayambe kulakalaka zimene Mlengi wake anamuletsa.

Yesu sanalole chilichonse kumusokoneza (Onani ndime 8)

8. (a) Kodi Satana anayesa bwanji Yesu pogwiritsa ntchito “chilakolako cha thupi”? (b) N’chifukwa chiyani Satana sanathe kupusitsa Yesu?

8 Satana anagwiritsa ntchito njira yomweyi poyesa Yesu m’chipululu. Yesu atasala kudya masiku 40, Satana anayesa kumukopa pogwiritsa ntchito chilakolako chofuna kudya. Satana anati: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.” (Luka 4:1-3) Nayenso Yesu anayenera kusankha zochita. Akanasankha kugwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira yozizwitsa kuti apeze chakudya kapena ayi. Koma Yesu anadziwa kuti sayenera kugwiritsa ntchito mphamvu zakezi kuti angopeza zofuna zake. Ngakhale kuti anali ndi njala, iye ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa chakudya. Yesu anayankha Satana kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’”—Mat. 4:4.

“CHILAKOLAKO CHA MASO”

9. (a) Kodi mawu akuti “chilakolako cha maso” akusonyeza chiyani? (b) Kodi Satana anagwiritsa ntchito bwanji chilakolako chimenechi poyesa Hava?

9 Yohane ananenanso za “chilakolako cha maso.” Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu angayambe kulakalaka chinthu atangochiona. Pa nthawi imene Satana ankayesa Hava, anagwiritsa ntchito chilakolako chimenechi. Iye anamuuza kuti: “Maso anu adzatseguka.” Pamene Hava ankayang’anitsitsa chipatso choletsedwachi, anayamba kuchilakalaka. Hava anaona kuti ‘zipatso za mtengowo ndi zokhumbirika.’

10. (a) Kodi Satana anagwiritsa ntchito bwanji “chilakolako cha maso” poyesa Yesu? (b) Kodi Yesu anamuyankha bwanji?

10 Kodi Satana anagwiritsa ntchito bwanji “chilakolako cha maso” poyesa Yesu? Iye “anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kochepa. Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse.’” (Luka 4:5, 6) Sikuti Yesu anaonadi maufumu onsewa pa kanthawi kochepako. Satana anamuonetsa ulemerero wa maufumuwo m’masomphenya mwina poganiza kuti akopeka nawo. Mopanda manyazi, Satana ananena kuti: “Ngati inuyo mungandiweramireko kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.” (Luka 4:7) Koma Yesu sanafune n’komwe kuti asangalatse Satana. Nthawi yomweyo anayankha kuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”—Luka 4:8.

 “KUDZIONETSERA NDI ZIMENE MUNTHU ALI NAZO PA MOYO WAKE”

11. Kodi Satana anapusitsa bwanji Hava?

11 Pofotokoza zinthu za m’dzikoli, Yohane anatchula “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” Pa nthawi imene Adamu ndi Hava anali m’munda wa Edeni, sakanatha ‘kudzionetsera ndi zimene anali nazo pa moyo wawo’ chifukwa anali okhaokha. Komabe anasonyeza kuti anali onyada. Pamene Satana ankayesa Hava anam’chititsa kuganiza kuti Mulungu akumumana zinthu zabwino kwambiri. Mdyerekezi anauza Hava kuti pa tsiku limene adzadye chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” ‘adzafanana ndi Mulungu ndipo adzadziwa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 2:17; 3:5) Ponena mawu amenewa, Satana ankatanthauza kuti Hava angathe kumachita zinthu payekha osadalira Yehova. Zikuoneka kuti kunyada ndi chinthu chimodzi chimene chinam’chititsa kuti akhulupirire bodza limeneli. Iye anadya chipatso choletsedwacho pokhulupirira kuti sadzafa. Koma apa anapusitsidwadi.

12. Kodi Satana anayesanso Yesu m’njira iti, ndipo Yesu anayankha bwanji?

12 Mosiyana ndi Hava, Yesu anasonyeza kudzichepetsa kwambiri. Satana anauza Yesu kuti ayese Mulungu pochita zinthu zodzionetsera. Koma Yesu sanayerekeze n’komwe kuchita zimenezi. Ngati akanachita zimenezi, akanasonyeza mtima wonyada. M’malomwake, anayankha mosapita m’mbali kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”—Werengani Luka 4:9-12.

KODI TINGATETEZE BWANJI UBWENZI WATHU NDI YEHOVA?

13, 14. Kodi Satana amapusitsa bwanji anthu masiku ano?

