Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi “ana a Mulungu woona” otchulidwa pa Genesis 6:2, 4 amene analipo Chigumula chisanachitike anali ndani?

Pali umboni wosonyeza kuti anali angelo. Kodi umboni wake ndi uti?

Lemba la Genesis 6:2 limanena kuti: “Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.”

M’Malemba Achiheberi, mawu akuti “ana a Mulungu woona” ndiponso “ana a Mulungu” amapezeka pa Genesis 6:2, 4; Yobu 1:6; 2:1; 38:7 ndi pa Salimo 89:6. Kodi malemba amenewa amasonyeza kuti ‘ana a Mulunguwo’ ndi ndani?

Mawu oti “ana a Mulungu woona” amene ali pa Yobu 1:6 amanena za angelo amene anasonkhana pamaso pa Yehova. Pagululo panalinso Satana ndipo iye ankachokera ‘kozungulirazungulira m’dziko lapansi.’ (Yobu 1:7; 2:1, 2) Pa Yobu 38:4-7, timawerenganso kuti “ana onse a Mulungu anayamba kufula ndi chisangalalo” pamene Mulungu ‘anaika mwala wapakona’ wa dziko lapansi. Ana amenewa ayenera kuti ndi angelo chifukwa pa nthawiyo anthu anali asanalengedwe. Komanso zikuonekeratu kuti “ana a Mulungu” otchulidwa pa Salimo 89:6 ndi angelo amene amakhala ndi Mulungu kumwamba osati anthu.

Ndiyeno, kodi “ana a Mulungu woona” otchulidwa pa Genesis 6:2, 4 anali ndani? Malinga ndi mfundo za m’Baibulo zimene takambiranazi, m’pomveka kunena kuti ana amenewa anali angelo a Mulungu amene anabwera padziko lapansi.

Anthu ena zimawavuta kukhulupirira kuti angelo angakhale ndi chilakolako chofuna kugonana. Pajatu pa Mateyu 22:30, Yesu anasonyeza kuti angelo kumwamba sakwatirana kapena kugonana. Koma kumbukirani kuti nthawi zina, angelo ankavala matupi a anthu n’kumadya ndiponso kumwa limodzi ndi anthu. (Gen. 18:1-8; 19:1-3) Choncho, n’zomveka kunena kuti ngati atavala matupi a anthu akhozanso kugonana ndi akazi.

Pali umboni wina wa m’Baibulo wosonyeza kuti angelo anachitadi zimenezi. Lemba la Yuda 6 ndi 7 limanena kuti amuna a ku Sodomu ankagonana m’njira imene si yachibadwa. Ndiyeno limayerekezera zimenezi ndi “angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala.” Lembali likusonyeza kuti zochita za amuna a ku Sodomu zikufanana ndi za angelowa chifukwa chakuti onse ‘anachita dama loipitsitsa ndiponso kugonana m’njira imene si yachibadwa.’ Komanso lemba la 1 Petulo 3:19, 20 limasonyeza kuti angelo osamverawa analipo “m’masiku a Nowa.” (2 Pet. 2:4, 5) Choncho zimene angelo osamvera anachita m’masiku a Nowa zikufanana ndi tchimo la anthu a ku Sodomu ndi Gomora.

Chifukwa cha zimenezi, m’pomveka kunena kuti “ana a Mulungu woona” otchulidwa pa Genesis 6:2, 4 anali angelo amene anavala matupi a anthu n’kumachita dama ndi akazi.

 Kodi mawu a pa 1 Petulo 3:19 akuti Yesu “anapita kukalalikira kwa mizimu imene inali m’ndende” amatanthauza chiyani?

Mtumwi Petulo ananena kuti mizimu imeneyi ndi imene “inali yosamvera pa nthawi imene Mulungu anali kuleza mtima m’masiku a Nowa.” (1 Pet. 3:20) Apa zikuonekeratu kuti Petulo ankanena za angelo amene anasankha kugwirizana ndi Satana yemwe ndi mdani wa Mulungu. Nayenso Yuda ananena za “angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala.” Ananenanso kuti “Mulungu anawasunga kosatha m’maunyolo, mu mdima wandiweyani kuti adzaweruzidwe pa tsiku lalikulu.”Yuda 6.

M’masiku a Nowa, kodi angelo ena anachita zinthu ziti zosonyeza kusamvera Mulungu? Chigumula chisanachitike, angelo oipawa anavala matupi a anthu ndipo izi zinali zosemphana ndi cholinga cha Mulungu. (Gen. 6:2, 4) Komanso iwo ankagonana ndi akazi. Izinso zinali zosemphana ndi mmene Mulungu anawalengera. (Gen. 5:2) Pa nthawi yake yoyenerera, Mulungu adzawononga angelo oipawa. Mogwirizana ndi zimene Yuda ananena, panopa iwo ali “mu mdima wandiweyani,” ndipo zili ngati ali m’ndende.

Kodi ndi liti pamene Yesu analalikira “mizimu imene inali m’ndende,” ndipo anachita bwanji zimenezi? Petulo analemba kuti Yesu anachita izi ‘ataukitsidwa monga mzimu.’ (1 Pet. 3:18, 19) Onaninso kuti Petulo ananena kuti Yesu “anapita kukalalikira.” Mawu amenewa akusonyeza kuti iye analalikira mizimuyo Petulo asanalembe kalata yake yoyambayi. Choncho zikuoneka kuti nthawi inayake ataukitsidwa, Yesu analengeza kwa mizimu yoipayi za chilango chimene ikuyenera kulandira. Iye sanalalikire uthenga wopatsa chiyembekezo koma wachiweruzo. (Yona 1:1, 2) Yesu anali woyenerera kulengeza uthenga umenewu chifukwa anali atakhala wokhulupirika mpaka imfa, kenako n’kuukitsidwa. Izi zinasonyeza kuti Mdyerekezi analibe mphamvu iliyonse pa iye.—Yoh. 14:30; 16:8-11.

Angelo amenewa adakali mu mdima wandiweyani. Koma posachedwa, Yesu adzamanga Satana ndi angelo akewa n’kuwaponya kuphompho. (Luka 8:30, 31; Chiv. 20:1-3) Pamapeto pake, iwo adzawonongedwa.—Chiv. 20:7-10.