13 Masiku ano, Satana amayesanso anthu pogwiritsa ntchito njira zomwezi. Mdyerekezi amagwiritsa ntchito dziko lakeli pokopa anthu ndi “chilakolako cha maso” kuti azichita chiwerewere komanso kuti azidya ndi kumwa mopitirira muyeso. Iye amagwiritsanso ntchito zithunzi zolaula, makamaka pa Intaneti, kuti anthu ena akopeke ndi “chilakolako cha maso.” Anthu onyada kapena ofuna ‘kudzionetsera ndi zimene ali nazo pa moyo wawo’ angakopeke mosavuta ndi kufunafuna chuma, udindo kapena kutchuka.

Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingakuthandizeni pa zinthu izi? (Onani ndime 13 ndi 14)

14 ‘Zinthu za m’dzikoli’ zili ngati nyambo zimene msodzi amagwiritsa ntchito. Zimakhala zokopa koma chilichonse chimakhala ndi mbedza yake. Pofuna kuti anthu achite zosemphana  ndi malamulo a Mulungu, Satana amagwiritsa ntchito zinthu zimene anthu amazilakalaka mwachibadwa. Koma amagwiritsa ntchito zinthuzo m’njira yoti zisokoneze mtima wathu kuti tiyambe kulakalaka zoipa. Iye amafuna kutichititsa kukhulupirira kuti kupeza zimene timalakalaka n’kofunika kwambiri kuposa kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi tilola kuti atipusitse?

15. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pokana mayesero a Satana?

15 Satana anapusitsa Hava koma analephera kupusitsa Yesu. Nthawi zonse, Yesu ankayankha kuti: “Malemba amati.” Ifenso tikamaphunzira Baibulo mwakhama tidzadziwa bwino Malemba ndipo tidzakumbukira mavesi amene angatithandize kusankha zinthu mwanzeru pa nthawi imene tikuyesedwa. (Sal. 1:1, 2) Kukumbukiranso zitsanzo za m’Malemba za anthu amene anali okhulupirika kwa Mulungu kungatithandize kuti tiwatsanzire. (Aroma 15:4) Kuti tidziteteze kwa Satana, tiyenera kuopa Yehova, kukonda zimene amakonda ndiponso kudana ndi zimene amadana nazo.—Sal. 97:10.

16, 17. Kodi “luntha la kuganiza” lingatithandize bwanji?

16 Mtumwi Paulo ananena kuti tiyenera kugwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” n’cholinga choti maganizo athu aziumbidwa ndi Yehova osati dzikoli. (Aroma 12:1, 2) Pofotokoza kufunika koti tizilamulira maganizo athu, Paulo ananena kuti: “Tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu.” (2 Akor. 10:5) Nthawi zambiri, anthufe timachita zimene timaganiza, choncho tiyenera ‘kupitiriza kuganizira’ zinthu zabwino.—Afil. 4:8.

17 N’zosatheka kukhala oyera ngati timaganizira kapena kulakalaka zinthu zoipa. Tiyenera kukonda Yehova ndi ‘mtima woyera.’ (1 Tim. 1:5) Koma mtima wathu ndi wonyenga ndipo mwina sitingazindikire kuti tasokonezedwa ndi ‘zinthu za m’dzikoli.’ (Yer. 17:9) Choncho ndi bwino ‘kupitiriza kudziyesa kuti tione ngati tikadali olimba m’chikhulupiriro. Tipitirize kudziyesa n’cholinga choti tidziwe kuti ndife anthu otani.’ Tingachite zimenezi podzifufuza kuti tione ngati timatsatiradi zimene timaphunzira m’Baibulo.—2 Akor. 13:5.

18, 19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala mtundu wa anthu amene Yehova amafuna?

18 Chinthu china chimene chingatithandize kupewa ‘zinthu za m’dzikoli’ ndi kukumbukira mawu a Yohane akuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Dziko la Satana limaoneka ngati lili bwinobwino ndipo silidzatha. Komabe tsiku lina lidzatha ndithu. Palibe chinthu chilichonse m’dziko la Satanali chimene sichidzatha. Kukumbukira zimenezi kungatithandize kuti tisapusitsidwe ndi Mdyerekezi.

19 Mtumwi Petulo anatilimbikitsa kuti tikhale anthu amene amasangalatsa Mulungu. Ananenanso kuti tizichita zimenezi “poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova, pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka, ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka.” (2 Pet. 3:12) Posachedwapa, tsikulo lifika ndipo Yehova awononga chinthu chilichonse m’dziko la Satanali. Mpaka nthawiyo, Satana apitiriza kugwiritsa ntchito ‘zinthu za m’dzikoli’ kuti atiyese ngati mmene anachitira ndi Hava ndiponso Yesu. Sitiyenera kumangofuna kupeza zimene timalakalaka ngati mmene anachitira Hava. Kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi kunena kuti Satana ndi mulungu wathu. M’malomwake, tiyenera kutsanzira Yesu n’kukana mayesero ngakhale atakhala okopa kwambiri. Tiyeni tiziyesetsa kukhala mtundu wa anthu amene Yehova amafuna.